Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo

 ANA AZAKA ZOSAPITIRIRA ZITATU

Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo

Tsiku lina kunja kunkagwa mvula.

Tomoko anadandaula kuti:

“Ndikulephera kutuluka.

N’chifukwa chiyani mvulayi sikusiya?”

Koma kenako,

mvula ija inasiya.

Ndipo dzuwa linawala.

Tomoko anakondwera kwambiri.

Atathamangira panja,

anadabwa kwambiri

ndi zimene anaona.

Tomoko ananena kuti:

“Sindimadziwa kuti mvulayi,

yomwe ndi yochokera kwa Mulungu,

imachititsa kuti

zomera zipange maluwa.”

ZOTI MAKOLO ACHITE

Muuzeni mwana wanuyo kuti aloze:

  • Windo

  • Tomoko

  • Maluwa

  • Mbalame

  • Mtengo

Pezani zinthu zobisika izi:

  • Chikumbu

  • Ndege

Werengani Machitidwe 14:17. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova analenga mvula?