Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

KODI n’chiyani chinathandiza munthu wina amene anakula movutika kwambiri komanso anali chidakwa kuti akhale mwamuna wosangalala komanso bambo wachikondi? Nanga n’chiyani chinathandiza mayi wina, yemwe poyamba anali ndi makhalidwe oipa, kuti asinthe moyo wake? Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene anthuwa ananena.

“Ndinkadziona kuti ndine munthu wosafunika.”​—VÍCTOR HUGO HERRERA

  • CHAKA CHOBADWA: 1974

  • DZIKO: CHILE

  • POYAMBA: NDINALI CHIDAKWA

KALE LANGA:

Ndinabadwira mumzinda wokongola wa Angol womwe uli kum’mwera kwa dziko la Chile. Bambo anga sindikuwadziwa. Pamene ndinali ndi zaka zitatu, mayi anga anatenga ineyo ndi mchimwene wanga n’kusamukira mumzinda wa Santiago, womwe ndi likulu la dzikoli. Kumeneko tinkakhala m’kanyumba kopanda chipinda. Tinkagwiritsa ntchito chimbudzi chapanja chimene chinkagwiritsidwanso ntchito ndi anthu ambiri. Komanso tinkakatunga madzi pachipaipi cha anthu ozimitsa moto.

Patatha zaka ziwiri, boma linatipatsa nyumba yaing’ono kudera lina kuti tizikhalamo. Koma anthu ambiri m’derali ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kumwa mowa mwauchidakwa, kuphwanya malamulo komanso kuchita uhule.

Tsiku lina amayi anga anakumana ndi bambo ena ndipo patapita nthawi anakwatirana. Bambo wondipezawa anali chidakwa chadzaoneni. Nthawi zina akaledzera ankawamenya amayi anga komanso ineyo. Nthawi zambiri ndikakhala ndekha ndinkalira ndipo ndinkalakalaka nditakhala ndi bambo woti azinditeteza.

Tinali osauka kwambiri ngakhale kuti amayi ankayesetsa kutipezera zofunika. Nthawi zambiri tinkangogonera tiyi. Kuti tisangalaleko, ineyo ndi mchimwene wanga tinkasuzumira pawindo la nyumba ya aneba n’kumaonera TV. Koma tsiku lina eniake anationa n’kutiletsa kuti tisadzasuzumirenso.

Bambo anga akakhala kuti sanaledzere ankatigulira chakudya. Komanso nthawi ina anatigulira TV yaing’ono. Ndimakumbukira kuti imeneyi ndi nthawi yomwe ndinasangalalako pa moyo wanga.

Ndili ndi zaka 12, ndinaphunzira kuwerenga. Chaka chotsatira ndinasiya sukulu ndipo ndinayamba kugwira ntchito. Ndikaweruka kuntchito, ine ndi anzanga tinkapita kukamwa mowa ndiponso kukasuta chamba. Pasanapite nthawi ndinayamba kumwa mowa kwambiri komanso kusuta chamba.

Ndili ndi zaka 20, ndinakumana ndi mtsikana wina, dzina lake Cati, ndipo kenako tinakwatirana. Poyamba zinthu zinkatiyendera bwino koma kenako ine ndinayambiranso khalidwe langa loipa. Pa nthawiyi, ndinkachita zoipa kwambiri kuposanso poyamba paja. Ndinazindikira kuti khalidwe langali linditengera kundende kapena kumanda. Vuto linanso linali lakuti ndinkachitira nkhanza mwana wanga, dzina lake Víctor, potengera zimene bambo anga ondipeza aja ankandichitira ndili mwana. Zimenezi zinkandikhumudwitsa kwambiri ndipo zinachititsa  kuti ndizidziona ngati munthu wosafunika.

