Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Amafuna Kuti Akazi Azilemekezedwa

Mulungu Amafuna Kuti Akazi Azilemekezedwa

ALI padziko lapansi, Yesu anasonyeza bwino makhalidwe a Atate ake komanso mmene amachitira zinthu. Iye anati: “Sindichita kanthu mongoganiza ndekha. Koma ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira. . . . Ndimachita zinthu zomukondweretsa nthawi zonse.” (Yohane 8:28, 29; Akolose 1:15) Choncho, tingadziwe mmene Mulungu amaonera akazi tikaphunzira ndi kumvetsa bwino mmene Yesu ankachitira zinthu ndi akazi, komanso mmene ankawaonera.

Kuchokera pa zimene zinalembedwa m’Mauthenga Abwino, akatswiri ambiri amaphunziro amavomereza kuti Yesu ankaona akazi mosiyana kwambiri ndi mmene anthu ena pa nthawiyo ankawaonera. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu ankalemekeza akazi? Kodi zimene Yesu ankaphunzitsa zimathandizanso masiku ano kuti akazi azilemekezedwa?

Mmene Yesu Ankaonera Akazi

Yesu sankaona kuti akazi analengedwa n’cholinga choti amuna azigona nawo basi. Atsogoleri ena achipembedzo achiyuda ankaona kuti kuchita zinthu ndi akazi kungapangitse kuti munthu achite chiwerewere. Chifukwa cha zimenezi akazi sankaloledwa kulankhula ndi amuna pagulu komanso  sankaloledwa kuyenda osaphimba kumutu. Koma Yesu analangiza amuna kuti azilemekeza akazi ndipo asamawasale koma kuti amunawo azidziletsa.​—Mateyu 5:28.

Yesu ananenanso kuti: “Aliyense wosiya mkazi wake ndi kukwatira wina, wachita chigololo molakwira mkaziyo.” (Maliko 10:11, 12) Choncho iye anatsutsa zimene Arabi ankaphunzitsa kuti amuna azisiya akazi awo “pa chifukwa chilichonse.” (Mateyu 19:3, 9) Mfundo yoti mwamuna akachita chigololo amalakwira mkazi wake inali yachilendo kwa Ayuda ambiri. Arabi ankawaphunzitsa kuti mwamuna akachita chigololo sanalakwire mkazi wake. Koma mkazi akachita chigololo ndi amene ankaonedwa kuti ndi wosakhulupirika. Katswiri wina wa Baibulo ananena kuti: “Pamene Yesu ananena kuti mwamuna akachita chigololo nayenso walakwira mkazi wake, anasonyeza kuti nawonso akazi ndi ofunika.”

Mmene mfundoyi imathandizira masiku ano: Mumpingo wa Mboni za Yehova, akazi amakhala momasuka ndi amuna pamisonkhano. Komabe, iwo amaonetsetsa kuti pakati pawo sipakuchitika zinthu zosayenera kapena kuzolowerana mopambanitsa chifukwa amuna achikhristu amaona ‘akazi achikulire ngati amayi awo, akazi achitsikana ngati alongo awo ndipo sakhala ndi maganizo alionse oipa.’​1 Timoteyo 5:2.

Yesu ankaphunzitsanso akazi. Arabi ankaona kuti akazi ndi osayenera kuwaphunzitsa. Koma mosiyana ndi zimenezi, Yesu ankawaphunzitsa komanso ankawalimbikitsa kunena momasuka maganizo awo. Yesu sanalepheretse Mariya kukhala ndi mwayi womvetsera pamene iyeyo ankaphunzitsa, ndipo pamenepa anasonyeza kuti ntchito ya akazi si kuphika basi. (Luka 10:38-42) Malita, mchemwali wake wa Mariya, nayenso anapindula ndi zimene Yesu ankaphunzitsa, ndipo umboni wa zimenezi ndi zomwe iye anayankha Yesu, Lazaro atamwalira.​—Yohane 11:21-27.

