Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Zoti Achinyamata Achite

Pewani Mtima Wofuna Kutchuka

Pewani Mtima Wofuna Kutchuka

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezani kuti inuyo mukuona zimene zikuchitikazo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera mu mtima mwawo.

Amene akutchulidwa kwambiri m’nkhaniyi: Davide, Abisalomu ndi Yowabu.

Chidule cha nkhaniyi: Abisalomu ankafuna kulanda ufumu wa bambo ake.

ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.—WERENGANI 2 SAMUELI 14:25-33; 15:1-17; 18:9-17, 30-33.

Kodi mukuganiza kuti Abisalomu ankaoneka bwanji? (Werenganinso 2 Samueli 14:25, 26.)

Kodi mukuganiza kuti Abisalomu anali ndi zolinga zotani, pamene ankakopa anthu omwe ankabwera kwa mfumu kuti awaweruzire milandu? Nanga mawu ake ankamveka bwanji? (Werenganinso 2 Samueli 15:2-6.)

Malinga ndi zimene zili palemba la 2 Samueli 14:28-30, kodi mukuganiza kuti Abisalomu anali munthu wotani?

FUFUZANI MOZAMA.

Kodi Abisalomu anachita chiyani kuti alande ufumu? (Zokuthandizani: Werengani 2 Samueli 13:28, 29. Aminoni anali mwana wamkulu wa Davide, choncho iye ndi amene anali woyenera kudzalowa ufumu.)

Ngakhale kuti Abisalomu ankafuna kukhala mfumu komanso kutchuka, kodi mmene anaikidwira m’manda zikusonyeza kuti anthu ankamuona kuti anali munthu wotani? (Werenganinso 2 Samueli 18:17.)

Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chinachititsa Abisalomu kukhala ndi mtima wofuna kutchuka? (Yerekezerani ndi zimene lemba la 3 Yohane 9, 10 limanena zokhudza Diotirefe.)

 Kodi zimene Abisalomu ankachita zinamukhudza bwanji Davide? (Zokuthandizani: Werengani Salimo 3:1-8. Davide analemba salimo limeneli pa nthawi imene Abisalomu anamuukira.)

GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA . . .

Kuwopsa kokhala ndi mtima wofuna kutchuka.

Mavuto amene makolo komanso anthu ena angakumane nawo chifukwa cha zochita za mwana.

MMENE MUNGAGWIRITSIRE NTCHITO MFUNDOZI.

Ndi zinthu ziti zimene zingakuchititseni kuti muyambe kukhala ndi mtima wofuna kutchuka?

Kodi mungapewe bwanji kunyada?

M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ITI IMENE YAKUKHUDZANI MTIMA KWAMBIRI, NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

Mukuganiza bwanji? Kodi Abisalomu akanakhala kuti anali wodzichepetsa, zikanamuyendera bwanji?—Miyambo 18:12.