Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | MABODZA OMWE AMALEPHERETSA ANTHU KUKONDA MULUNGU

Bodza Lachiwiri: Mulungu ndi Wosamvetsetseka

Bodza Lachiwiri: Mulungu ndi Wosamvetsetseka

ZIMENE ANTHU AMAKHULUPIRIRA

Zipembedzo zachikhristu “zikuluzikulu zitatu, zomwe ndi Chikatolika, Eastern Orthodoxy ndi Chipulotesitanti, zimakhulupirira kuti pali milungu itatu mwa Mulungu m’modzi. Pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu Woyera. Milungu itatu imeneyi imapanga Mulungu mmodzi.”—The New Encyclopædia Britannica.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Yesu, Mwana wa Mulungu, sananenepo kuti ndi wofanana ndi Atate wake. Koma iye ananena kuti: “Ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu. Ngati munali kundikonda, mukanakondwera kuti ndikupita kwa Atate wanga, chifukwa Atate ndi wamkulu kuposa ine.” (Yohane 14:28) Anauzanso mmodzi wa ophunzira ake kuti: “Ine ndikukwera kwa Atate wanga ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.”—Yohane 20:17.

Mzimu woyera si Mulungu. Akhristu oyambirira “anadzazidwa ndi mzimu woyera,” ndipo Yehova anati: “Ndidzatsanulira mbali ya mzimu wanga pa anthu osiyanasiyana.” (Machitidwe 2:1-4, 17) Choncho mzimu woyera si Mulungu koma ndi mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu.

CHIFUKWA CHAKE KUDZIWA ZIMENEZI N’KOFUNIKA

Akatswiri achikatolika, omwe ndi Karl Rahner ndi Herbert Vorgrimler, ananena kuti: “Munthu sangamvetse chikhulupiriro cha Utatu pokhapokha chitaululidwa kwa iye, ndipo ngakhale chitaululidwa kwa iye sangachimvetsebe bwinobwino.” Kodi n’zotheka kukonda munthu amene simum’dziwa ndipo simungathe kumumvetsetsa? Chiphunzitso cha Utatu chimalepheretsa anthu kudziwa komanso kukonda Mulungu.

Marco, amene tamutchula m’nkhani yoyamba ija, ankaona kuti chiphunzitso cha Utatu chinkamulepheretsa kudziwa bwino Mulungu. Iye anati: “Ndinkaona kuti Mulungu safuna kuti ndimudziwe kuti ndi wotani, ndipo zimenezi zinapangitsa kuti ndizimuona kuti sakhudzidwa ndi mavuto athu, ndi wosamvetsetseka komanso sindingakhale naye pa ubwenzi.” Komabe iye sadzibisa ndipo amafuna kuti timudziwe. Yesu anati: “Ife timalambira chimene tikuchidziwa.”—Yohane 4:22.

Marco ananena kuti: “Nditaphunzira kuti Mulungu si Utatu zinandithandiza kuti ndikhale naye pa ubwenzi.” Ngati titamaona Yehova ngati weniweni, zingatithandize kuti tizimukonda. Baibulo limanena kuti: “Munthu wopanda chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi.”—1 Yohane 4:8.