Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mayankho A Mafunso 10 Okhudza Kugonana

Mayankho A Mafunso 10 Okhudza Kugonana

 Mayankho A Mafunso 10 Okhudza Kugonana

1 Kodi tchimo loyamba limene Adamu ndi Hava anachita m’munda wa Edeni linali kugonana?

▪ Yankho: Anthu ambiri amaganiza kuti chipatso choletsedwa chimene Adamu ndi Hava anadya m’munda wa Edeni chinkaphiphiritsira kugonana. Komatu zimenezi si zimene Baibulo limaphunzitsa.

Taganizirani mfundo izi: Hava asanalengedwe, Mulungu anali atalamula kale Adamu kuti asadye chipatso cha “mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.” (Genesis 2:15-18) Popeza pa nthawiyi n’kuti Adamu ali yekha, ndiye kuti lamulo limeneli silinkanena za kugonana. Komanso Mulungu anauza Adamu ndi Hava lamulo lomveka bwino lakuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Kodi Mulungu, yemwe ndi wachikondi, akanalamula banjali kuti ‘lidzaze dziko lapansi,’ zomwe zinkafunikira kuti azigonana, kenako n’kuwapha chifukwa chomvera lamulolo?​—1 Yohane 4:8.

Kuwonjezera pamenepo, pamene Hava anali yekha popanda mwamuna wake m’pamene “anathyola chipatso cha mtengowo [woletsedwa] n’kudya. Pambuyo pake, anapatsako mwamuna wake pamene anali limodzi, ndipo nayenso anadya.”​—Genesis 3:6.

Komanso, Mulungu sanadzudzule Adamu ndi Hava pamene anagonana n’kubereka ana. (Genesis 4:1, 2) Ndiyetu apa n’zoonekeratu kuti chipatso chimene Adamu ndi Hava anadya sichiimira kuti iwo anagonana koma ndi chipatso chenicheni chimene anathyola mumtengo.

2 Kodi Baibulo limaletsa kugonana n’cholinga chongofuna kusangalala?

▪ Yankho: Buku loyambirira la m’Baibulo limanena kuti Mulungu ndi amene analenga “mwamuna ndi mkazi.” Ndipo iye ananena kuti zimene analenga “zinali zabwino kwambiri.” (Genesis 1:27, 31) Kenako Mulungu anauzira munthu wina amene analemba nawo Baibulo kupereka malangizo awa kwa amuna: “Usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako. . . . Mabere ake akukhutiritse nthawi zonse.” (Miyambo 5:18, 19) Kodi mawu amenewa akusonyeza kuti Baibulo limaletsa kugonana n’cholinga chongofuna kusangalala?

Umboni ukusonyeza kuti, kuwonjezera pa mfundo yoti Mulungu  analenga mwamuna ndi mkazi m’njira yoti azitha kubereka ana, iye anawalenganso m’njira yoti azitha kusonyezana chikondi moti onse awiri azisangalala. Zimenezi zimathandiza kuti mwamuna ndi mkazi wake omwe amakondana kwambiri azikhala osangalala pa moyo wawo.

3 Kdi Baibulo limavomereza zoti mwamuna ndi mkazi yemwe sanakwatirane motsatira malamulo azikhalira limodzi?

▪ Yankho: Baibulo limanena momveka bwino kuti “Mulungu adzaweruza adama.” (Aheberi 13:4) Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti dama (por·neiʹa) amatanthauza kugonana kwa mtundu wina uliwonse kwa anthu omwe si okwatirana. * Choncho, Mulungu amaona kuti n’kulakwa kuti mwamuna ndi mkazi yemwe sanakwatirane azikhalira limodzi, ngakhale iwo atakhala ndi maganizo oti adzakwatirana.

Ngakhale mwamuna ndi mkazi atakhala kuti amakondana kwambiri, Mulungu amafuna kuti akwatirane kaye motsatira malamulo asanayambe kugonana. Mulungu ndi amene anatilenga m’njira yoti tizikondana. Ndipotu khalidwe lalikulu la Mulungu ndi chikondi. Choncho, monga nkhani yotsatira ikusonyezera, pali chifukwa chabwino chimene Mulungu amanenera kuti anthu okwatirana okha ndi amene ayenera kugonana.

4 Kodi Mulungu amalola kukwatira mitala?

▪ Yankho: Pa nthawi ina, Mulungu ankalola mwamuna kukwatira akazi angapo. (Genesis 4:19; 16:1-4; 29:18–30:24) Koma poyambirira penipeni Mulungu sanakonze zoti mwamuna azikwatira mitala. Iye anapatsa Adamu mkazi mmodzi yekha.

Mulungu anapatsa Yesu Khristu mphamvu zoti abwezeretsenso lamulo Lake loti mwamuna azikwatira mkazi mmodzi yekha. (Yohane 8:28) Anthu atafunsa Yesu za ukwati, iye anayankha kuti: “Amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi n’kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’”​—Mateyu 19:4, 5.

Kenako wophunzira wina wa Yesu anauziridwa ndi Mulungu kulemba kuti: “Mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.” (1 Akorinto 7:2)  Baibulo limanenanso kuti mwamuna aliyense amene angapatsidwe udindo wapadera mumpingo wachikhristu ayenera kukhala “mwamuna wa mkazi mmodzi.”​—1 Timoteyo 3:2, 12.

5 Kodi n’kulakwa kugwiritsa ntchito njira zolera m’banja?

▪ Yankho: Yesu sanalamule ophunzira ake kuti azibereka kapena asamabereke ana. Komanso palibe mtumwi aliyense wa Yesu amene anapereka malangizo amenewo. Palibenso vesi lililonse m’Baibulo limene limaletsa kugwiritsa ntchito njira zolera.