M’chaka cha 2001, azimayi awiri a Mboni za Yehova anafika kunyumba kwathu ndipo anayamba kuphunzira Baibulo ndi Cati. Mkazi wangayu ankandifotokozera zimene ankaphunzira ndipo chifukwa chochita chidwi ndi zimenezo, nanenso ndiyamba kuphunzira Baibulo. M’chaka cha 2003, Cati anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Tsiku lina ndinawerenga lemba la Rute 2:12 limene limanena kuti Yehova amadalitsa anthu amene amasonyeza chikhulupiriro komanso amene amafuna kuti iye aziwateteza. Ndinazindikira kuti nditasintha khalidwe langa, Mulungu angasangalale kwambiri komanso angandidalitse. Ndinaonanso kuti Baibulo limaletsa kumwa mowa mwauchidakwa. Lemba linanso limene linandithandiza kwambiri ndi la 2 Akorinto 7:1 limene limatilimbikitsa kuti “tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa.” Choncho ndinayamba kusintha khalidwe langa loipa. Koma nditayamba kusintha, sindinkachedwa kupsa mtima komabe Cati ankandithandiza kwambiri.

Kenako ndinasiya ntchito chifukwa ndinaona kuti ndi imene inkandipangitsa kuti ndizisuta komanso kumwa mowa mwauchidakwa. Ngakhale kuti kusiya ntchito kunachititsa kuti ndizikhala ndi ndalama zochepa, kunandithandiza kuti ndizipeza nthawi yambiri yophunzira Baibulo. Ndimaona kuti nthawi imeneyi ndi pamene moyo wanga unasintha kwambiri. Mkazi wanga sankandivutitsa kuti ndizimugulira zinthu zomwe sindikanakwanitsa komanso sankandinyoza chifukwa choona kuti sindinkakwanitsa kugula zinthu zapamwamba. Ndimamuyamikira kwambiri chifukwa cha mtima umene anasonyezawu.

Pang’ono ndi pang’ono, ndinayamba kucheza kwambiri ndi a Mboni. Iwo anandithandiza kuzindikira kuti ngakhale kuti ndine wosaphunzira kwenikweni, Yehova amayamikira mtima wofuna kumutumikira umene ndili nawo. Banja lathu linaona kuti a Mboni za Yehova amakondana komanso kugwirizana, ndipo zimenezi zinatithandiza kwambiri. Tinali tisanaonepo anthu amtendere ngati amenewa. Mu December 2004, inenso ndinabatizidwa.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Ndaona kuti mawu a Yehova opezeka palemba la Yesaya 48:17 ndi oona. Lembali limati: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.” Mayi komanso mchimwene wanga uja anadabwa kwambiri ataona kuti ndasiya khalidwe langa loipa ndipo nawonso anayamba kuphunzira Baibulo. Ngakhale anthu a kudera lathu anasangalala ataona kuti ndasintha komanso ataona kuti banja lathu likusangalala.

Mkazi wanga amakonda kwambiri Mulungu komanso amandidalira. Iye amandiona kuti ndine mnzake wapamtima. Ngakhale kuti bambo anga sindiwadziwabe mpaka pano, Baibulo landiphunzitsa kulera bwino ana athu atatu. Iwo amandilemekeza kwambiri. Komanso chofunika kwambiri n’choti anawa amakonda kwambiri Yehova.

“Ngakhale kuti bambo anga sindiwadziwa, Baibulo landiphunzitsa kulera bwino ana athu atatu”

Ndimayamikira kwambiri kuti Yehova wandithandiza kukhala ndi moyo wosangalala ngakhale kuti ndinakula movutika kwambiri.

 “Ndinali munthu waukali komanso wosachedwa kupsa mtima.”​—NABIHA LAZAROVA

  • CHAKA CHOBADWA: 1974

  • DZIKO: BULGARIA

  • POYAMBA: NDINKAGULITSA MANKHWALA OSOKONEZA BONGO

KALE LANGA:

Ndinabadwira mumzinda wa Sofia m’dziko la Bulgaria ndipo banja lathu silinali lolemera kwenikweni. Ndili ndi zaka 6, bambo ndi mayi anga analekana ndipo bambo athuwo sankatisamaliranso. Zimenezi zinandikhumudwitsa kwambiri ndipo zinandisokoneza maganizo. Ndinkadziona kuti ndine wosafunika ndipo palibe amene angandikonde. Nditakula, maganizo amenewa anachititsa kuti ndipanduke. Ndinali munthu waukali komanso wosachedwa kupsa mtima.

