Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsatira Mfundo za M’Baibulo?

Kodi N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsatira Mfundo za M’Baibulo?

 Kodi N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsatira Mfundo za M’Baibulo?

KODI malangizo a m’Baibulo pa nkhani ya kugonana ndi achikale komanso okhwima? Ayi, chifukwa malangizo a m’Baibulo angatithandize kupewa:

Kutenga matenda opatsirana pogonana

Kutenga mimba zapathengo

Mavuto amene amakhalapo ukwati ukatha

Kuvutika ndi chikumbumtima

Kudzichotsera ulemu

Mlengi wathu, Yehova Mulungu, * amafuna kuti tisangalale ndiponso kupindula ndi mphatso zimene watipatsa. Mulungu ‘amakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.’ (Yesaya 48:17) Munthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo pa nkhani ya kugonana amapindula chifukwa:

Mulungu amakondwera naye

Amakhala ndi mtendere wamumtima

Banja lake limakhala lokondana komanso lolimba

Amakhala ndi mbiri yabwino

Anthu amamulemekeza

Komano bwanji ngati panopa simukutsatira mfundo za m’Baibulo? Kodi n’zotheka kusintha khalidwe lanu? Kodi Mulungu adzapitirizabe kukuonani ngati woipa ngakhale mutasintha?

Taganizirani mfundo iyi: M’nthawi ya atumwi, anthu ena omwe anali mumpingo wachikhristu, poyamba anali adama, achigololo komanso omwe ankagonana ndi amuna anzawo. Koma anthu amenewa anasintha khalidwe lawo ndipo anadalitsidwa kwambiri. (1 Akorinto 6:9-11) Masiku anonso, anthu ambiri padziko lonse lapansi asintha khalidwe loipa limene ankachita poyamba. Anthu amenewa asintha khalidwe lawo lachiwerewere, n’kuyamba  kukhala moyo wogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo ndipo zimenezi zawabweretsera madalitso ambiri. Mwachitsanzo, taganizirani za Sarah amene tinamutchula m’nkhani yoyambirira ija.

“Nthawi Yomweyo Mtima Wanga Unakhala M’malo”

Sarah anazindikira kuti khalidwe lake lotayirira silinkam’patsa chimwemwe komanso ufulu umene ankafuna. Iye anati: “Chikumbumtima changa chinkandivutitsa kwambiri. Ndinkachita manyazi komanso ndinkada nkhawa kuti nditenga mimba kapena matenda oopsa. Ndinkakhulupirirabe kuti Mulungu aliko ndipo ndinkadziwanso kuti zochita zanga zimamukhumudwitsa. Ndinkaona kuti siine woyera pamaso pa Mulungu ndipo maganizo amenewa ankandisowetsa mtendere kwambiri.”

Kenako Sarah anatsimikiza mtima kuti akufuna kusintha khalidwe lake. Iye anapempha makolo ake, omwe ndi a Mboni za Yehova, kuti amuthandize. Anapemphanso thandizo kwa akulu a mumpingo wa Mboni za Yehova umene uli m’dera lawo. Iye anati: “Ndinadabwa kuona kuti makolo anga komanso akulu anandithandiza mwachifundo komanso mwachikondi kwambiri. Nthawi yomweyo mtima wanga unakhala m’malo.”

Panopa Sarah ali ndi ana awiri. Iye anati: “Sindimawabisira ana anga za khalidwe loipa limene ndinkachita. Ndimafuna kuti adziwe mavuto amene ndakumana nawo chifukwa chosatsatira malangizo a Mulungu. Ndimachita zimenezi n’cholinga chakuti ndiwathandize kudziwa kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo zokhudza kugonana kumatithandiza kwambiri pa mbali zonse za moyo wathu. Ndikukhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu amatipatsa mfundo za makhalidwe abwino pofuna kutiteteza.”

Inunso mungapindule chifukwa chotsatira malangizo achikondi a Mulungu. M’Baibulo muli lonjezo ili: “Malamulo ochokera kwa Yehova ndi olungama, amasangalatsa mtima. Chilamulo cha Yehova ndi choyera, chimatsegula maso. . . . Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.”​—Salimo 19:8, 11. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.

^ ndime 20 Kuti mudziwe zambiri zokhudza mfundo zothandiza za m’Baibulo, kambiranani ndi Mboni za Yehova za m’dera lanu. Kapena lembani kalata pogwiritsa ntchito adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 4. Kapenanso mungapite pamalo athu a pa Intaneti pogwiritsa ntchito adiresi iyi: www.jw.org.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Anthu amene satsatira mfundo za m’Baibulo amakhumudwitsa anzawo

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo amakhala ndi chikumbumtima choyera komanso amakhala ndi banja losangalala