Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Dziko Lapansili Lidzawonongedwa?

Kodi Dziko Lapansili Lidzawonongedwa?

▪ Anthu ena ankaganiza kuti dziko litha pa 21 October, 2011 koma silinathe. Izi zinasonyeza kuti zomwe analosera munthu wina, dzina lake Harold Camping, yemwe ndi woulutsa mawu pa wailesi ina ku United States, sizinakwaniritsidwe. Iye ankanena kuti pa 21 May 2011, lidzakhala Tsiku la Chiweruzo ndipo kudzachitika chivomezi choopsa padziko lonse lapansi kenako pakadzatha miyezi isanu, pa 21 October, dziko lonseli lidzawonongedwa.

Komatu dziko lapansili silidzawonongedwa. Mlengi wa dzikoli sangalole kuti zimenezi zichitike. Mawu ake amati: “Mwakhazikitsa mwamphamvu dziko lapansi, kuti lisagwedezeke.”​—Salimo 119:90.

Koma anthu ena owerenga Baibulo amatsutsa mfundo imeneyi ndipo amanena kuti dzikoli lidzawonongedwa ndi moto. Iwo amaganiza choncho potengera zimene zili palemba la 2 Petulo 3:7, 10, lomwe limati: “Mwa mawu amodzimodziwo, kumwamba kumene kulipo panopa limodzi ndi dziko lapansi, azisungira moto m’tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu. . . . Komabe, tsiku la Yehova lidzafika ngati mbala, pamene kumwamba kudzachoka ndi mkokomo waukulu, koma zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri n’kusungunuka, ndipo dziko lapansi ndi ntchito zake zidzaonekera poyera.” Kodi mawu a mtumwi Petulo amenewa akutanthauza chiyani kwenikweni?

Mawu amene Petulo anagwiritsa ntchito palembali ndi ophiphiritsira. Kuti timvetse mfundo ya palembali tiyenera kuliyerekezera ndi zimene Petulo ankafotokoza m’kalatayi komanso ndi nkhani zina za m’Baibulo. Zitakhala kuti mawu a palembali si ophiphiritsa, zingatanthauze kuti kumwamba, komwe kuli nyenyezi ndiponso zinthu zina mabiliyoni ambirimbiri, komanso dziko lapansili zidzawonongedwa ndi moto. Zimenezi sizingakhale zomveka. Mulungu sangawononge zinthu zonsezi chifukwa cha anthu oipa amene ali padziko lapansili, lomwe ndi laling’ono kwambiri poliyerekezera ndi chilengedwe chonse. Kodi inuyo mungawononge mchenga wonse wa m’mbali mwa nyanja chifukwa choti kamchenga kamodzi kokha sikanakusangalatseni? N’zodziwikiratu kuti simungatero. Yehovanso sangawononge zinthu zonse zimene analenga chabe chifukwa chakuti dziko lapansi lili ndi anthu oipa.

Komanso, kuganiza kuti Mulungu angawononge dziko lapansili, n’kosemphana ndi zimene Yesu Khristu ananena. Iye anati: “Odala ndi anthu amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5; Salimo 37:29) Kodi bambo wachikondi angamangire banja lake nyumba yabwino kenako n’kuiwotcha? (Salimo 115:16) Palibe bambo amene angachite zimenezi. Yehovanso sangawononge dzikoli chifukwa iye ndi Mlengi komanso Tate wachikondi.​—Salimo 103:13; 1 Yohane 4:8.

Petulo anagwiritsa ntchito mawu akuti “dziko lapansi” potanthauza anthu ndipo kwenikweni ankanena za anthu oipa. Komanso onani kuti Petulo anayerekezera dziko limeneli ndi dziko limene linalipo m’masiku a Chigumula cha Nowa. (2 Petulo 3:5, 6) Pa chigumula chimenechi, anthu oipa okha ndi amene anawonongedwa, koma dziko lenilenili komanso Nowa ndi banja lake anapulumuka. Mawu akuti “kumwamba” amene Petulo anagwiritsa ntchito, nawonso ndi ophiphiritsira. Mawu amenewa akutanthauza maboma amene akulamulira anthu oipa. Choncho, anthu oipa omwe safuna kusintha, limodzi ndi maboma amene akuwalamulira, adzawonongedwa ndipo Ufumu wa Mulungu ndi umene udzayambe kulamulira.​—Danieli 2:44.

Ndiyeno kodi dziko lapansili lidzawonongedwa? Ayi silidzawonongedwa. Chomwe chidzawonongedwe ndi dziko lophiphiritsira, lomwe ndi anthu oipa. Koma dziko lapansili lidzakhalapo mpaka kalekale. Nawonso anthu abwino amene azidzakhala m’dzikoli, adzakhala mpaka kalekale.​—Miyambo 2:21, 22.