Mmene Mawu a Mulungu Anathandizira Banja Lathu Lachihindu
SINDIDZAIWALA zimene zinachitika Lolemba pa August 22, 2005 pamene banja lathu linasonkhana pa chakudya cha m’mawa. Pa nthawiyo sizinkadziwika ngati ndingakhale ndi moyo chifukwa ndinali ndi chotupa chachikulu muubongo. Mwamuna wanga, dzina lake Krishna, anapemphera ndipo kenako ndinayamba kulankhula ndi abale angawo.
Ndinawauza kuti: “Ndikupita kuchipatala kukachitidwa opaleshoni yaikulu kwambiri moti za moyo wanga sizikudziwika, choncho mungokonzekera chilichonse chimene chingachitike. Ngati ndingamwalire, ndakonzeratu zonse zokhudza mwambo wa maliro anga. Kwa inu amene mukutumikira Yehova, ndikukulimbikitsani kuti chonde musasiye. Inu amene simunayambe, ndikukupemphani kuti muyambe kuphunzira Baibulo komanso kusonkhana ndi Mboni za Yehova. Ngati mutachita zimenezi, tidzakhala limodzi m’paradaiso padziko lapansi mmene anthu omwe amatumikira Mulungu adzakhala kosatha ali ndi thanzi labwino.”
Ndisanafotokoze mmene opaleshoniyi inayendera, ndifotokoze kaye mmene ndinakulira komanso zimene zinachititsa kuti ndidziwe Mulungu woona.
Ndinakulira M’banja Lachihindu
Banja lathu linkakhala mumzinda wa Durban womwe uli m’mbali mwa nyanja yamchere ku South Africa. Tinkakhala m’nyumba yaikulu yomangidwa ndi matabwa ndiponso zitsulo ndipo nyumbayi inali paphiri. Kuti tifike pageti la nyumba yathu, tinkakwera masitepe okwana 125 kuchokera mumsewu waukulu. Tikakwera masitepe amenewa, tinkafika m’kanjira kam’tchire komwe kankatifikitsa pageti. Kumbali ina ya getili, kunali kachisi wa agogo anga aakazi ndipo pakachisipa panali zithunzi komanso zifaniziro za milungu yachihindu. Agogo aakazi ankandiuza kuti ndine “mwana wapakachisi.” Iwo ankandiuzanso kuti milungu imene tinkailambira ndi imene inachititsa kuti ndibadwe. Kumbali ina ya getili kunali masitepe ofiira omwe ankakafika pachitseko chakutsogolo kwa nyumba yathu. Nyumbayi inali yaikulu kwambiri ndipo inali ndi kolido yaitali, khitchini yaikulu yokhala ndi sitovu ya malasha, zipinda zogona 7 komanso kanyumba kena kapanja. Anthu amene tinkakhala m’nyumbayi tinalipo 27. Munali agogo anga, bambo anga, azichimwene atatu a bambo komanso mchemwali wawo wa bambo ndipo onsewa anali ndi mabanja awo.
Sinali ntchito yamasewera kusamalira banja lalikulu chonchili. Koma kukhala nyumba imodzi kunathandiza kuti banja lathu lizigwirizana komanso kuti tizisangalala. Mayi anga, omwe dzina lawo ndi Gargee Devi, komanso azimayi anga aang’ono aja ankathandizana ntchito zapakhomo. Iwo ankasinthana kuyeretsa pakhomo komanso kuphika chakudya. Agogo aamuna ndi amene anali mutu wa banja lonseli ndipo ankagula chakudya cha banjali. Lachitatu lililonse iwo ndi agogo aakazi ankapita kumsika kukagula nyama, zipatso komanso masamba zokwanira mlungu wonse. Anafe tinkakonda kukhala pansi pa mtengo wa paini n’kumawadikirira. Tikangowaona akutsika basi, tinkathamanga kutsika masitepe 125 aja kukawalandira mabasiketi aakulu omwe munkakhala zinthu zosiyanasiyana.
