Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

Kodi Mulungu Adzakhazikitsa Boma Lolamulira Dziko Lonse Lapansi?

Kodi Mulungu Adzakhazikitsa Boma Lolamulira Dziko Lonse Lapansi?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. N’chifukwa chiyani anthu akufunikira boma lolamulira dziko lonse lapansi?

Masiku ano anthu ambiri padziko lonse akukumana ndi mavuto. M’mayiko ambiri muli anthu osauka komanso oponderezedwa. Pamene m’mayiko ena anthu ali ndi zinthu zochuluka. Boma limene lingalamulire dziko lonse lapansi ndi limene lingathe kugawira anthu mofanana zinthu zimene zili padzikoli.—Werengani Mlaliki 4:1; 8:9.

2. Kodi ndani angakhale woyenera kupatsidwa udindo wolamulira dziko lonse lapansi?

Anthu ambiri sangafune kuti dziko lonse lapansi lizilamuliridwa ndi boma limodzi chifukwa amaona kuti palibe munthu amene angakwanitse kulamulira bwino dzikoli. Komanso palibe wolamulira amene anthu a m’mayiko onse angamuone kuti ndi wabwino. Vuto linanso ndi lakuti anthu ambiri akakhala pa udindo amagwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika. Choncho anthu ambiri amaona kuti ngati wolamulirayo atakhala wankhanza, ndiye kuti padziko lonse pangakhale mavuto.—Werengani Miyambo 29:2; Yeremiya 10:23.

Yehova Mulungu wasankha Mwana wake, Yesu, kuti adzalamulire dziko lonse lapansi kwamuyaya. (Luka 1:32, 33) Yesu amadziwa bwino mavuto a anthu chifukwa choti anakhalapo padzikoli. Ali padziko lapansi pano, iye anachiritsa odwala, kuphunzitsa anthu a mitima yabwino komanso ankapeza nthawi yocheza ndi ana. (Maliko 1:40-42; 6:34; 10:13-16) Choncho Yesu ndi yemwe ali woyenera kulamulira dziko lonse.—Werengani Yohane 1:14.

 3. Kodi n’zothekadi kukhala ndi boma loti lizilamulira dziko lonse lapansi?

Mulungu wasankha Mwana wake kuti adzalamulire dziko lapansi ali kumwamba. (Danieli 7:13, 14) Mofanana ndi mmene zimakhalira kuti wolamulira sachita kufunika kuti azikhala mumzinda uliwonse wa m’dziko limene akulamulira, Yesunso sadzafunika kuchita kukhala padzikoli kuti akwanitse kulamulira anthu.—Werengani Mateyu 8:5-9, 13.

Kodi anthu onse adzavomereza Yesu kukhala Wolamulira wawo? Ayi. Anthu okhawo amene amakonda zabwino ndi amene adzalole kuti Yesu awalamulire. Yehova adzawononga anthu onse amene adzakane Yesu, yemwe ndi Wolamulira wachikondi komanso wachilungamo amene iye wamusankha.—Werengani Mateyu 25:31-33, 46.

4. Kodi Wolamulira ameneyu adzachita chiyani?

Monga mmene m’busa amasonkhanitsira nkhosa zake, Yesunso anayamba kale kusonkhanitsa anthu a mitima yabwino kuchokera m’mitundu yonse ndipo akuwaphunzitsa kuti azichita zinthu mwachikondi ngati mmene Mulungu amachitira. (Yohane 10:16; 13:34) Anthu oterewa akaphunzira za Mulungu amakhala otsatira a Yesu ndipo amamuona kuti ndi Mfumu yawo. (Salimo 72:8; Mateyu 4:19, 20) Padziko lonse lapansi, otsatira a Yesu amenewa amadziwitsa anthu kuti Yesu ndi Mfumu ndipo amachita zimenezi mogwirizana.—Werengani Mateyu 24:14.

Posachedwapa Yesu adzapulumutsa anthu amene akhala akuponderezedwa ndi maboma oipawa. Iye wasankha otsatira ake ena kuti adzalamulire naye dziko lapansi ali kumwamba. (Danieli 2:44; 7:27) Ufumu wa Yesu udzachititsa kuti padzikoli pakhale anthu odziwa Yehova okhaokha ndipo udzabwezeretsa paradaiso amene analipo Adamu ndi Hava atangolengedwa kumene.—Werengani Yesaya 11:3, 9; Mateyu 19:28.