Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO: KODI MUYENERA KUOPA KUTHA KWA DZIKOLI?

Nkhani ya Kutha kwa Dziko, Kodi Ndi Yoopsa, Yosangalatsa Kapena Yokhumudwitsa?

Nkhani ya Kutha kwa Dziko, Kodi Ndi Yoopsa, Yosangalatsa Kapena Yokhumudwitsa?

Kodi mukuganiza bwanji za tsiku la 21 December, 2012, limene anthu ankanena kuti dziko litha malinga ndi kalendala ya anthu otchedwa Amaya? Mogwirizana ndi zimene munkayembekezera pa tsikuli, mwina munasangalala poona kuti zimene munkaopa sizinachitike, kapena munakhumudwa chifukwa zimene munkayembekezera sizinachitike mwinanso zinakupangitsani kuti musakhalenso ndi chidwi ndi nkhaniyi poona kuti mapeto akuchedwa. Kodi n’kutheka kuti anthu anangolakwitsa kunena kuti dziko litha pa 21 December, 2012 monga mmene akhala akuchitira m’mbuyomu?

Kodi Baibulo limafotokoza zotani pa nkhani ya “kutha kwa dziko lino lapansi?” (Mateyu 24:3, Chipangano Chatsopano Cholembedwa M’Chichewa Chamakono) Anthu ena amaopa kuti dzikoli lidzawotchedwa ndi moto pamene ena amachita chidwi kuti adzaone zomwe zidzachitike pa nthawiyo. Anthu ambiri anatopa ndi kuuzidwa kuti dzikoli litha posachedwa. Kodi zimene anthu amanenazi zidzachitikadi kapena zangokhala zinthu zimene amangoganiza basi?

Mwina mungadabwe ndi zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kutha kwa dziko. Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziyembekezera mapeto a dzikoli. Koma limanenanso kuti anthu ena amataya mtima poona kuti mapetowo akuchedwa. Tikukupemphani kuti muone mayankho a m’Baibulo a mafunso amene anthu ambiri amafunsa okhudza kutha kwa dziko.

 Kodi dzikoli lidzawotchedwa ndi moto?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: ‘Mulungu anakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba. Silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.’SALIMO 104:5.

Dziko lapansili silidzawonongedwa ndi moto kapena china chilichonse. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu analenga dzikoli kuti anthu azikhalamo mpaka kalekale. Baibulo pa Salimo 37:29 limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 115:16; Yesaya 45:18.

Mulungu atalenga zinthu zambirimbiri kuphatikizapo dziko lapansili, ananena kuti “zinali zabwino kwambiri,” ndipo amaonabe kuti zimene analengazo ndi zabwino. (Genesis 1:31) M’malo mowononga dzikoli, iye akulonjeza ‘kuwononga amene akuwononga dziko lapansi’ ndi kuteteza dzikoli kuti anthu asapitirizebe kuliwononga mpaka kalekale.—Chivumbulutso 11:18.

Mwina mungaganize kuti lemba la 2 Petulo 3:7 limanena kuti dziko lapansi lidzawotchedwa ndi moto chifukwa vesili limati: “Kumwamba kumene kulipo panopa limodzi ndi dziko lapansi, azisungira moto.” Kodi zimenezi zikusonyeza kuti dziko lapansili lidzawotchedwa ndi moto? Dziwani kuti nthawi zina Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “kumwamba,” “dziko lapansi,” ndi “moto” mophiphiritsa. Mwachitsanzo, pa Genesis 11:1 Baibulo limati: “Dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi.” (Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Pamenepa mawu akuti “dziko lapansi” akutanthauza anthu.

Mavesi ena m’chaputala 3 cha 2 Petulo amasonyeza kuti kumwamba, dziko lapansi komanso moto zimene zikutchulidwa m’chaputalachi n’zophiphiritsa. Mwachitsanzo, vesi 5 ndi 6 limayerekezera zimenezi ndi zomwe zinachitika pa nthawi ya Chigumula cha Nowa. Pa nthawiyo anawonongedwa ndi anthu osati dziko lenilenili. “Dziko” limene linawonongedwa pa nthawi ya Chigumulacho ndi anthu osamvera Mulungu. Chigumulacho chinawononganso “kumwamba” kutanthauza anthu amene ankalamulira pa nthawiyo. (Genesis 6:11) Mofanana ndi zimenezi, lemba la 2 Petulo 3:7 limalosera za chiwonongeko cha maboma ndi anthu oipa ndipo popeza anthuwa akadzawonongedwa sadzakhalakonso mpaka kalekale, zidzangokhala ngati awonongedwa ndi moto.

Kodi n’chiyani chidzachitike pa kutha kwa dziko?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.”1 YOHANE 2:17.

“Dziko” limene likutchulidwa palembali kuti likupita si dziko lapansi lenilenili, koma ndi anthu amene zochita zawo sizigwirizana ndi zofuna za Mulungu. Monga mmene dokotala amachitira kuti amangochotsa chotupa pofuna kupulumutsa moyo wa wodwala, Mulungunso  adzachotsa anthu oipa kutanthauza ‘kuwapha’ n’cholinga chakuti anthu abwino asangalale ndi moyo padziko lapansili. (Salimo 37:9) Choncho tingati anthu abwino adzasangalala ‘dzikoli’ likadzatha kapena kuti anthu oipa akadzawonongedwa.

