Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anapulumutsidwa M’ng’anjo Yoyaka Moto

Anapulumutsidwa M’ng’anjo Yoyaka Moto

 Zoti Achinyamata Achite

Anapulumutsidwa M’ng’anjo Yoyaka Moto

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera mumtima mwawo.

Amene akutchulidwa kwambiri m’nkhaniyi: Sadirake, Mesake, Abedinego ndi Nebukadinezara

Chidule cha Nkhaniyi: Chikhulupiriro cha anyamata atatu achiheberi chinayesedwa.

1 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI DANIELI 3:1-30.

Mukamawerenga vesi 3 mpaka 7 yerekezerani phokoso limene likumveka.

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti ng’anjoyo inkaoneka bwanji? Fotokozani.

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti mawu a Nebukadinezara ankamveka bwanji pamene ankalamula kuti ng’anjoyo aisonkhezere kuwirikiza ka 7 kuposa mmene ankachitira nthawi zonse? (Werenganinso vesi 19 ndi 20.)

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti munthu wachinayi amene anali nawo m’ng’anjoyo ankaoneka bwanji? (Werenganinso vesi 24 ndi 25.)

․․․․․

Malinga ndi zimene zili m’vesi 16 mpaka 18, kodi mukuona kuti Sadirake, Mesake ndi Abedinego anasonyeza makhalidwe ati pamene ankalankhula ndi Nebukadinezara?

․․․․․

2 FUFUZANI MOZAMA.

Gwiritsani ntchito zinthu zofufuzira zimene muli nazo kuti mupeze kutalika kwa fano limene Nebukadinezara anapanga. (Werenganinso vesi 1.)

․․․․․

Mukayerekezera vesi 19 komanso 20 ndi vesi 28 komanso 29, kodi mukuona kuti Nebukadinezara anali munthu wotani?

․․․․․

 3 GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA . . .

Kulemekeza anthu amene ali ndi udindo.

․․․․․

Kufunika kotsatira zimene mumakhulupirira zivute zitani.

․․․․․

Mmene Yehova amatithandizira pa nthawi ya mayesero.

․․․․․

MMENE MUNGAGWIRITSIRE NTCHITO MFUNDOZI.

Kodi ndi pa zochitika ziti pamene chikhulupiriro chanu chikhoza kuyesedwa?

․․․․․

Kodi nkhani ya Sadirake, Mesake ndi Abedinego ingakuthandizeni bwanji kukhalabe wokhulupirika?

․․․․․

4 M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ITI IMENE YAKUKHUDZANI MTIMA KWAMBIRI, NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

Ngati mulibe Baibulo uzani a Mboni za Yehova, kapena kawerengeni Baibulo pa adiresi ya pa Intaneti iyi: www.jw.org.