Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Kuonera Zolaula Kuli Ndi Mavuto Otani?

Kodi Kuonera Zolaula Kuli Ndi Mavuto Otani?

Masiku ano zolaula zili paliponse. * Zimapezeka m’mafilimu, m’nyimbo, m’magazini, m’masewera a pakompyuta, pa TV, m’mafoni komanso pa Intaneti. Masiku ano anthu ambiri akumaonera zolaula kuposa kale ndipo akuona kuti palibe vuto lililonse kuchita zimenezi.—Onani bokosi lakuti,  “Anthu Ambiri Akumaonera Zolaula.”

Komanso zolaula zimene anthu ankaonera m’mbuyomu zikusiyana ndi zimene anthu akumaonera masiku ano. Pulofesa wina, dzina lake Gail Dines, analemba kuti: “Masiku ano anthu akumaonera zithunzi zimene poyamba anthu ankaziona kuti n’zoipa kwambiri kapena n’zosayenera.”

Kodi inuyo mumaganiza bwanji pa nkhani imeneyi? Kodi mumaona kuti kuonera zolaula kuli ndi vuto lililonse? Yesu ananena kuti: “Mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse wovunda umabala zipatso zopanda pake.” (Mateyu 7:17) Kodi munthu amene amaonera zolaula amakumana ndi mavuto otani? Kuti tipeze yankho la funso limeneli, choyamba tiyeni tiyankhe kaye mafunso ena okhudza zolaula.

 Kodi zolaula zimakhudza bwanji woonerayo?

ZIMENE AKATSWIRI ENA AMANENA: Munthu akayamba kuonera zolaula samafuna kusiya. Anthu ena amene anachita kafukufuku anapeza kuti munthu amene amaonera zolaula amakhala ndi chibaba ngati munthu wosuta fodya.

Brian, * yemwe anazolowera kuonera zolaula pa Intaneti, ananena kuti: “Ndinkalephera kusiya. Ndinkaona kuti palibe chilichonse chomwe ndingachite kuti ndisiye kuonera zolaula. Ndinkati ndikapanda kuonera zolaula, ndinkanjenjemera ndipo mutu unkandipweteka. Ndinkayesetsa kuti ndisiye koma ndinkalephera.”

Nthawi zambiri anthu amene amaonera zolaula amachita zimenezi mobisa komanso amakonda kunama. N’chifukwa chake ambiri amasowa ocheza nawo, amachita manyazi, amakhala ndi nkhawa, amavutika maganizo komanso amakhala okwiya. Nthawi zina amafunanso kudzipha. Serge, yemwe ankapanga dawunilodi zolaula pa foni yake tsiku lililonse, ananena kuti: “Nthawi zambiri ndinkangokhala wolusa komanso sindinkaganizira anthu ena. Ndinkadziona kuti ndine munthu wopanda pake, ndinkadziimba mlandu komanso ndinkaona kuti sindingathe kusiya. Ndinkachita mantha komanso manyazi kuti ndiuze anthu ena.”

Kuonera zolaula n’koopsa kwambiri ngakhale munthu atangoonera pang’ono kapena atangoziona mwangozi. Mzimayi wina amene anatsogolera pa kafukufuku wokhudza zolaula, dzina lake Judith Reisman, ananena kuti: “Munthu akamaonera zolaula, ubongo wake umasokonezeka komanso umasunga zimene waonazo moti zimavuta kuti aziiwale.” Mtsikana wina wazaka 19, yemwe ankakonda kuonera zolaula pa Intaneti, dzina lake Susan, ananena kuti: “Sindimaiwala zithunzi zimene ndinkaonera. Nthawi zina zimangopezeka kuti zangobwera m’maganizo mwanga. Ndimaona kuti sindidzakwanitsa kuchotseratu zithunzi zimenezi m’maganizo mwanga.”

MFUNDO YOFUNIKA KUIKUMBUKIRA: Anthu amene amaonera zolaula amakhala ngati kapolo komanso amavutika kwambiri.—2 Petulo 2:19.

Kodi zolaula zimakhudza bwanji banja la munthuyo?

ZIMENE AKATSWIRI ENA AMANENA: “Banja likhoza kutha ngati mwamuna kapena mkazi amaonera zolaula.”—Linatero buku lakuti, The Porn Trap, lomwe Wendy komanso Larry Maltz analemba.

Kuonera zolaula kumasokoneza banja chifukwa

 • kumapangitsa kuti mwamuna ndi mkazi asamakhulupirirane komanso kuti asamakondane.—Miyambo 2:12-17.

 • kumapangitsa kuti woonera zolaulayo azidzikonda komanso kuti asamasangalale ndi mwamuna kapena mkazi wake.—Aefeso 5:28, 29.

 • kumalimbikitsa zilakolako zoipa zogonana.—2 Petulo 2:14.

 • woonerayo amakakamiza mwamuna kapena mkazi wake kuti azigonana potengera zimene waonerazo.—Aefeso 5:3, 4.

 • kumapangitsa kuti munthu azingoganiza zogonana komanso akhoza kuchita chigololo.—Mateyu 5:28.

