Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Ine Ndachititsa Kuti Adziwe Dzina Lanu’

‘Ine Ndachititsa Kuti Adziwe Dzina Lanu’

 ‘Ine Ndachititsa Kuti Adziwe Dzina Lanu’

“Anthu amene munawatenga m’dziko ndi kundipatsa ine ndawadziwitsa dzina lanu. . . . Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa.”​—YOHANE 17:6, 26.

Kodi Mawu Amenewa Amatanthauza Chiyani? Yesu ankagwiritsa ntchito dzina la Mulungu pa utumiki wake ndipo zimenezi zinathandiza kuti anthu alidziwe. Nthawi zambiri, Yesu ankawerenga Malemba ndipo akamachita zimenezi ankatchula dzina la Mulungu. (Luka 4:16-21) Komanso iye anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Atate, dzina lanu liyeretsedwe.”​—Luka 11:2.

Mmene Akhristu Oyambirira Ankachitira Zimenezi: Mtumwi Petulo anauza amuna aakulu a ku Yerusalemu kuti Mulungu anali atatenga anthu a mitundu ina kuti akhale “anthu odziwika ndi dzina lake.” (Machitidwe 15:14) Komanso atumwi ndi anthu ena ankalalikira kuti “aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Machitidwe 2:21; Aroma 10:13) Iwo ankagwiritsanso ntchito dzina la Mulungu m’zolemba zawo. Buku lina la malamulo a Ayuda lomwe anamaliza kulilemba cha m’ma 300 C.E., lotchedwa Tosefta, limanena mawu otsatirawa pofotokoza za mabuku a Akhristu omwe ankawotchedwa ndi anthu otsutsa Chikhristu: “Mabuku a anthu olengeza Uthenga Wabwino ndiponso mabuku a anthu otchedwa Aminimu [anthu ena amaganiza kuti anthu amenewa anali Akhristu achiyuda] ankawotchedwa ndi moto. Koma ankawawotchera pamalo amene awapezerapo ndipo ankawasiya mpaka anyekere pompo. . . . moti mabuku onsewo pamodzi ndi masamba onse otchula Dzina la Mulungu ankapsera limodzi.”

Ndani Akuchita Zimenezi Masiku Ano? Mawu oyamba a m’Baibulo la Revised Standard Version lomwe linavomerezedwa ndi bungwe lina lachipembedzo la ku United States (National Council of the Churches of Christ) amanena kuti: “Kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu, yemwe alipo mmodzi yekha, kumachititsa kuti zizioneka ngati pali milungu ina ndipo mukufuna kusiyanitsa Mulungu ndi milungu inayo. Choncho Ayuda anasiya kuchita zimenezi Chikhristu chisanayambe ndipo kugwiritsa ntchito dzinali n’kosayenera pa chikhulupiriro cha anthu onse amene ali mumpingo wachikhristu.” Motero, m’Baibuloli anachotsamo dzina la Mulungu n’kuikamo mawu akuti “AMBUYE.” Posachedwapa akuluakulu a Tchalitchi cha Katolika ku Vatican analamula mabishopu a tchalitchichi kuti: “Dzina la Mulungu lolembedwa pogwiritsa ntchito zilembo zinayi za YHWH * lisamagwiritsidwenso ntchito kapena kutchulidwa poimba nyimbo ndiponso popemphera.”

Kodi ndani masiku ano amene amagwiritsa ntchito dzina la Mulungu komanso kudziwitsa anthu dzinali? Munthu wina wa ku Kyrgyzstan, dzina lake Sergey, ali mnyamata, anaonera filimu ina imene inanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Iye ataonera filimuyi panatha zaka 10 asanamvenso dzinali. Kenako, Sergey atasamukira ku United States, anthu awiri a Mboni za Yehova anabwera kunyumba kwawo ndipo anamusonyeza dzina la Mulungu kuchokera m’Baibulo. Sergey anasangalala kupeza gulu la anthu amene amagwiritsa ntchito dzina lakuti Yehova. Chochititsa chidwi n’chakuti dikishonale ina potanthauzira mawu akuti “Yehova Mulungu,” inanena kuti “Mulungu yekhayo amene Mboni za Yehova zimalambira ndi kuvomereza kuti ndiye Mulungu woona.”​—Webster’s Third New International Dictionary.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 M’Chichewa, dzina la Mulungu limamasuliridwa kuti “Yehova.”