Yesu ankachitanso chidwi ndi zimene akazi amaganiza pa nkhani zosiyanasiyana. Pa nthawi imeneyo, akazi ambiri achiyuda ankakhulupirira kuti munthu amakhala wosangalala akakhala ndi mwana wamwamuna wotchuka, apo ayi mneneri. Pa nthawi ina mayi wina atafuula kuti: “Ndi wodala mayi amene mimba yake inanyamula inu,” Yesu anamuuza mfundo ina yosonyeza kuti maganizo amenewa ndi olakwika. (Luka 11:27, 28) Zimene Yesu anauza mayiyu zikusonyeza kuti kumvera Mulungu ndiye kofunika kwambiri kuposa kutchuka.​—Yohane 8:32.

Mmene mfundoyi imathandizira masiku ano: Akulu mumpingo wachikhristu amalola kuti akazi aziyankha momasuka pamisonkhano. Iwo amayamikira akazi okonda zinthu zauzimu chifukwa chokhala “aphunzitsi a zinthu zabwino” pa zochita zawo zonse. (Tito 2:3) Akazi ndi odalirikanso kwambiri pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.​—Salimo 68:11; onani bokosi lakuti,  “Kodi Mtumwi Paulo Analetsa Akazi Kulankhula?” patsamba 9.

Yesu sankaona kuti akazi ndi otsika. Kale, ana  aakazi ankaonedwa kuti ndi otsika poyerekeza ndi ana aamuna. Mu Talmud muli mawu awa osonyeza kuti anthu ambiri analidi ndi maganizo amenewa: “Wodala ndi munthu amene ali ndi ana aamuna, koma tsoka kwa iye amene ali ndi ana aakazi.” Makolo ena ankaona kuti kukhala ndi mwana wamkazi ndi chintchito chifukwa ankayenera kumupezera mwamuna, kumuperekera malowolo komanso ankaona kuti mwana wamkaziyo sadzawathandiza akadzakalamba.

Yesu anasonyeza kuti palibe kusiyana pakati pa mwana wamkazi ndi wamwamuna. Iye anachita zimenezi poukitsa mwana wamkazi wa Yairo monganso anachitira poukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye wa ku Nayini. (Maliko 5:35, 41, 42; Luka 7:11-15) Yesu atachiritsa mayi wina “amene mzimu woipa unamudwalitsa zaka 18,” anamutchula kuti “mwana wa Abulahamu.” Zimene Yesu anachitazi, potchula mkaziyu kuti “mwana wa Abulahamu,” zinali zachilendo kwa Ayuda. (Luka 13:10-16) Pomutchula mayiyo ndi mawu olemekeza amenewa, Yesu anazindikira kuti mayiyu anali ndi chikhulupiriro cholimba ndipo sanali wotsika poyerekezera ndi amuna.​—Luka 19:9; Agalatiya 3:7.

Mmene mfundoyi imathandizira masiku ano: Ku Asia kuli mwambi wakuti: “Kulera mwana wamkazi n’kopanda phindu chifukwa kuli ngati kuthirira dimba la munthu wina.” Koma makolo achikhristu sakhala ndi maganizo amenewa ndipo iwo amasamalira ana awo, aamuna ndi aakazi, mofanana. Iwo amaonetsetsa kuti ana awo onse akusamalidwa mofanana pa nkhani ya maphunziro ndi thandizo lachipatala.

Yesu ankaona kuti akazi nawonso ndi odalirika. M’khoti la Ayuda, umboni wa mkazi unkaonedwa mofanana ndi wa kapolo. Wolemba mbiri wina wa m’nthawi ya atumwi, dzina lake Josephus, analangiza anthu kuti: “Musamagwiritse ntchito umboni wa akazi chifukwa ndi achibwanabwana.”

