Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzikhulupirira Mulungu

Muzikhulupirira Mulungu

TAYEREKEZERANI kuti mnzanu amene mumamukhulupirira kwambiri wachita zinazake zomwe zikukuvutani kumvetsa. Anthu ena akunena kuti zimene wachita mnzanuyo zikusonyeza kuti ndi wankhanza. Kodi mungangovomereza zimene anthuwo akunena kapena mungadikire kaye kuti mnzanuyo afotokoze yekha zifukwa zimene anachitira zimenezo? Ngati mnzanuyo palibe, kodi mungadikirebe kuti mudzamve maganizo ake m’malo mongovomereza kuti ndi wankhanza?

Musanayankhe funso limeneli mungafunike kudziwa zambiri. Mwachitsanzo, mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimadziwa zotani za munthu ameneyu ndipo n’chiyani chimene chimandichititsa kuti ndizimukhulupirira?’ Kodi sitingagwiritsenso ntchito mafunso amenewa pofuna kudziwa ngati Mulungu ali wankhanza?

Mwina simungamvetse zinthu zina zimene Mulungu wachita, kapena simungamvetse chifukwa chimene walolera kuti zinthu zina zichitike. Pali anthu ambiri amene amakhulupirira kuti Mulungu ndi wankhanza ndipo angakulimbikitseni kuti inunso muzikhulupirira zomwezo. Mungafunike kufufuza kaye musanayambe kuganiza kuti Mulungu ndi wankhanza? Mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene Mulungu wandichitira?’

Ngati mwakhala mukukumana ndi mavuto pamoyo wanu, mwina mungaone kuti Mulungu ndi wankhanza. Koma taganizirani kaye mfundo iyi: Mulungu si amene amachititsa mavuto amene timakumana nawo, m’malo mwake Iye amatichitira zabwino. Monga mmene taonera kale, Satana ndi amene ‘akulamulira dzikoli,’ osati Yehova. (Yohane 12:31) Chotero Satana ndi amene amachititsa mavuto komanso zinthu zopanda chilungamo padzikoli. Kuwonjezera apo, anthufe timavutika chifukwa chakuti ndife opanda ungwiro komanso chifukwa cha zinthu zosayembekezereka.

Mulungu si amene amachititsa mavuto amene timakumana nawo

Komano, kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene Mulungu watipatsa? Taganizirani zimene Baibulo limanena kuti Mulungu ndi “Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi” komanso kuti anapanga matupi athu omwe ‘anapangidwa modabwitsa.’ Limanenanso kuti Yehova ndi “Mulungu amene amasunga mpweya wanu . . . m’dzanja lake.” (Salimo 124:8; 139:14; Danieli 5:23) Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani?

Amatanthauza kuti Mlengi ndi amene anatipatsa moyo komanso mpweya umene timapuma. (Machitidwe 17:28) Komanso amatanthauza kuti zinthu zonse zabwino monga zinthu zachilengedwe zimene timasangalala nazo, anzathu amene timakondana nawo, zakudya zokoma, zonunkhira komanso nyimbo zabwino, zimachokera kwa Mulungu. (Yakobo 1:17) Madalitso onsewa amatipangitsa kuti tiziona Mulungu monga bwenzi lathu komanso kuti tizimukhulupirira.

Mwina inuyo mumaona kuti n’zovuta kukhulupirira Mulungu chifukwa chakuti simumamudziwa bwinobwino, ndipo zimenezi n’zomveka. Mu nkhanizi takambirana zifukwa zochepa zimene zimachititsa anthu ena kuganiza kuti Mulungu ndi wankhanza. Koma mungachite bwino mutayesetsa kuti mudziwe zambiri zokhudza Mulungu. * Ngati mutachita zimenezi, mudzazindikira kuti Mulungu si wankhanza chifukwa: “Mulungu ndiye chikondi.”—1 Yohane 4:8.

^ ndime 8 Mwachitsanzo, mukhoza kudziwa chifukwa chimene Mulungu walolera kuti anthu azivutika. Nkhaniyi imapezeka m’mutu 11 wa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.