Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi kale ankagwiritsa ntchito inki komanso zolembera zotani?

Pa makalata atatu omwe mtumwi Yohane analemba m’Baibulo, kumapeto kwa kalata yake yachitatu iye analemba kuti: “Ndinali ndi zambiri zoti ndikulembere, koma sindikufuna kuti ndipitirize kukulembera ndi inki ndi cholembera.” Mawu amene Baibulo lina linagwiritsa ntchito pomasulira mawu achigiriki omwe anali pavesi limeneli, amasonyeza kuti Yohane sanafune kupitiriza kulemba ndi “[inki] yakuda ndi bango.”—3 Yohane 13, The Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures.

Zolembera zimene anthu akale ankagwiritsa ntchito zinkapangidwa ndi bango limene ankalisongola mbali imodzi ndipo ankasongola zolemberazi ndi mwala wosasalala. Zolembera zabangozi zinkafanana komanso kugwira ntchito monga mmene zolembera zina zamasiku ano zimagwirira ntchito.

Nthawi zambiri inki ya zolemberazi ankaipanga posakaniza mwaye ndi ulimbo umene unkapangitsa mwayewo kuti ugwirane pamodzi. Inki imeneyi inkakhala yolimba ndipo munthu ankachita kusungunula ndi madzi asanaigwiritse ntchito. Akamalembera inki yotereyi sinkalowerera mkatikati mwa gumbwa amene ankalembapo. Choncho munthu akalakwitsa kulemba ankatha kufufuta pogwiritsira ntchito kansalu konyowa, kamene wolemba aliyense ankakhala nako. Nkhani yokhudza zolembera ndi inkiyi, ikutithandiza kudziwa zimene anthu ena amene analemba Baibulo ankatanthauza pamene ananena zoti Mulungu adzafafaniza mayina m’buku lake la moyo.—Ekisodo 32:32, 33; Chivumbulutso 3:5.

Kodi mahema omwe mtumwi Paulo ankapanga anali otani?

Lemba la Machitidwe 18:3 limanena kuti mtumwi Paulo ankagwira ntchito yopanga mahema kapena kuti matenti. Kale anthu opanga mahema, ankaluka ubweya wa ngamila kapena wa mbuzi n’kupanga nsalu. Akatero ankalumikiza nsaluzo n’kupanga mahema amene anthu apaulendo ankagwiritsa ntchito. Komabe mahema ambiri pa nthawiyo ankakhala opangidwa ndi zikopa. Mahema ena ankakhala opangidwa ndi nsalu zimene zinkachokera m’tawuni ya Tariso komwe kunali kwawo kwa Paulo. N’kutheka kuti Paulo ankagwiritsira ntchito zikopa kapena nsalu popanga mahemawa. Pa nthawi imene Paulo ankagwira ntchito ndi Akula, ankapanga mahema oteteza kudzuwa amene ankagwiritsidwa ntchito m’nyumba za anthu.

Paulo ayenera kuti anaphunzira ntchito yopanga mahemayi ali mnyamata. Umboni womwe unapezeka m’zolembedwa zagumbwa zimene zinapezeka ku Egypt zimasonyeza kuti pa nthawi imene Aroma ankalamulira dzikoli, anyamata ankayamba kuphunzira ntchito zosiyanasiyana ali ndi zaka 13. Ngati Paulo anayamba kuphunzira ntchito yopanga mahema ali ndi zaka 13, ndiye kuti pa nthawi imene anali ndi zaka 15 kapena 16 n’kuti ataidziwa bwino ntchitoyi moti ankatha kudula nsalu n’kuisoka mwaluso pogwiritsira ntchito zisongole zosiyanasiyana. Buku lina linanena kuti: “Paulo atamaliza kuphunzira ntchitoyi, ayenera kuti anapatsidwa zipangizo zogwirira ntchito yakeyi.” (The Social Context of Paul’s Ministry) Buku lomweli linanenanso kuti: “Popeza zipangizo zogwirira ntchitoyi zinali mipeni ndi zisongole basi, munthu ankatha kukagwirira ntchitoyi kulikonse.” Choncho Paulo ankatha kugwira ntchito imeneyi n’kumadzisamalira pa ntchito yake yaumishonale.