Mosiyana ndi zimenezi, Yesu atangoukitsidwa anaonekera kwa akazi ndipo anawauza kuti akauze anthu za kuuka kwake. (Mateyu 28:1, 8-10) Ngakhale kuti akazi okhulupirika amenewa anali mboni zoona ndi maso kuphedwa ndiponso kuikidwa m’manda kwa Ambuye wawo, atumwi zinawavuta kukhulupirira kuti zimene akaziwa ankanena zinali zoona. (Mateyu 27:55, 56, 61; Luka 24:10, 11) Komabe poonekera choyamba kwa akazi, Khristu anasonyeza kuti akazi ndi ofunikanso pa nkhani yochitira umboni mofanana ndi amuna.​—Machitidwe 1:8, 14.

Mmene mfundoyi imathandizira masiku ano: M’mipingo ya Mboni za Yehova, akulu amasonyeza kuti saona kuti akazi ndi otsika. Iwo amachita zimenezi pogwiritsa ntchito zimene akaziwo amanena.  Komanso amuna achikhristu ‘amapatsa ulemu’ akazi awo mwa kumvetsera zimene akunena.​—1 Petulo 3:7; Genesis 21:12.

Mfundo za M’Baibulo Zimathandiza Akazi Kukhala Osangalala

Amuna akamatengera chitsanzo cha Khristu, amalemekeza akazi awo komanso kuwapatsa ufulu ngati mmene Mulungu anafunira poyamba. (Genesis 1:27, 28) M’malo motsatira maganizo oti amuna ndi apamwamba kuposa akazi, amuna achikhristu amatsatira mfundo za m’Baibulo. Zimenezi zimathandiza kuti akazi awo azikhala osangalala m’banja.​—Aefeso 5:28, 29.

Pa nthawi imene mayi wina, dzina lake Yelena, ankayamba kuphunzira Baibulo n’kuti mwamuna wake akumuchitira nkhanza. Komanso iye anakulira m’dera limene amuna ankakonda kuba akazi kuti akakhale akazi awo ndiponso kuchitira nkhanza akazi kunali ponseponse. Yelena ananena kuti: “Zimene ndinaphunzira m’Baibulo zinandithandiza kwambiri. Ndinayamba kuona kuti Mulungu amandikonda kwambiri komanso amandiona kuti ndine wofunika. Ndinaonanso kuti ngati mwamuna wanga atayamba kuphunzira Baibulo angayambe kundikonda.” Patapita nthawi mwamuna wake anayambadi kuphunzira Baibulo ndipo kenako anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Yelena ananenanso kuti: “Mwamuna wanga anasiya kundichitira nkhanza ndipo tinaphunzira kukhululukirana.” Pomalizira pake Yelena anati: “Mfundo za m’Baibulo zandithandiza kwambiri kuti ndiziona kuti ndine wofunika komanso wotetezeka m’banja.”​—Akolose 3:13, 18, 19.

Pali mabanja ambiri amene apindula chifukwa chophunzira Baibulo. Akazi ambirimbiri akusangalala m’banja chifukwa choti iwo ndi amuna awo akuyesetsa kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo m’banja mwawo. Akazi oterewa amalemekezedwa, kulimbikitsidwa komanso amakhala omasuka kucheza ndi Akhristu anzawo.​—Yohane 13:34, 35.

Amuna ndi akazi achikhristu amazindikira kuti onse ndi ochimwa ndipo ndi opanda ungwiro. Iwo amadziwanso kuti ali mbali ya chilengedwe chimene “chinaperekedwa ku mkhalidwe wopanda pake.” Komabe amazindikiranso kuti kukhala pa ubwenzi ndi Atate wawo, Yehova Mulungu, kumawathandiza kukhala ndi chiyembekezo choti ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.’ Chimenechitu ndi chiyembekezo chosangalatsa kwambiri kwa amuna ndi akazi omwe, amene onse Mulungu amawakonda.​—Aroma 8:20, 21.