Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Funso Lachiwiri: Kodi Chidzandichitikire N’chiyani Ndikadzamwalira?

Funso Lachiwiri: Kodi Chidzandichitikire N’chiyani Ndikadzamwalira?

ROMAN ali mnyamata, mnzake wapamtima anamwalira pa ngozi ya galimoto. Iye anati: “Imfa ya mnzanga ameneyu inandikhudza kwambiri. Kwa zaka zambiri chichitikereni ngoziyi, ndinkadzifunsa kuti chimachitika n’chiyani anthufe tikamwalira?”

N’chifukwa chiyani anthu amafunsa funso limeneli?

Imfa sizolowereka. Palibe munthu amene amafuna kufa ngakhale atakhala kuti ndi wokalamba. Anthu ambiri amakhala ndi mantha posadziwa zimene zidzawachitikire akadzafa.

Kodi anthu ena amayankha bwanji funsoli?

Anthu ambiri amakhulupirira kuti munthu akamwalira, mzimu wake suufa. Iwo amakhulupiriranso kuti anthu abwino amapita kukasangalala kumwamba pamene anthu oipa amakalangidwa kumoto kwa moyo wawo wonse chifukwa cha machimo awo. Anthu ena amakhulupirira kuti munthu akamwalira, ndiye kuti basi zake zathera pomwepo ndipo pakapita nthawi anthu amamuiwala.

Kodi mayankho amenewa akusonyeza kuti anthu ambiri ali ndi maganizo otani?

Anthu amene amakhulupirira kuti munthu akamwalira mzimu wake suufa, ndiye kuti amaganiza kuti mzimu wakewo umapitirizabe kukhala ndi moyo. Pomwe anthu amene amakhulupirira kuti munthu akamwalira ndiye kuti basi zake zathera pomwepo, amaona kuti moyo ulibe cholinga chilichonse. Choncho iwo amakhala ndi maganizo akuti: “Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.”—1 Akorinto 15:32.

Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhaniyi?

Baibulo siliphunzitsa kuti munthu akamwalira pali chinachake chimene sichifa. Kudzera mwa Mfumu Solomo, Mulungu ananena kuti: “Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5) Anthu amene “sadziwa chilichonse” sangathe kuchita kanthu. Choncho anthu akufa sangatithandize kapena kutichitira zoipa.

Mosiyana ndi zimene ambiri amakhulupirira, Mulungu sanafune kuti anthu azifa. Iye analenga munthu woyambirira, Adamu, n’cholinga choti akhale ndi moyo kosatha padziko lapansi. Nthawi  yoyamba imene Mulungu anatchula za imfa, ndi pamene ankauza Adamu za chilango chimene adzapatsidwe ngati sadzamvera. Iye analetsa Adamu kuti asadye chipatso cha mtengo winawake ndipo anamuchenjeza kuti akadzadya, ‘adzafa ndithu.’ (Genesis 2:17) Adamu ndi Hava akanamvera, iwo komanso ana awo akanakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi.

Adamu anasankha kusamvera zimene Mulungu ananena. Choncho anafa chifukwa anachimwa. (Aroma 6:23) Adamu atafa sanapite kulikonse komanso mzimu wake sunapitirize kukhala ndi moyo. Mulungu anauza Adamu kuti: “Udzadya chakudya kuchokera m’thukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa. Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Popeza tonsefe tinachokera kwa Adamu, n’chifukwa chake timachimwa ndiponso timafa.—Aroma 5:12.

Ngakhale kuti Adamu anasankha kusamvera, Mulungu adzakwaniritsa cholinga chake chodzaza dziko lapansi ndi ana a Adamu. (Genesis 1:28; Yesaya 55:11) Posachedwapa Yehova adzaukitsa anthu ambiri amene anamwalira. Ponena za nthawi imeneyo, mtumwi Paulo ananena kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Machitidwe 24:15.

Roman, yemwe tamutchula poyamba uja, anaphunzira zimene Baibulo limaphunzitsa ponena za zimene zimachitika munthu akamwalira komanso zokhudza Yehova Mulungu. Tikukupemphani kuti muwerenge nkhani yonena za iye patsamba 11 m’magazini ino.