Choncho mwamuna ndi mkazi wake ali ndi ufulu wosankha ngati akufuna kukhala ndi ana kapena ayi. Angasankhenso kuti akufuna kukhala ndi ana angati komanso akufuna kukhala nawo pa nthawi iti. Njira zolera zimene sizichotsa mimba sizitsutsana ndi mfundo za m’Baibulo. Choncho, ngati mwamuna ndi mkazi wake akufuna kugwiritsa ntchito njira zimenezi, chimenecho ndi chosankha chawo. * Munthu aliyense sayenera kuwaona ngati olakwa chifukwa choti asankha kugwiritsa ntchito njira zolera.​—Aroma 14:4, 10-13.

6 Kodi kuchotsa mimba n’kulakwa?

▪ Yankho: Mulungu amaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali ndipo amaonanso kuti mwana amene wangoyambika kumene m’mimba mwa mayi ake ndi munthu. (Salimo 139:16) Mulungu ananena kuti munthu akapha mwana wosabadwa aziimbidwa mlandu. Choncho Mulungu amaona kuti kupha mwana wosabadwa, n’chimodzimodzi ndi kupha munthu.​—Ekisodo 20:13; 21:22, 23.

Nangano kodi mwamuna ndi mkazi wake angatani ngati pa nthawi yobereka, zikuoneka kuti mayi akakhala ndi moyo mwana afa, kapena mwana akakhala ndi moyo mayi afa? Zikatere, iwo ayenera kusankha kuti apulumutsa moyo wa ndani. *

7 Kodi Baibulo limalola kuthetsa ukwati?

▪ Yankho: Baibulo limanena kuti ukwati ukhoza kutha. Komabe Yesu ananena kuti pali chinthu chimodzi chokha chimene chingachititse kuti ukwati uthe. Iye anati: “Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama [kugonana ndi munthu woti sunakwatirane naye].”​—Mateyu 19:9.

Mulungu amadana ndi anthu amene amathetsa banja mwachinyengo. Iye adzaimba mlandu anthu onse amene amasiya akazi kapena  amuna awo popanda chifukwa chomveka, makamaka amene amachita zimenezi n’cholinga chakuti akwatirane ndi wina.​—Malaki 2:13-16; Maliko 10:9.

8 Kodi Mulungu amavomereza kuti amuna kapena akazi azigonana okhaokha?

▪ Yankho: Baibulo limaletsa dama ndipo zimenezi zikuphatikizapo kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. (Aroma 1:26, 27; Agalatiya 5:19-21) Baibulo limanena momveka bwino kuti Mulungu amadana ndi khalidwe limeneli. Komabe, tikudziwanso kuti “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”​—Yohane 3:16.

Choncho, ngakhale kuti Akhristu oona amadana ndi khalidwe logonana amuna kapena akazi okhaokha, iwo amasonyeza kukoma mtima kwa anthu onse. (Mateyu 7:12) Mulungu amafuna kuti ‘tizilemekeza anthu, kaya akhale amtundu wotani.’ Motero, Akhristu oona sasala anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha.​—1 Petulo 2:17.

9 Kodi kutumizirana zithunzi ndiponso mauthenga okhudza kugonana pa foni za m’manja kapena pa Intaneti n’kulakwa?

▪ Yankho: Baibulo silitchula mwachindunji zinthu zimenezi, zimene zikuchitika masiku ano. Komabe limanena kuti: “Dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe n’komwe pakati panu, monga mmene anthu oyera amayenera kuchitira. Musatchule ngakhale za khalidwe lochititsa manyazi, nkhani zopusa kapena nthabwala zotukwana, zomwe ndi zinthu zosayenera.” (Aefeso 5:3, 4) Kutumizirana zithunzi ndiponso mauthenga okhudza kugonana pa foni za m’manja kapena pa Intaneti, kumapangitsa kuti anthu azikhala ndi maganizo olakwika pa nkhani zokhudza kugonana komanso kumachititsa kuti azigonana ndi anthu amene sanakwatirane nawo. M’malo mothandiza kuti anthu akhale odziletsa, zinthu zimenezi zimapangitsa anthu kukhala ndi mtima wongofuna kudzisangalatsa.

10 Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani yoseweretsa maliseche n’cholinga chofuna kuthetsa chilakolako chogonana?

▪ Yankho: Baibulo silitchula mwachindunji chizolowezi chimenechi. Komabe Mawu a Mulungu amalamula Akhristu kuti: “Chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, [ndi] chilakolako [choipa] cha kugonana.”​—Akolose 3:5.

Munthu amene ali ndi chizolowezi choseweretsa maliseche saona kugonana moyenera ndipo amangofuna kukhutiritsa chilakolako chake. Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu akhoza kuthandiza anthu amene akuyesetsa kuti asiye chizolowezi chimenechi mwa kuwapatsa “mphamvu yoposa yachibadwa.”​—2 Akorinto 4:7; Afilipi 4:13.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Mawu akuti por·neiʹa, angatanthauzenso chigololo, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha komanso kugona nyama. Zinthu zimenezi n’zosagwirizana ndi cholinga cha Mulungu polenga anthu.

^ ndime 19 Kuti mudziwe zambiri pa zimene Baibulo limanena pa nkhani ya njira yolera yotseketsa, onani nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1999, tsamba 27 ndi 28.

^ ndime 22 Kuti mudziwe ngati zili zoyenera kuti munthu amene wagwiriridwa achotse mimba, werengani Galamukani! ya June 8 1993, tsamba 31 ndi 32, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.