Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Yandikirani Mulungu

“Wamasiku Ambiri Anakhala pa Mpando”

“Wamasiku Ambiri Anakhala pa Mpando”

BAIBULO limanena kuti: “Palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse.” (Yohane 1:18) Mulungu ali ndi ulemelero waukulu moti palibe munthu amene angathe kumuona n’kukhalabe ndi moyo. (Ekisodo 33:20) Komabe m’Baibulo muli nkhani zina zimene zimasonyeza kuti Yehova anaonetsa anthu ena masomphenya akumwamba. Mmodzi mwa anthu amenewa anali mneneri Danieli. N’zosakayikitsa kuti zimene iye anaona zinamupangitsa kuti azilemekeza kwambiri Mulungu ndipo ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi. Taonani mmene Danieli anafotokozera zimene anaona m’masomphenya ake. *Werengani Danieli 7:9, 10.

“Wamasiku Ambiri anakhala pa mpando.” Mawu akuti “Wamasiku Ambiri,” omwe ndi Danieli yekha yemwe anawagwiritsa ntchito, akutanthauza “munthu wakale kapena wa zaka zambiri.” (Danieli 7:9, 13, 22) Kodi Yehova wakhalapo zaka zambiri bwanji? Popeza iye ndi “Mfumu yamuyaya,” anakhalapo kuyambira kalekale ndipo adzapitiriza kukhalapobe mpaka kalekale. (1 Timoteyo 1:17; Yuda 25) Mulungu alibe chiyambi komanso mapeto ndipo zimenezi zikusonyeza kuti iye ali ndi nzeru zopanda malire chifukwa Baibulo limasonyeza kuti munthu akakhala ndi zaka zambiri amakhala wanzeru. (Yobu 12:12) N’zoona kuti mfundo yoti Mulungu alibe chiyambi komanso mapeto ndi yovuta kwa anthufe kuimvetsa. Koma sitingayembekezere kudziwa zonse zokhudza nzeru za Mulungu zomwe n’zosayerekezeka.—Aroma 11:33, 34.

Onani kuti vesi 9 lanena kuti Wamasiku Ambiri “anakhala pa mpando.” N’chifukwa chiyani iye anakhala pampando? Mavesi oyandikana ndi vesili ali ndi mawu akuti “Bwalo la Milandu” komanso “chiweruzo” ndipo zimenezi zikutithandiza kudziwa chifukwa chake anakhala pampando. (Danieli 7:10, 22, 26) Choncho m’masomphenyawa, Danieli anaona Yehova atakhala pampando monga Woweruza. Kodi iye ankaweruza ndani? Ankaweruza mitundu ya anthu, omwe Danieli m’masomphenya ake oyambirira anawatchula kuti zilombo. * (Danieli 7:1-8) Kodi Yehova ndi Woweruza wotani?

“Zovala zake zinali zoyera kwambiri. Tsitsi lake linali looneka ngati ubweya wa nkhosa.” Nkhosa zina zimakhala ndi ubweya woyera, choncho tsitsi looneka ngati ubweya wa nkhosa liyenera kukhala loyera. Apa, ndiye kuti Danieli anaona Woweruza wa tsitsi loyera ngati ubweya wa nkhosa atavala mkanjo woyera. Mawu ophiphiritsa amenewa akutithandiza kudziwa kuti Yehova ndi Woweruza wachilungamo komanso wanzeru. Iye ndi Woweruza amene tiyenera kumukhulupirira ndiponso kumulemekeza kwambiri.

Yehova ndi Woweruza amene tiyenera kumukhulupirira ndi kumulemekeza kwambiri

“Panali atumiki okwana miliyoni imodzi amene anali kumutumikira nthawi zonse, ndi atumiki enanso mamiliyoni 100 amene anali kuimirira pamaso pake nthawi zonse.” Kodi atumiki a Mulungu akumwamba amenewa ndi ndani? Baibulo limanena kuti angelo ndi “atumiki” a Mulungu. (Salimo 104:4) Angelo a Mulungu, omwe alipo mamiliyoni ambirimbiri, nthawi zonse ‘amamvera malamulo ake’ komanso ‘kuchita chifuniro chake.’ (Salimo 103:20, 21) Umenewutu ndi umboni winanso wosonyeza kuti Mulungu ali ndi nzeru zopanda malire. Yehova yekha ndi amene angathe kukhala ndi gulu la angelo ambiri chonchi n’kumawatsogolera bwino komanso kuwapatsa zochita nthawi zonse kwa zaka zambirimbiri.

Masomphenya amene Danieli anaona amatithandiza kukhulupirira kwambiri Yehova yemwe ndi Wamasiku Ambiri. Yehova amaweruza mwachilungamo komanso ndi wanzeru zopanda malire. Tikukulimbikitsani kuti muphunzire zambiri zokhudza mmene mungayandikirire Mulungu ameneyu.

Mavesi amene mungawerenge mu October:

Danieli 4-12Hoseya 1-14

^ ndime 1 Sikuti Danieli anaona Mulungu. Koma Mulunguyo anangomuonetsa masomphenya m’maganizo mwake. Pofotokoza zimene anaona m’masomphenyawo, Danieli anagwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa komanso oyerekezera omwe amam’fotokoza Mulungu ngati munthu. Kafotokozedwe kameneka kamangotithandiza kumvetsa mmene Mulungu alili koma sizikutanthauza kuti iye amaoneka ngati munthu.

^ ndime 3 Kuti mudziwe zambiri zokhudza masomphenya a zilombo omwe Danieli anaona, werengani mutu 9 m’buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli! lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.