Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’koyenera Kuti Makolo Aziphunzitsa Ana Awo Nkhani Zokhudza Kugonana?

Kodi N’koyenera Kuti Makolo Aziphunzitsa Ana Awo Nkhani Zokhudza Kugonana?

 Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi N’koyenera Kuti Makolo Aziphunzitsa Ana Awo Nkhani Zokhudza Kugonana?

▪ Makolo ambiri amayesetsa mmene angathere kuteteza ana awo kuti asatenge matenda oopsa. Makolo ayeneranso kuchita chimodzimodzi poteteza ana awo kuti asatengere makhalidwe oipa a m’dzikoli. Njira imodzi imene angachitire zimenezi ndi mwa kuwaphunzitsa zoyenera pa nkhani yokhudza kugonana. (Miyambo 5:3-23) Zinthu zimene makolo angawaphunzitse ndi zofunika kwambiri chifukwa kawirikawiri ana amaona zinthu zambiri zokhudza kugonana pa TV, pa Intaneti, m’mabuku komanso m’mafilimu.

Pulofesa wina wa zamaphunziro yemwenso amalemba mabuku, dzina lake Diane Levin, ananena kuti: “Vuto limene lilipo masiku ano si lakuti ana athu amaphunzira zinthu zokhudza kugonana. Koma vuto ndi zimene amaphunzira pa nkhaniyi, msinkhu umene akuziphunzira komanso amene amawaphunzitsa. Ana amaphunzira nkhani zokhudza kugonana kuchokera kwa anthu amalonda komanso ku zinthu zimene amaonera, kumvetsera ndiponso kuwerenga. Nkhani zimenezi zimakhala zolaula kwambiri ndipo zikhoza kuwasokoneza.”

Makolo ayenera kuteteza ana awo kuti asatengere maganizo olakwika amene akuwononga anthu ambiri m’dzikoli. (Miyambo 5:1; Aefeso 6:4) Ana ayenera kudziwa mmene matupi awo amagwirira ntchito komanso mmene angadzisamalirire. Ayeneranso kudziwa mmene angadzitetezere kwa anthu a khalidwe loipa. Mwana wamkazi asanathe msinkhu, ayenera kuphunzitsidwa mmene thupi lake lidzasinthire komanso ayenera kumvetsa chifukwa chake mkazi amatha msinkhu ndiponso mmene zimenezi zimachitikira. Nawonso ana aamuna ayenera kuphunzitsidwiratu nkhani zokhudza kutulutsa umuna polota. Ana adakali aang’ono, makolo ayenera kuyamba kuwaphunzitsa mayina oyenera a ziwalo zawo zobisika. Makolo achikondi amaphunzitsa ana awo zinthu zitatu zofunika kwambiri zokhudza ziwalo zimenezi. Iwo amawaphunzitsa kuti: (1) Ziwalo zimenezi ndi zapadera komanso zobisika. (2) Sibwino kumangozitchula mwachisawawa. (3) Sayenera kulola munthu wina kugwira kapena kuona ziwalozi mwachisawawa. Pamene ana akukula, makolo ayenera kudziwa nthawi yoyenera kuwafotokozera zimene zimachitika kuti mkazi atenge mimba. *

Kodi makolo ayenera kuyamba liti kuphunzitsa ana awo zinthu zimenezi? Ayenera kuyamba mwamsanga kuposa mmene ambiri amaganizira. Mtsikana akhoza kutha msinkhu ali ndi zaka 10 kapenanso asanakwanitse zaka zimenezi. Mnyamata akhoza kuyamba kutulutsa umuna polota, ali ndi zaka 11 kapena 12. Kusintha kumene kumachitika pa moyo wawoku kukhoza kuwasokoneza kwambiri ngati sakudziwa chimene chikuchitika. Makolo ayenera kufotokozera ana awo pasadakhale kuti kusintha kumeneku n’kwachibadwa ndipo palibe cholakwika chilichonse ndi zimenezi. Imeneyinso ndi nthawi yoyenera kuwathandiza kuti amvetse kufunika kotsatira mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino. Maphunziro ambiri onena za nkhani zokhudza kugonana amene anthu amaphunzitsa samafotokoza kufunika kotsatira mfundo za m’Baibulo pa nkhaniyi.​—Miyambo 6:27-35.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Mabuku awa ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova angathandize makolo pophunzitsa ana awo nkhani zimenezi: Galamukani! ya May 2006, tsamba 10-13, m’nkhani yakuti, “Thandizani Mwana Wanu Wamkazi Kukonzekera Kutha Msinkhu.” Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, m’mutu 6 wakuti, “Kodi Thupi Langali Latani?” Komanso Nsanja ya Olonda ya November 1, 2010, tsamba 12-14 m’nkhani yakuti, “Chinsinsi cha Banja Losangalala​—Muzikambirana ndi Ana Anu Nkhani Zokhudza Kugonana.”