Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi ndani amapita kumwamba ndipo n’chifukwa chiyani?

Anthu ambiri amanena kuti adzapita kumwamba akadzamwalira. Yesu ananena kuti atumwi ake okhulupirika adzapita kumwamba. Asanamwalire, anawalonjeza kuti akupita kumwamba kwa Atate ake kukawakonzera malo.—Werengani Yohane 14:2.

N’chifukwa chiyani anthu ena amaukitsidwa kuti apite kumwamba? Kodi amapita kukatani? Yesu anauza atumwi ake kuti adzakhala mafumu ndipo adzalamulira dziko lapansi.—Werengani Luka 22:28-30; Chivumbulutso 5:10.

Kodi anthu onse abwino amapita kumwamba?

M’mayiko ambiri, anthu ochepa okha ndi amene amakhala olamulira. Popeza Yesu amaukitsa anthu kuti akakhale mafumu kumwamba, tikuyembekezera kuti anthu amene adzalamulira dziko lapansi ayenera kukhalanso ochepa. (Luka 12:32) Baibulo limatchula nambala yeniyeni ya anthu amene adzalamulire ndi Yesu kumwamba.—Werengani Chivumbulutso 14:1.

Yesu anakonzera otsatira ake ena malo kumwamba. Kodi mukudziwa zimene azidzachita kumwambako?

Komatu si anthu okhawa amene adzalandire mphoto ya moyo wosatha. Anthu amene adzakhale nzika za Ufumu wa Mulungu adzasangalala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. (Yohane 3:16) Anthu ena adzapulumuka n’kulowa m’Paradaiso Mulungu akamadzawononga anthu oipa, pamene ena adzachita kuukitsidwa kuchokera kumanda.—Werengani Salimo 37:29; Yohane 5:28, 29.