Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

Kodi Tizikumbukira Bwanji Imfa ya Yesu?

Kodi Tizikumbukira Bwanji Imfa ya Yesu?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi imfa ya Yesu iyenera kukumbukiridwa motani?

Yesu anauza otsatira ake kuti azikumbukira imfa yake pogwiritsa ntchito mkate ndi vinyo. Mkatewo umaimira thupi la Yesu ndipo vinyo amaimira magazi ake.​—Werengani Luka 22:19, 20.

Mkate umene Yesu anagwiritsa ntchito unali wopanda chofufumitsa kapena kuti wopanda yisiti. Nthawi zambiri m’Baibulo, yisiti amaimira uchimo. Choncho mkate wopanda chofufumitsa unali chizindikiro choyenera cha thupi langwiro la Yesu limene iye anapereka ngati nsembe. Nsembe imeneyi inathetsa nsembe za nyama zimene zinkaperekedwa potsatira Chilamulo cha Mose. (Aheberi 10:5, 9, 10) Vinyo amaimira magazi amtengo wapatali a Yesu amene anakhetsedwa monga nsembe ya machimo athu.​—Werengani 1 Petulo 1:19; 2:24; 3:18.

2. Kodi imfa ya Yesu iyenera kukumbukiridwa liti?

Yesu anaphedwa pa Nisani 14, lomwe linali tsiku la Pasika. Malinga ndi kalendala yachiyuda, tsiku limayamba dzuwa litalowa. Madzulo a tsiku limene anaphedwalo, Yesu anachita mwambo wa Pasika ndi ophunzira ake ndipo kenako anayambitsa mwambo watsopano wokumbukira imfa yake.​—Werengani Luka 22:14, 15.

Masiku ano, anthu a Mulungu amakumbukira zimene Mulungu anachita kudzera mwa Yesu pomasula mtundu wonse wa anthu ku uchimo ndi imfa. (Ekisodo 12:5-7, 13, 17) Mwambo wa Pasika unkachitika kamodzi pa chaka. Nawonso mwambo wokumbukira imfa ya Yesu umachitika kamodzi pa chaka. Mwambowu umachitika pa Nisani 14 dzuwa litalowa, malinga ndi kalendala ya m’Baibulo yotsatira tsiku limene mwezi waoneka.​—Werengani Yohane 1:29.

  3. Kodi ndani ayenera kudya mkate ndi kumwa vinyo?

Yesu atapereka vinyo kwa otsatira ake, anati: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano.” (1 Akorinto 11:25) Pangano latsopanoli linalowa m’malo mwa pangano la Chilamulo cha Mose limene Mulungu anachita ndi Aisiraeli. M’panganoli, Mulungu analonjeza Aisiraeli kuti ngati adzamvera mawu ake onse, adzakhala anthu ake. (Ekisodo 19:5, 6) Koma Aisiraeli sanamvere Mulungu. Choncho Yehova anakhazikitsa pangano latsopano.​—Werengani Yeremiya 31:31.

Kudzera m’pangano latsopanoli, Yehova anakonza zoti anthu ambiri adzapeze madalitso kudzera mwa anthu ochepa. Anthu amene ali m’pangano latsopanoli ndi okwana 144,000 basi. Kudzera mwa anthu amenewa, anthu mamiliyoni ambiri adzadalitsidwa ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Pakali pano, ena mwa anthu amene ali m’pangano latsopanoli adakatumikira Yehova padziko lapansi. Anthu amenewa okha ndi amene ayenera kudya mkate ndi kumwa vinyo chifukwa iwowa ndi amene ali m’pangano latsopanoli.​—Werengani Luka 12:32; Chivumbulutso 14:1, 3.

4. Kodi kukumbukira imfa ya Yesu kumatipindulitsa bwanji?

Mwambo wokumbukira imfa ya Yesu umene umachitika chaka chilichonse, umatithandiza kuti tiziyamikira kwambiri chikondi chachikulu chimene Yehova anatisonyeza. Iye anatumiza Mwana wake kuti adzatifere chifukwa cha machimo athu. Choncho, pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu, tiyenera kuganizira zimene imfa yake imatanthauza kwa ife. Tiyenera kuganiziranso zimene tingachite posonyeza kuyamikira zimene Yehova ndi Yesu anatichitira.​—Werengani Yohane 3:16; 2 Akorinto 5:14, 15.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri, werengani tsamba 206-208 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.