Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Yandikirani Mulungu

‘Kodi Yehova Akufuna Chiyani kwa Ife?’

‘Kodi Yehova Akufuna Chiyani kwa Ife?’

KODI Yehova amafuna kuti anthu amene amamulambira azichita chiyani? Kodi iye amafuna kuti anthuwo azichita zinthu mwangwiro, osalakwitsako chilichonse? Zikanakhala choncho bwenzi palibe aliyense yemwe akanatha kukondweretsa Mulungu chifukwa tonsefe ndife opanda ungwiro. Kapena kodi iye amafuna kuti tizichita zimene sitingakwanitse? Kupeza mayankho a mafunso amenewa kungatithandize kukhala osangalala potumikira Mulungu. Tiyeni tikambirane zimene Mulungu amafuna zomwe mneneri Mika anafotokoza.—Werengani Mika 6:8.

Iye amakuuzani zimene zili zabwino.’ Sitiyenera kungoganizira zimene Mulungu amafuna. Iye watifotokozera bwino m’Baibulo zimene amafuna. Ndipo zimene amafunazo ndi “zabwino” osati zoipa. “Mulungu ndiye chikondi,” choncho amatifunira zabwino. (1 Yohane 4:8; 5:3) Timasangalatsa Yehova tikamatsatira zimene iye amafuna ndipo kuchita zimenezi n’kothandiza kwambiri kwa ife.—Deuteronomo 10:12, 13.

‘Kodi Yehova Akufuna Chiyani Kwa Ife?’ Kodi Mulungu ali ndi mphamvu yotiuza zochita? Inde. Tiyenera kumumvera chifukwa iye ndi amene anatipatsa moyo komanso amatisamalira. (Salimo 36:9) Choncho kodi iye amafuna kuti tizichita chiyani? Mneneri Mika anafotokoza mfundo zitatu zimene tiyenera kuchita kuti tizikondweretsa Mulungu. Mfundo ziwiri zoyambirira zikukhudza mmene timachitira zinthu ndi anzathu, ndipo mfundo yachitatu ikukhudza ubwenzi wathu ndi Mulungu.

‘Muzichita chilungamo.’ Mogwirizana ndi zimene buku lina linanena, mawu achiheberi amene anamasuliridwa kuti “chilungamo” “amatanthauza kuchitira ena zabwino.” Mulungu amafuna kuti tizichitira ena zabwino mogwirizana ndi mfundo zake. Timakhala achilungamo ngati tili anthu abwino, opanda tsankho, komanso oona mtima pochita zinthu ndi ena. (Levitiko 19:15; Yesaya 1:17; Aheberi 13:18) Tikamachitira ena zachilungamo, iwonso adzatichitira chimodzimodzi.—Mateyu 7:12.

‘Mukhale okoma mtima.’ Mulungu amafuna kuti tikhale okoma mtima ndipo tiyenera kusonyeza zimenezi m’zochita zathu zonse. Mawu achiheberi omwe anawamasulira kuti “kukoma mtima” (cheʹsedh) angatanthauzenso “kukoma mtima kosatha” kapena “chikondi chosatha.” Katswiri wina wa Baibulo ananena kuti: “Mawu achiheberiwa, satanthauza chabe chikondi, chifundo ndiponso kukoma mtima koma amatanthauza makhalidwe onse atatuwa pamodzi.” Ngati tili okoma mtima, timasangalala kuthandiza ena. Tikatero tidzapeza chimwemwe chimene chimapezeka chifukwa chochitira ena zabwino.—Machitidwe 20:35.

‘Muziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wanu.’ M’Baibulo, mawu akuti ‘kuyenda’ amatanthauza “kutsatira njira inayake yochitira zinthu.” Timasonyeza kuti tikuyenda ndi Mulungu tikamatsatira zimene iye ananena m’Baibulo. Koma pochita zimenezi tiyenera kukhala ‘odzichepetsa.’ N’chifukwa chiyani zili choncho? Tikakhala odzichepetsa pamaso pa Mulungu timazindikira kuti ndife opanda ungwiro ndipo pali zina zomwe sitingathe kuchita. Choncho ‘kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu’ kumatanthauza kudziwa bwino zimene iye amafuna ndiponso zomwe ifeyo tingakwanitse kuchita.

N’zosangalatsa kuti Yehova sayembekezera kuti tizichita zimene sitingakwanitse. Iyetu amayamikira khama limene timachita pomutumikira. (Akolose 3:23) Komanso Mulungu amadziwa zomwe sitingathe kuchita. (Salimo 103:14) Modzichepetsa nafenso tikamavomereza zimenezi, tidzakhala osangalala pamene tikuyenda ndi Mulungu. Choncho tiyenera kuphunzira zomwe tingachite kuti tiyambe kuyenda ndi Mulungu. Kuchita zimenezi kudzachititsa kuti Mulungu atidalitse kwambiri.—Miyambo 10:22.

Mavesi amene mungawerenge mu November:

Yoweli 1-3Mika 1-7