Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 YANDIKIRANI MULUNGU

“Iye ndi Mulungu wa Anthu Amoyo”

“Iye ndi Mulungu wa Anthu Amoyo”

Kodi imfa ndi yamphamvu kuposa Mulungu? Ayi. Palibe “mdani” aliyense, ngakhale imfa, amene ndi wamphamvu kuposa “Mulungu Wamphamvuyonse.” (1 Akorinto 15:26; Ekisodo 6:3) Mulungu ali ndi mphamvu zothetsa imfa, ndipo walonjeza kudzaukitsa akufa m’dziko latsopano. * Kodi tingatsimikize bwanji kuti Mulungu adzachitadi zimenezi? Mawu amene Mwana wa Mulungu, Yesu, ananena amatitsimikizira kuti Mulungu adzachitadi zimenezi.—Werengani Mateyu 22:31, 32.

Polankhula ndi Asaduki, omwe sankakhulupirira zoti akufa adzauka, Yesu anati: “Kunena za kuuka kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’? Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa.” Apa Yesu ankanena za zimene Mulungu anauza Mose cha m’ma 1514 B.C.E., pachitsamba choyaka moto. (Ekisodo 3:1-6) Yesu ankaona kuti mawu amene Yehova anauza Mose akuti, “Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo,” akusonyeza kuti lonjezo lakuti akufa adzauka lidzakwaniritsidwadi. N’chifukwa chiyani tikutero?

Taganizirani mmene zinthu zinalili pa nthawi imene Yehova ankalankhula mawu amenewa. Pa nthawiyi, n’kuti Abulahamu, Isaki ndi Yakobo atamwalira kalekale. Panali patatha zaka 329 kuchokera pamene Abulahamu anamwalira, zaka 224, kuchokera pamene Isaki anamwalira komanso zaka 197, kuchokera pamene Yakobo anamwalira. Koma Yehova sananene kuti “Ine ndinali” Mulungu wawo. M’malomwake iye anati, “Ine ndine” Mulungu wawo. Ponena za makolo a Aisiraeli amenewo, Yehova ananena ngati kuti iwo adakali ndi moyo. Kodi n’chifukwa chiyani ananena choncho?

Yesu anati: “[Yehova] ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa.” Taganizirani zimene tikuphunzira pa mawu amenewa. Akanakhala kuti anthu akufa sadzaukitsidwa, ndiye kuti tikanati Yehova sadzaukitsanso Abulahamu, Isaki ndi Yakobo ndipo Yehova akanakhala Mulungu wa anthu akufa. Zimenezi zikanasonyeza kuti imfa ndi yamphamvu kuposa Yehova moti iye walephera kulanditsa anthu ake okhulupirika ku imfa.

Ndiye kodi zimenezi zikutiuza chiyani za Abulahamu, Isaki, Yakobo ndi atumiki onse okhulupirika a Yehova amene anamwalira? Yesu ananena kuti: “Kwa iye onsewa ndi amoyo.” (Luka 20:38) Popeza Yehova amafunitsitsa kudzaukitsa atumiki ake, iye akamalankhula za atumiki akewa, amanena ngati iwo ali moyo. (Aroma 4:16, 17) Yehova amakumbukira anthu amenewa ndipo pa nthawi yake adzawaukitsa kuti akhalenso ndi moyo.

Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa imfa

Kodi mungakonde kudzaonananso ndi achibale anu amene anamwalira? Ngati ndi choncho, kumbukirani kuti Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa imfa. Palibe chimene chingamulepheretse kukwaniritsa lonjezo lake lodzaukitsa akufa. Tikukupemphani kuti muphunzire zambiri zokhudza lonjezo limeneli komanso zokhudza Mulungu. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuyandikira Yehova, yemwe ndi “Mulungu wa anthu amoyo.”

Mavesi amene mungawerenge mu February

Mateyu chaputala 22-28mpaka Maliko chaputala 1-8

^ ndime 3 Kuti mudziwe zambiri zokhudza lonjezo la Mulungu loti adzaukitsa akufa m’dziko latsopano, onani mutu 7 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.