Ndili ndi zaka 14, ndinachoka panyumba. Nthawi zambiri ndinkaba ndalama za mayi anga kapena za agogo. Khalidwe langa lopsa mtima linkachititsa kuti ndizipeza mavuto ambiri kusukulu moti pa zaka zochepa zokha ndinatumizidwa m’sukulu zoposa zisanu. Kutatsala zaka zitatu kuti ndilembe mayeso omaliza, ndinasiya sukulu ndipo ndinayamba kuchita zachiwerewere. Ndinayambanso kumwa mowa mwauchidakwa, kupita kumapate komanso kusuta kwambiri fodya ndi chamba. Kuwonjezera pamenepa ndinkagulitsanso mankhwala osokoneza bongo. Ndikaganizira mavuto amene ali padzikoli, ndinkaona kuti palibe chifukwa choti ndizichita zabwino. Choncho ndinkangochita zinthu zimene ndinkaona kuti zindisangalatsa patsikulo ndipo ndinkaona kuti zamawa, ndidzaziona mawa lomwelo.

M’chaka cha 1998, ndili ndi zaka 24, ndinamangidwa pabwalo la ndege mumzinda wa São Paulo ku Brazil, atandigwira ndi mankhwala osokoneza bongo. Zitatere, anandilamula kuti ndikhale m’ndende zaka zinayi.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Mu 2000, a Mboni za Yehova anayamba kumabwera kawiri pa mlungu kudzalalikira kundende yomwe ndinali. Mmodzi mwa a Mboniwa, dzina lake Marines, ankandikomera mtima kwambiri. Iye anachititsa kuti ndiganize zoyamba kuphunzira Baibulo. Koma popeza ndinali ndisanamvepo zokhudza Mboni za Yehova, ndinafunsa akaidi anzanga kuti andiuze zimene akudziwa zokhudza a Mboni. Ndinadabwa kuti zimene ambiri ananena zinasonyeza kuti ankadana ndi Mboni za Yehova. Mkaidi wina anandiuza kuti ndikhoza kuyamba chipembedzo chilichonse, koma osati cha Mboni za Yehova. Zimene ananenazi, zinachititsa kuti ndiyambe kufufuza kuti ndidziwe kuti n’chifukwa chiyani anthu ambiri amadana ndi a Mboni. Ndinapeza kuti n’chifukwa choti chipembedzo cha Mboni za Yehova ndi choona. Ndipotu Baibulo limanena kuti aliyense amene amayesetsa kutsatira Yesu, amazunzidwa.—2 Timoteyo 3:12.

Pa nthawi imeneyi, anandiuza kuti ndizigwira ntchito m’maofesi apandendepa. Tsiku lina ndikugwira ntchito m’chipinda chosungira zinthu, ndinapeza katoni yomwe munali magazini akale a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! * Ndinatenga magaziniwa ndipo nditabwerera kuchipinda chimene ndinkagona, ndinayamba kuwawerenga. Zimene ndinkawerenga m’magaziniwa, zinkandipangitsa kumva ngati munthu amene ali m’chipululu, ndipo wapeza chitsime cha madzi abwino. Popeza ndinkakhala ndi nthawi yambiri, tsiku lililonse ndinkawerenga Baibulo kwa nthawi yaitali.

 Tsiku lina, akuluakulu apandendepa anandiitana kuofesi kwawo. Ndinaganiza kuti mwina akufuna kunditulutsa, choncho ndinalongedza tikatundu tanga n’kutsanzika kwa anzanga. Koma nditafika kumeneko, anandiuza kuti andipezanso ndi mlandu wina wowerenga mabuku oletsedwa. Choncho anandiwonjezera zaka zina ziwiri zoti ndikhale m’ndende.

