Phunzirani Zimene Mawu A Mulungu Amanena
Kodi N’zotheka Kukhala Ndi Moyo Kwamuyaya?
Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.
1. Kodi n’chifukwa chiyani moyo wathu umaoneka kuti ndi waufupi?
Pali akamba ena amene amakhala ndi moyo zaka 150 komanso mitengo ina imene imakhala kwa zaka 3,000. Koma anthu amakhala ndi moyo zaka zochepa kwambiri poyerekezera ndi zaka zimenezi. Komatu munthu akhoza kuchita zinthu zaphindu kwambiri kuposa kamba komanso mtengo. Yehova Mulungu analenga anthu m’njira yoti azitha kusangalala ndi zinthu ngati nyimbo, masewera, chakudya, kuphunzira, kuona malo osiyanasiyana komanso kudziwana ndi anthu. Mulungu anatipatsa mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.—Werengani Mlaliki 3:11.
2. Kodi n’zothekadi kukhala ndi moyo kwamuyaya?
Yehova ndi wamuyaya ndipo sadzafa. Iye ndi kasupe wa moyo choncho akhoza kupatsa anthu moyo wosatha. (Salimo 36:9; Habakuku 1:12) Komanso iye analonjeza kuti adzapereka moyo wosatha kwa anthu amene amamumvera. Yehova adzachotsanso chimene chimachititsa kuti anthu azikalamba.—Werengani Yobu 33:24, 25; Yesaya 25:8; 33:24.
Zimene Yesu anachita ali padziko lapansi ndi umboni wakuti lonjezo la Mulungu la moyo wosatha komanso wopanda matenda lidzakwaniritsidwadi. Yesu anachiritsa anthu odwala matenda osiyanasiyana ndiponso anaukitsa akufa.—Werengani Luka 7:11-15, 18, 19, 22.
3. Kodi ndi liti pamene anthu adzakhale ndi moyo wosatha?
Mulungu amafuna kuti tikhale ndi moyo wosatha, osati m’dziko lachiwawa ndi loponderezanali, koma m’paradaiso. Iye amafuna kuti tizikhala moyo wopanda vuto lililonse. (Salimo 37:9, 29; Yesaya 65:21, 22) Mulungu adzabwezeretsa dziko lapansili kuti likhalenso Paradaiso ndiponso adzaukitsa anthu amene anamwalira. Anthu oukitsidwa omwe adzasankhe kulambira Mulungu komanso kumumvera, adzakhala ndi moyo kwamuyaya.—Werengani Luka 23:42, 43; Yohane 5:28, 29.
4. Kodi tingatani kuti tidzapeze moyo wosatha?
Mulungu yekha ndi amene angatipatse moyo wosatha choncho tingachite bwino kumuyandikira mwa kuyesetsa kuphunzira za iye kuti timudziwe. Baibulo limayerekezera kuphunzira za Mulungu ndi kudya chakudya. (Mateyu 4:4) Kudya chakudya kumakhala kosangalatsa koma pamafunika khama kuti upeze komanso ukonze chakudyacho. N’chimodzimodzinso ndi kuphunzira za Mulungu chifukwa nakonso kumafuna khama. Koma palibe chinthu chimene tingachite chomwe ndi chofunika kwambiri kuposa kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu n’kudzapeza moyo wosatha.—Werengani Luka 13:23, 24; Yohane 6:27; 17:3.