Pakhomo pathu panali mtengo wa mgwalangwa wautali womwe mbalame zinkamangamo zisa. Mbalamezi zinkakonda kuuluka komanso kulira. Nthawi zambiri agogo aakazi ankakhala
pamasitepe a khomo lakutsogolo, n’kumatiuza nthano ndipo zinkangokhala ngati akumasulira zomwe mbalamezi zikuimba. Pali zinthu zambiri zomwe zinkachitika kunyumba kwathu zimene ndimazikumbukirabe. Tinkaseka, kulira komanso kupemphera limodzi monga banja. Komanso kunyumba kwathuku n’kumene tinayambira kuphunzira za Mlengi wathu, Yehova, ndi Mwana wake Yesu Khristu.Kale, tisanayambe kuphunzira za Yehova, tsiku lililonse tinkachita miyambo yachipembedzo chathu chachihindu. Tinkakhalanso ndi zikondwerero pafupipafupi pamene tinkalambira milungu yathu yaimuna ndi yaikazi ndipo pa nthawiyi tinkaitananso anthu ena. Nthawi zina pa nthawiyi agogo aakazi ankagwidwa mizimu ndipo ankati akulankhulana ndi mizimuyo. Ndiyeno pakati pa usiku tinkapereka nsembe za nyama pofuna kuti mizimuyo isangalale. Nawonso agogo aamuna ankathandiza kwambiri m’dera lathu pa ntchito zomanga sukulu komanso akachisi achihindu.
Mmene Tinaphunzirira Choonadi Chonena za Yehova
Mu 1972 agogo aamuna anadwala ndipo anamwalira. Patapita miyezi ingapo akazi awo a bambo anga aang’ono, dzina lawo a Jane, anapatsidwa magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi azimayi awiri a Mboni za Yehova. Iwo anadandaula kuti sanawalowetse m’nyumba a Mboniwo. Nthawi zonse a Mboni akabwera kunyumba kwathu sitinkawalandira bwino. Koma pa nthawi ina a Mboniwo atabweranso, a mayi anga aang’onowa anawalowetsa m’nyumba ndipo anawafotokozera mavuto awo a m’banja okhudza amuna awo omwe ankamwa mowa mwauchidakwa. Anthu osiyanasiyana komanso achibale ankawauza mayi angawa kuti angothetsa banja. Koma a Mboniwo anawafotokozera mmene Mulungu amaonera ukwati. (Mateyu 19:6) Mayi angawa anachita chidwi ndi malangizo a m’Baibulo ndiponso zimene limalonjeza zokhudza moyo wabwino umene anthu adzakhale nawo padziko lapansi. * Iwo anaganiza kuti asathetse banja lawo ndipo anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Mayiwa akamaphunzira ndi a Mboni pabalaza, azimayi anga ena aja ankamvetsera ali m’zipinda zawo.
M’kupita kwa nthawi, azimayi anga onse aja nawonso anayamba kuphunzira Baibulo. Mayi anga aang’ono, a Jane, anayamba kuuza ena zimene ankaphunzira ndipo nthawi zambiri ankatiwerengera ndi kutifotokozera nkhani za m’buku lakuti Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuruyo. * Azibambo anga aang’ono aja atamva kuti azimayi anga ayamba kuphunzira Baibulo, sanagwirizane nazo ngakhale pang’ono. Abambo anga ena anatenga mabuku athu onse, ndi Baibulo lomwe, n’kuwawotcha. Tikapita kumisonkhano ya Mboni, ankatikalipira komanso kutimenya. Bambo anga okha ndi amene sankachita nawo zimenezi ndipo sankatiletsa kuphunzira za Yehova. Komabe azimayi anga onse aja anapitirizabe kusonkhana ndi Mboni za Yehova ndipo anayamba kukonda kwambiri Yehova Mulungu.
