Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mose Anali Munthu Wachikondi

Mose Anali Munthu Wachikondi

KODI CHIKONDI N’CHIYANI?

Chikondi chimatanthauza mmene munthu amamvera mumtima mwake chifukwa cha munthu amene amasangalatsidwa naye kwambiri. Munthu wachikondi amasonyeza chikondi chakecho mwa zolankhula komanso zochita zake kwa anthu amene amawakondawo ngakhale pamene kuchita zimenezi kungachititse kuti adzimane zinthu zina.

KODI MOSE ANASONYEZA BWANJI KUTI ANALI WACHIKONDI?

Mose anasonyeza kuti ankakonda Mulungu. Kodi iye anasonyeza bwanji zimenezi? Kumbukirani mawu a palemba la 1 Yohane 5:3 omwe amati: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.” Mose ankatsatira mfundo imeneyi. Chilichonse chimene Mulungu wamuuza kuchita ankachita. Kaya wamuuza kuti achite chinthu chovuta, ngati kukalankhula ndi Farao wamphamvu, kapena wamuuza kuchita chinthu chosavuta, ngati kumenya madzi a m’Nyanja Yofiira ndi ndodo, Mose ankamvera. Baibulo limati: Iye “anachitadi momwemo.”—Ekisodo 40:16.

Mose ankakondanso Aisiraeli anzake. Aisiraeli ankadziwa kuti Yehova ankagwiritsa ntchito Mose powatsogolera, choncho iwo ankapita kwa Mose akakhala ndi mavuto. Baibulo limati: “Anthu anali kubwera ndi kuimirira pamaso pa Mose kuyambira m’mawa mpaka madzulo.” (Ekisodo 18:13-16) Mose ayenera kuti ankatopa kwambiri kumvetsera madandaulo a anthuwa. Komabe iye ankawathandiza mosanyinyirika chifukwa ankawakonda.

Kuwonjezera pa kumvetsera madandaulo awo, Mose ankapemphereranso anthuwa. Iye ankapempherera ngakhale anthu amene amulakwira. Mwachitsanzo, mchemwali wake, Miriamu atayamba kutsutsa Mose, Yehova anakantha Miriamuyo ndi khate. M’malo mosangalala chifukwa cha chilango chimene Miriamu analandira, iye anam’pempherera kwa Yehova kuti: “Chonde Mulungu wanga! M’chiritseni chonde.” (Numeri 12:13) Chikondi n’chimene chinachititsa Mose kupempha Mulungu kuti achiritse Miriamu.

ZIMENE TIKUPHUNZIRA KWA MOSE:

Mofanana ndi Mose, nafenso tiyenera kukonda Mulungu ndi mtima wonse. Chikondi choterechi chingatichititse kuti tizimvera malamulo ake “mochokera pansi pa mtima.” (Aroma 6:17) Tikamamvera Yehova mochokera pansi pa mtima, timasangalatsa mtima wake ndiponso timapindula kwambiri. (Miyambo 27:11) Komanso kutumikira Mulungu chifukwa chomukonda kuchokera pansi pa mtima, kudzatithandiza kuti tizichita zinthu zabwino komanso kuti tizichita zinthuzo mosangalala.—Salimo 100:2.

Tingatsanzirenso Mose pokhala ndi chikondi chololera kuvutikira ena. Anzathu kapena achibale athu akamatiuza mavuto awo, chikondi chingatipangitse (1) kumvetsera ndi mtima wonse zimene akutiuza, (2) kuwamvera chisoni, kapena kuganizira mmene tikanamvera mavutowo akanachitikira ifeyo, komanso (3) kuwasonyeza kuti tikuwadera nkhawa.

Mofanana ndi Mose, ifenso tizipempherera anthu ena. Nthawi zina munthu akatiuza mavuto ake, tingaone kuti palibe chimene tingachite kuti timuthandize. Koma zikatere ndi bwino kungomuuza kuti: “Ineso mavuto anuwa andithetsa nzeru. Chimene ndingachite ndi kukupemphererani basi.” Musaiwale kuti, “pembedzero la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.” (Yakobo 5:16) Pemphero lathu lingachititse kuti Yehova achite zinazake pothandiza munthuyo zimene mwina sakanachita tikanapanda kumupempherera. Ndipotu ngati sitikudziwa mmene tingathandizire munthu amene watiuza mavuto ake, palibe chinthu chofunika chimene tingachite kuposa kumupempherera. *

Kodi simukuvomereza kuti palidi zambiri zimene tingaphunzire kuchokera kwa Mose? Ngakhale kuti iye anali munthu ngati ife tomwe, anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya chikhulupiriro, kudzichepetsa komanso chikondi. Tikamatsatira kwambiri chitsanzo chake, sizithandiza ife tokha koma zimathandizanso ena.—Aroma 15:4.

^ ndime 8 Ngati tikufuna kuti Mulungu azimva mapemphero athu, tiyenera kuyesetsa kutsatira malamulo ake. Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 17 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.