Baibulo limanena kuti anthu okwatirana asamachitirane “zachinyengo.” (Malaki 2:16) Munthu akachita  chigololo amakhala kuti wamuchitira mnzakeyo zachinyengo, zomwe zimasokoneza banja ndipo zingapangitse kuti okwatiranawo apatukane kapena banjalo lithe. Kupatukana komanso kutha kwa banja kumasokonezanso ana a m’banjamo.

Komanso zolaula pazokha zimasokoneza ana. Mwachitsanzo, Brian, yemwe tamutchula kale uja, ananena kuti: “Tsiku lina ndikusewera chibisalirano ndinaona magazini a bambo anga a zithunzi zolaula. Pa nthawi imeneyi n’kuti ndili ndi zaka 10. Ndinayamba kumaziona mobisa koma sindinkamvetsa kuti n’chifukwa chiyani ndinkakopeka nazo. Kuyambira nthawi imeneyo ndinangozolowera kuonera zolaula.” Kafukufuku amasonyeza kuti achinyamata akamaonera zolaula amayamba kugonana adakali aang’ono, amagonana ndi anthu osiyanasiyana komanso amasokonezeka maganizo.

MFUNDO YOFUNIKA KUIKUMBUKIRA: Kuonera zolaula kumasokoneza banja komanso ana ndipo kumabweretsa mavuto aakulu.—Miyambo 6:27.

 Zimene Baibulo limanena pa nkhani ya zolaula

BAIBULO LIMATI: “Chititsani ziwalo za thupi lanu . . . kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje, kumene ndiko kulambira mafano.”—Akolose 3:5.

Kunena mwachidule, Yehova * Mulungu amadana ndi zolaula. Sikuti Mulungu amaletsa zolaula chifukwa chodana ndi zoti anthu azigonana. Tikutero chifukwa Mulungu anatilenga kuti tizikhala ndi chilakolako chogonana n’cholinga choti anthu okwatirana azisangalala, azikondana komanso kuti azibereka ana.—Yakobo 1:17.

Nanga n’chifukwa chiyani Mulungu amadana kwambiri ndi zolaula? Taonani zifukwa zina:

 • Amadziwa kuti kuonera zolaula kumabweretsa mavuto aakulu.—Aefeso 4:17-19.

 • Amatikonda choncho amafuna kutiteteza kuti tisakumane ndi mavuto.—Yesaya 48:17, 18.

 • Yehova amafuna kuti mabanja komanso ana asasokonekere.—Mateyu 19:4-6.

 • Amafuna kuti tikhale ndi makhalidwe abwino komanso kuti tizichita zinthu zolemekeza ufulu wa anthu ena.—1 Atesalonika 4:3-6.

 • Amafuna kuti tizilemekeza komanso kugwiritsa bwino ntchito mphatso yogonana.—Aheberi 13:4.

 • Yehova amadziwa kuti kuonera zolaula kumapangitsa anthu kukhala odzikonda komanso kukhala ndi maganizo olakwika omwe Satana amalimbikitsa pa nkhani ya kugonana.—Genesis 6:2; Yuda 6, 7.

MFUNDO YOFUNIKA KUIKUMBUKIRA: Munthu amene amaonera zolaula amawononga ubwenzi wake ndi Mulungu.—Aroma 1:24.

Komabe, Yehova amafunitsitsa kuthandiza anthu amene akufuna kusiya kuonera zolaula. Baibulo limati: “Yehova ndi wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha. Pakuti iye akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.” (Salimo 103:8, 14) Yehova akufuna kuti anthu onse odzichepetsa omwe akufuna kusiya kuonera zolaula ‘awachitire chifundo ndi kuwasonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene akufunika thandizo.’—Aheberi 4:16; onani bokosi lakuti,  “Zimene Munthu Angachite Kuti Asiye Kuonera Zolaula.”

Anthu ambiri akwanitsa kusiya kuonera zolaula chifukwa analola kuti Mulungu awathandize. Ponena za anthu ena amene anasiya makhalidwe awo oipa, Baibulo limati: “Koma mwasambitsidwa kukhala oyera, mwapatulidwa, mwayesedwa olungama m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, komanso ndi mzimu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:11) Anthu amenewa amanena mawu ofanana ndi amene mtumwi Paulo ananena kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13.

Susan, yemwe anakwanitsa kusiya kuonera zolaula, ananena kuti: “Ndi Yehova yekha amene angathandize munthu kusiyiratu kuonera zolaula. Ngati mutamupempha kuti akuthandizeni, n’kumatsatira malangizo ake mukhoza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi iye. Musakayikire kuti Yehova akhoza kukuthandizani.”

^ ndime 3 Mawu akuti “zolaula” amatanthauza zinthu zokhudza kugonana zimene zimapangidwa n’cholinga choti munthu amene akuonera, kumvetsera kapena kuwerengayo akhale ndi maganizo ofuna kugonana. Zolaula zimatha kupezekanso m’mabuku, m’magazini, m’nyimbo komanso m’zithunzi.

^ ndime 8 Mayina asinthidwa.

^ ndime 25 Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.