Mu 1974 a Jane anabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova ndipo pasanapite nthawi, mayi anga komanso azimayi ena aja anabatizidwanso. Patapita nthawi agogo aakazi nawonso anasiya chipembedzo chachihindu. Kwa zaka zambiri ndinkangotsatira amayi anga ndipo ndinkapezeka
pa misonkhano yonse ya Mboni. Kenako pa msonkhano waukulu wa Mboni za Yehova, wa Mboni wina dzina lake Shameela Rampersad, anandifunsa kuti, “Kodi ubatizidwa liti?” Ndinamuyankha kuti, “Inetu sindingabatizidwe chifukwa sindiphunzira Baibulo ndi aliyense.” Iye anandiuza kuti ayamba kundiphunzitsa Baibulo. Pa msonkhano wotsatira umene unachitika pa December 16, 1977 ndinabatizidwa. Patapita nthawi, pa anthu 27 a m’banja lathu, anthu 18 anabatizidwa. Koma pa nthawi yomwe ndinachitidwa opaleshoni ija n’kuti bambo anga, a Sonny Deva, adakali m’chipembedzo chachihindu.“Musamade Nkhawa Ndi Kanthu Kalikonse”
Mawu a palemba la Afilipi 4:6, 7 anandithandiza kwambiri makamaka pa nthawi yomwe anandipeza ndi chotupa chachikulu muubongo. Lemba limeneli limati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” N’zovuta kuti munthu ‘usamade nkhawa’ makamaka ngati wauzidwa kuti nthawi ina iliyonse ukhoza kufa. Poyamba ndinkangolira koma nditapemphera kwa Yehova, ndinayamba kukhala ndi “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.”
Zinali ngati Yehova Mulungu anandigwira dzanja lamanja n’kumanditsogolera. (Yesaya 41:13) Iye anandithandiza kufotokoza molimba mtima kwa madokotala cholinga changa chomvera lamulo la m’Baibulo pa nkhani ya kupewa magazi. (Machitidwe 15:28, 29) Zimenezi zinachititsa kuti dokotala amene anandipanga opaleshoni komanso wopereka mankhwala opha ululu avomereze kundipanga opaleshoni popanda kundithira magazi. Atamaliza, dokotalayo ananena kuti opaleshoniyo yayenda bwino kwambiri ndipo anachotsa chotupa chonse. Iye ananenanso kuti sanaonepo wodwala atatsitsimuka mwamsanga, ngati mmene ndinachitira ineyo, pambuyo pochitidwa opaleshoni ya chotupa muubongo.
Patangodutsa milungu itatu ndinakwanitsa kuchititsa phunziro la Baibulo ndidakali m’chipatala. Patatha milungu 7 ndinayambanso kuyendetsa galimoto, kupita kukalalikira komanso kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Ndimayamikira a Mboni anzanga amene ndinkapita nawo kolalikira. Iwo ankaonetsetsa kuti sindili ndekha komanso ndafika bwinobwino kunyumba. Ndimaona kuti kumvetsera Baibulo patepi komanso kukonda kwambiri zinthu zauzimu kunandithandiza kuti ndichire mwamsanga.
Ndinasangalalanso kwambiri kuona kuti pambuyo pa opaleshoni yanga, bambo anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Iwo anabatizidwa ali ndi zaka 73 ndipo akutumikira Yehova modzipereka. Pakali pano, pali achibale oposa 40 amene akutumikira Yehova. Ngakhale kuti diso langa lakumanzere linawonongeka ndiponso anandiika tizitsulo m’mutu, ndikuyembekezera nthawi imene Yehova adzapange ‘zinthu zonse kukhala zatsopano’ m’Paradaiso padziko lapansi.—Chivumbulutso 21:3-5.
Ndimayamikira kuti ndili ndi mwamuna wachikondi yemwenso ndi mkulu mumpingo. Ndimayamikiranso mwana wanga wamkazi, dzina lake Clerista, yemwe amandithandiza kuti ndipitirize kulalikira nthawi zonse. Yehova Mulungu wadalitsa kwambiri utumiki wanga moti ndathandiza anthu ambiri kusintha moyo wawo chifukwa cha zimene Baibulo limaphunzitsa. Pa anthu amenewa, oposa 30 anadzipereka kwa Mulungu ndipo anabatizidwa.
Ndimayembekezera mwachidwi nthawi imene Yehova Mulungu adzathetse mavuto onse amene ali m’dzikoli n’kubweretsa paradaiso.
^ ndime 12 Kuti mudziwe zambiri zokhudza cholinga cha Mulungu cha dziko lapansi, werengani mutu 3 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ ndime 13 Buku limeneli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma anasiya kulisindikiza.