Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mose Anali Munthu Wachikhulupiriro Cholimba

Mose Anali Munthu Wachikhulupiriro Cholimba

KODI CHIKHULUPIRIRO N’CHIYANI?

M’Baibulo mawu akuti “chikhulupiriro” amatanthauza kukhulupirira ndi mtima wonse zinazake malinga ndi umboni womwe ulipo. Munthu amene amakhulupirira Mulungu amatsimikiza ndi mtima wonse kuti iye adzakwaniritsa malonjezo ake onse.

KODI MOSE ANASONYEZA BWANJI KUTI ANALI NDI CHIKHULUPIRIRO CHOLIMBA?

Nthawi zonse Mose ankakhulupirira malonjezo a Mulungu. (Genesis 22:15-18) Iye anali ndi mwayi wokhala ndi moyo wapamwamba ku Iguputo, koma “anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu, m’malo mochita zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo.” (Aheberi 11:25) Kodi pamenepa tingati Mose anasankha zinthu mopupuluma asanaganize bwino? Ayi, Baibulo limafotokoza kuti Mose “anapitiriza kupirira moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.” (Aheberi 11:27) Choncho iye sananong’oneze bondo chifukwa cha zimene anasankhazi.

Mose ankathandizanso anthu ena kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika pamene Aisiraeli ankaona kuti alibe kothawira ndipo asilikali a Farao, omwe ankawalondola, awagwira chifukwa kutsogolo kwawo kunali Nyanja Yofiira. Chifukwa cha mantha iwo anadandaulira Yehova komanso Mose. Kodi pamenepa Mose akanatani?

N’kutheka kuti Mose sankadziwa kuti Mulungu alekanitsa madzi a Nyanja Yofiira, kuti Aisiraeli awoloke pothawa adani awowo. Komabe iye anali ndi chikhulupiriro chonse kuti Mulungu achita chinachake kuti ateteze anthu ake. Mose anafuna kuti Aisiraeli anzakewo akhalenso ndi chikhulupiriro chimenechi. Baibulo limati: “Pamenepo Mose anauza anthuwo kuti: ‘Musachite mantha. Chilimikani ndi kuona chipulumutso cha Yehova chimene akuchitireni lero.’” (Ekisodo 14:13) Kodi Mose anathandizadi Aisiraeli anzakewo kukhala ndi chikhulupiriro cholimba? Inde, chifukwa Baibulo limanena za Aisiraeli onse osati Mose yekha kuti: “Mwa chikhulupiriro, anthu a Mulunguwo anawoloka Nyanja Yofiira ngati kuti akudutsa pamtunda pouma.” (Aheberi 11:29) Choncho chikhulupiriro chimene Mose anali nacho sichinathandize iye yekha koma chinathandizanso Aisiraeli anzake.

ZIMENE TIKUPHUNZIRA KWA MOSE:

Mofanana ndi Mose, nafenso tizikhulupirira malonjezo a Mulungu. Mwachitsanzo, Mulungu amalonjeza kuti tikamaika patsogolo zinthu zokhudza kulambira, iye adzatipatsa zofunika pa moyo. (Mateyu 6:33) N’zoona kuti masiku ano n’zovuta kuika zinthu zokhudza kulambira patsogolo chifukwa anthu ambiri m’dzikoli amangoganizira zopeza chuma basi. Koma tikamayesetsa kukhala moyo wosalira zambiri n’kumaika patsogolo zinthu zokhudza kulambira, tingakhale ndi chikhulupiriro choti Yehova adzatipatsa zofunika pa moyo wathu. Iye amatitsimikizira kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”—Aheberi 13:5.

Tiyeneranso kuthandiza anthu ena kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Mwachitsanzo, makolo anzeru amazindikira kuti ali ndi udindo waukulu wothandiza ana awo kuti azikhulupirira kwambiri Mulungu. Ana akamakula amafunika kudziwa kuti kuli Mulungu ndipo iye ndi amene ayenera kutiuza zoyenera kuchita ndi zimene tiyenera kupewa. Kuwonjezera pamenepo, iwo ayeneranso kukhulupirira ndi mtima wonse kuti kutsatira zomwe Mulungu amanena n’kothandiza kwambiri. (Yesaya 48:17, 18) Makolo akamathandiza ana awo kukhulupirira kuti Mulungu “alikodi, ndi kuti amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse,” ndiye kuti akuwapatsa anawo mphatso ya mtengo wapatali.—Aheberi 11:6.