Zimenezi zikusonyeza kuti kutha kwa dzikoli ndi nkhani yosangalatsa kwa anthu abwino. Poganizira mfundo imeneyi omasulira Baibulo ena anamasulira kuti: “Mapeto a nthawi ino.” (Mateyu 24:3) Popeza dziko lapansili ndiponso anthu abwino sadzawonongedwa, Baibulo limasonyeza kuti anthu abwinowo ndiwo adzapange dziko latsopano.—Luka 18:30.

Yesu anatchula nthawi imeneyo kuti ndi “nthawi yakukonzanso zinthu zonse.” Pa nthawi imeneyo iye adzachititsa anthu kukhalanso angwiro ngati mmene Mulungu ankafunira. (Mateyu 19:28, Chipangano Chatsopano mu M’Chichewa cha Lero) Pa nthawiyo anthu adzasangalala ndi madalitso otsatirawa:

Ngati timachita “chifuniro cha Mulungu” sitiyenera kuopa kutha kwa dzikoli koma tiyenera kusangalala nako.

Kodi mapeto ali pafupidi?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Mukadzaona zimenezi zikuchitika, mudzadziwe kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.”LUKA 21:31.

Pulofesa Richard Kyle analemba m’buku lake kuti, “kusintha kwa zinthu padzikoli kukuchititsa kuti anthu azinena zosiyanasiyana zokhudza kutha kwa dziko” makamaka ngati sakutha kumvetsa bwino chifukwa chake zinthu zikusintha choncho.—The Last Days Are Here Again.

Komabe aneneri amene analemba zokhudza kutha kwa dzikoli m’Baibulo, sanalosere potengera mmene zinthu zinalili m’nthawi yawo. M’malomwake iwo anauziridwa ndi Mulungu kufotokoza zinthu zimene zidzasonyeze kuti dzikoli lili pafupi kutha. Taonani ena mwa maulosi amenewa ndipo muone ngati akukwaniritsidwadi m’nthawi yathu ino.

Monga mmene Yesu ananenera, popeza tikuona “zinthu zonsezi,” tiyenera kudziwa kuti mapeto a dzikoli ali pafupi. (Mateyu 24:33) A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti pali umboni wonse woti mapeto ali pafupi ndipo amauza ena zimene amakhulupirirazi mwa kulalikira m’mayiko okwana 236.

Popeza mapeto sanafike pa nthawi imene ena ankakhulupirira kuti afika, kodi ndiye kuti sadzafika?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Pamene azidzati: ‘Bata ndi mtendere!’ chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo monga zowawa za pobereka za mkazi wapakati, ndipo sadzapulumuka.”1 ATESALONIKA 5:3.

Baibulo limayerekezera kuwonongedwa kwa dzikoli ndi zowawa za pobereka zimene zimayamba mwadzidzidzi. Zochitika pa nthawi yoti mapeto atsala pang’ono kufika ndi zofanana ndi zimene zimachitikira mayi woyembekezera. Ululu umene amamva miyezi ikamapita, umamuthandiza kudziwa kuti masiku ake obereka ayandikira. Dokotala akhoza kumuuza deti limene mwana wake adzabadwe. Koma ngakhale detilo litayandikira kwambiri n’kupezeka kuti mayiyo matenda sanamuyambe, akhozabe kukhala ndi chikhulupiriro choti mwana wake abadwa pasanapite masiku ambiri. Mofanana ndi zimenezi, ngakhale kuti mapeto sanafike pa nthawi imene ena ankakhulupirira kuti afika, sizikutanthauza kuti mfundo yoti tili ‘m’masiku otsiriza’ ndi yabodza.—2 Timoteyo 3:1.

Mwina mungafunse kuti, ‘Ngati palidi umboni woti mapeto ali pafupi, n’chifukwa chiyani anthu ambiri sakuzindikira zimenezi?’ Baibulo limanena kuti mapeto akamadzayandikira, anthu ambiri adzakana dala umboni woti mapetowo ayandikira. Iwo sadzakhulupirira kuti tili m’masiku otsiriza komanso kuti zinthu m’dzikoli zikuipiraipira ndipo azidzanena monyoza kuti: “Kuchokera tsiku limene makolo athu anamwalira,  zinthu zonse zikupitirirabe chimodzimodzi ngati mmene zakhalira kuyambira pa chiyambi cha chilengedwe.” (2 Petulo 3:3, 4) Choncho zizindikiro zoti tili m’masiku otsiriza zikuoneka bwino, koma anthu ambiri akungonyalanyaza dala.—Mateyu 24:38, 39.

M’nkhaniyi tangokambiranako umboni wina wa m’Malemba wosonyeza kuti mapeto ayandikira. * Kodi mungakonde kudziwa zambiri pa nkhaniyi? Pemphani a Mboni za Yehova kuti aziphunzira nanu Baibulo. Mukhoza kumaphunzirira kunyumba kwanu kapena pamalo aliwonse amene mungafune kapenanso mukhoza kumaphunzira pafoni. Phunziroli limakhala laulere chofunika kwa inu n’kungopeza nthawi yophunzirayo ndipo mudzapindula kwambiri.

^ ndime 39 Kuti mudziwe zambiri werengani mutu 9 wakuti “Kodi Tili ‘M’masiku Otsiriza’?” m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.