Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Muyandikire Mulungu?

Kodi Mungatani Kuti Muyandikire Mulungu?

 Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

Kodi Mungatani Kuti Muyandikire Mulungu?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi Mulungu amayankha mapemphero onse?

Mulungu amauza anthu amitundu yonse kuti amuyandikire kudzera m’pemphero. (Salimo 65:2) Komabe sikuti iye amayankha mapemphero onse. Mwachitsanzo, pamene Aisiraeli anapitirizabe kuchita zinthu zoipa, Mulungu anakana kumva mapemphero awo. (Yesaya 1:15) Komanso mapemphero a mwamuna amene amachitira nkhanza mkazi wake amatsekerezedwa. (1 Petulo 3:7) Koma munthu amene wachita tchimo akalapa, ngakhale tchimo lakelo litakhala lalikulu, Mulungu amamva mapemphero ake.​—Werengani 2 Mbiri 33:9-13.

2. Kodi tiyenera kupemphera bwanji?

Ndi mwayi waukulu kuti anthufe timatha kupemphera kwa Mulungu ndipo pemphero ndi mbali ya kulambira kwathu. Choncho tiyenera kupemphera kwa Yehova basi. (Mateyu 4:10; 6:9) Koma popeza anthufe ndife ochimwa, tiyenera kupemphera m’dzina la Yesu chifukwa iye ndiye “njira.” (Yohane 14:6) Yehova safuna kuti tizinena mobwerezabwereza mapemphero oloweza kapena olemba. Iye amafuna kuti tizipemphera kuchokera mumtima.​—Werengani Mateyu 6:7; Afilipi 4:6, 7.

Mlengi wathu amamvanso munthu akapemphera chamumtima mosatulutsa mawu. (1 Samueli 1:12, 13) Iye amatiuzanso kuti tizipemphera nthawi zonse. Mwachitsanzo, tingapemphere podzuka, pogona, tisanayambe kudya komanso pamene takumana ndi mavuto.​—Werengani Salimo 55:22; Mateyu 15:36.

3. Kodi n’chifukwa chiyani Akhristu amasonkhana pamodzi?

Kuti tiyandikire Mulungu pamafunika kuchita khama chifukwa pali anthu amene sakhulupirira Mulungu amenenso amanyoza lonjezo lake lakuti dzikoli lidzakhala lamtendere. (2 Timoteyo 3:1, 4; 2 Petulo 3:3, 13) Choncho timafunika kusonkhana ndi Akhristu anzathu kuti tizilimbikitsana.​—Werengani Aheberi 10:24, 25.

Kucheza ndi anthu amene amakonda Mulungu kungakuthandizeni kuyandikira Mulungu. Misonkhano ya Mboni za Yehova imathandiza anthu kukhala ndi chikhulupiriro cholimba poona chikhulupiriro chimene enanso ali nacho.​—Werengani Aroma 1:11, 12.

  4. Kodi mungatani kuti muyandikire Mulungu?

Kusinkhasinkha kapena kuti kuganizira kwambiri zimene mwaphunzira m’Mawu a Mulungu kungakuthandizeni kuti muyandikire Yehova. Muyenera kuganizira kwambiri zochita za Mulungu, malangizo ake ndiponso malonjezo ake. Kuganizira kwambiri zinthu zimenezi ndiponso kupemphera kumathandiza munthu kuti aziyamikira chikondi ndiponso nzeru za Mulungu.​—Werengani Yoswa 1:8; Salimo 1:1-3.

Mungayandikire kwa Mulungu kokha ngati mumamudalira komanso kumukhulupirira. Koma chikhulupiriro chimafunika kuchilimbitsa. Muyenera kulimbitsa chikhulupiriro chanu mwa kuganizira kwambiri zinthu zimene mukuphunzira.​—Werengani 1 Atesalonika 5:21; Aheberi 11:1, 6.

5. Kodi kuyandikira Mulungu kungakuthandizeni bwanji?

Yehova amasamalira anthu amene amamukonda. Amawateteza ku zinthu zilizonse zimene zingawononge chikhulupiriro chawo ndiponso chiyembekezo chawo cha moyo wosatha. (Salimo 91:1, 2, 7-10) Yehova amatichenjeza kuti tizipewa zinthu zimene zingawononge thanzi lathu komanso zimene zingatipangitse kukhala osasangalala. Iye amatiphunzitsa zimene tingachite kuti tizikhala moyo wabwino kwambiri.​—Werengani Salimo 73:27, 28; Yakobo 4:4, 8.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 17 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.