Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chifukwa Chiyani Kudziwa Zimenezi Kuli Kofunika?

Kodi N’chifukwa Chiyani Kudziwa Zimenezi Kuli Kofunika?

 Kodi N’chifukwa Chiyani Kudziwa Zimenezi Kuli Kofunika?

“Ndinayamba kucheza ndi anyamata ndili ndi zaka 10. Poyamba tinkangogwirana manja ndiponso kupsompsonana. Koma kenako tinayamba kugwiranagwirana malo obisika komanso kuyerekezera njira zosiyanasiyana zogonanira. Ndili ndi zaka 15, ndinayamba ntchito ndipo kuntchitoko ndinayamba kukumana ndi azibambo amene ankafuna kuti ndizichita nawo zachiwerewere. Sindinkafuna kuoneka wotsalira ndipo ndinayamba kuchita nawo zonse zimene anzanga kuntchitoko ankachita. Komanso sindinkafuna kuti anzanga azindisala ndipo zimenezi zinachititsa kuti tipitirizebe kuyeserera njira zosiyanasiyana zogonana.”​—SARAH, * AUSTRALIA.

MUNGADABWE kudziwa kuti Sarah anakulira m’banja loopa Mulungu. Kuyambira ali mwana, makolo ake anayesetsa kumuphunzitsa kuti azitsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wake. Koma Sarah sanafune kutsatira zimene ankaphunzitsidwazo.

Anthu ena angaganize kuti zimene Sarah ankachita zilibe vuto lililonse. Anthu oterewa amaona kuti zomwe Baibulo limanena pa nkhani ya kugonana n’zosathandiza komanso n’zachikale. Ena amaona kuti palibe vuto kumalimbikira zachipembedzo koma kwinaku n’kumakhalanso moyo wachiwerewere.

Kodi kudziwa ndiponso kutsatira zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhaniyi kuli ndi phindu lililonse? Baibulo limanena kuti ndi ‘louziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi lopindulitsa pa kuphunzitsa.’ (2 Timoteyo 3:16) Ngati mumakhulupirira kuti Mulungu ndi amene analenga anthu komanso kuti Baibulo ndi Mawu ake ouziridwa, ndiye kuti mufunika kudziwa zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.

N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri sadziwa zenizeni zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya kugonana. Atsogoleri a chipembedzo amene amanena kuti amalemekeza zimene Baibulo limaphunzitsa, amanena zinthu zosiyana pa nkhani ya kugonana. Ndipo nkhani imeneyi yagawanitsa anthu a m’matchalitchi akuluakulu ambiri.

M’malo mongodalira zimene anthu ena amanena, bwanji osapeza nthawi n’kufufuza zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi? Nkhani yotsatirayi ili ndi mayankho a mafunso 10 amene anthu ambiri amakhala nawo okhudza zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kugonana. Mayankho amene ali mu nkhaniyi ndi osapita m’mbali ndipo ndi ochokera pa zimene Baibulo limaphunzitsa. Nkhani yomalizira pa nkhanizi ili ndi mfundo zotithandiza kudziwa kuti zimene timasankha kuchita zingakhale ndi zotsatira zabwino kapena zoipa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Dzinali talisintha.