Nditangomva zimenezi ndinakhumudwa kwambiri. Koma patatha masiku angapo ndinazindikira kuti kukhala m’ndende zaka zina ziwiri kundithandiza. Ngakhale kuti ndinali nditaphunzira zinthu zambiri kuchokera m’Baibulo, ndinkaganizabe kuti ndikangotuluka kundende ndikapitiriza khalidwe langa lija. Choncho ndinaona kuti zaka ziwirizi zindithandiza kuti ndiphunzirebe zambiri.

Nthawi zina ndinkaganiza kuti Mulungu sangalole kuti ineyo ndizimulambira. Koma ndinkaganizira malemba monga la 1 Akorinto 6:9-11. Lemba limeneli limanena kuti m’nthawi ya atumwi, anthu ena asanakhale Akhristu, anali akuba, zidakwa, ndiponso olanda. Koma Yehova anawathandiza kuti asinthe. Chitsanzo chawochi chinandilimbikitsa kwambiri.

Sindinavutike kusiya makhalidwe ena oipa. Mwachitsanzo sizinandivute kwenikweni kusiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Koma zinali zovuta kwambiri kuti ndisiye kusuta fodya. Komabe ndinayesetsa kwa chaka chathunthu ndipo kenako ndinasiya kusuta. Kuganizira mmene fodya amawonongera thanzi la munthu n’kumene kunandithandiza kuti ndisinthe. Koma chomwe chinandithandizanso kwambiri ndi choti ndinkapemphera kwa Yehova nthawi zonse.

“Ndinazindikira kuti ndapeza Atate wabwino kwambiri yemwe sangandisiye”

Pamene ubwenzi wanga ndi Yehova unkakula, maganizo odziona ngati wosafunika aja, omwe anayamba bambo anga atatithawa, anayamba kuchepa. Mawu a palemba la Salimo 27:10 anandithandiza kwambiri. Lemba limeneli limati: “Ngakhale bambo anga ndi mayi anga atandisiya, Yehova adzanditenga.” Ndinazindikira kuti ndapeza Atate wabwino kwambiri yemwe sangandisiye. Tsopano ndinayamba kuona kuti moyo wanga uli ndi phindu. Mu April 2004, patatha miyezi 6 kuchokera pamene ndinatuluka m’ndende, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Panopa ndine munthu wosangalala kwambiri. Ndinasiya makhalidwe onse amene ankawononga thanzi langa ndipo ndili ndi thanzi labwino kuposa kale. Tsopano ndili ndi banja losangalala komanso ndili pa ubwenzi wabwino ndi Atate wanga wakumwamba, Yehova. M’gulu la anthu ake, ndapezamo atate, amayi, abale komanso alongo. (Maliko 10:29, 30) Ndikuyamikira kwambiri kuti anthu amenewa anaona kuti ndingathe kukhala mtumiki wa Yehova ngakhale kuti ineyo pa nthawiyo sindinkadziwa kuti zimenezi zingatheke.

Nthawi zina ndimakhumudwa ndikaganizira zimene ndinkachita poyamba. Koma ndimalimbikitsidwa chifukwa chodziwa kuti m’dziko latsopano, zoipa zimene tinachita tisanayambe kutumikira Mulungu, “sizidzakumbukiridwanso.” (Yesaya 65:17) Panopa, zimene ndinkachita poyamba zimandithandiza kuti ndizimvera chisoni anthu amene akuchita zimenezi. Mwachitsanzo ndikamalalikira kunyumba ndi nyumba, ndimalalikira mosavuta anthu omwe amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, amene amamwa mowa mwauchidakwa komanso anthu ophwanya malamulo. Ndimaona kuti anthu amenewanso amafunika kumva uthenga wabwino. Ndimakhulupirira kuti ngati ineyo ndinasintha n’kuyamba kutumikira Yehova, nawonso akhoza kusintha.

^ ndime 29 Magazini amenewa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.