Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi Mdyerekezi anachokera kuti?

Mulungu sanalenge Mdyerekezi, koma analenga mngelo wabwinobwino yemwe kenako anachita zinthu zomwe zinachititsa kuti akhale Mdyerekezi kapena kuti Satana. Yesu anasonyeza kuti poyamba Mdyerekezi anali mngelo wolungama ndipo anali mmodzi mwa ana a Mulungu.—Werengani Yohane 8:44.

Kodi zinatheka bwanji kuti mngelo wabwinobwino akhale Mdyerekezi?

Mngelo amene anakhala Mdyerekezi anapandukira Mulungu ndipo anachititsanso anthu oyambirira kupandukira Mulungu. Choncho iye anadzichititsa kukhala Satana kutanthauza “Wotsutsa.”—Werengani Genesis 3:1-5; Chivumbulutso 12:9.

Mofanana ndi anthu komanso angelo onse, mngelo amene anakhala Mdyerekezi anali ndi ufulu wosankha kuchita zabwino kapena zoipa, koma iye anayamba kufuna kuti azilambiridwa. Iye ankafuna kwambiri kuti azilambiridwa kuposa kukondweretsa Mulungu.—Werengani Mateyu 4:8, 9; Yakobo 1:13, 14.

Kodi Mdyerekezi akupitirizabe kusocheretsa anthu pogwiritsa ntchito njira ziti? Kodi tiyenera kumuopa? Mungapeze mayankho a mafunso amenewa m’Baibulo.

Mayankho a mafunso ena a m’Baibulo mungawapeze pa Webusaiti yathu