Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Amene Akulamulira Dzikoli Ndani Kwenikweni?

Kodi Amene Akulamulira Dzikoli Ndani Kwenikweni?

 Kodi Amene Akulamulira Dzikoli Ndani Kwenikweni?

N’KUTHEKA kuti inuyo simunakumanepo ndi mtsogoleri wa gulu la zigawenga aliyense. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti kulibe anthu amene amatsogolera zigawengazi? Atsogoleri a zigawenga amakhala ochenjera kwambiri ndipo amachita zinthu mwakabisira moti nthawi zina amatha kumatsogolerabe zigawenga zinzawo iwowo ali m’ndende. Komabe, nkhani za m’manyuzipepala zonena za nkhondo yolimbana ndi anthu ozembetsa mankhwala osokoneza bongo, magulu a anthu ochita zachiwerewere, oba anthu ndiponso nkhani zina zambiri, zimatichititsa kudziwa kuti atsogoleri amenewa alipo komanso kuti zochita zawo zimabweretsa mavuto oopsa. Tikaona zinthu zimene zimachitika padzikoli, timadziwa kuti kunja kuno kuli atsogoleri a zigawenga.

Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, limanena kuti Satana ndi munthu weniweni wauzimu yemwe, mofanana ndi mkulu wa zigawenga, amaonetsetsa kuti zofuna zake zikukwaniritsidwa kudzera mu “zizindikiro zabodza” komanso “kusalungama ndi chinyengo.” Ndipotu Baibulo limanena kuti iyeyu “amadzisandutsa mngelo wa kuwala.” (2 Atesalonika 2:9, 10; 2 Akorinto 11:14) Choncho timakhulupiriranso kuti Mdyerekezi alipo tikaona zochita zake. Komabe anthu ambiri zimawavuta kukhulupirira kuti pali munthu wina wauzimu amene ndi woipa kwambiri. Tisanakambirane zimene Baibulo limanena zokhudza Mdyerekezi, tiyeni tione kaye zinthu zina zimene anthu ambiri amakhulupirira zomwe zimawachititsa kulephera kuvomereza mfundo yoti Mdyerekezi ndi weniweni ndipo alikodi.

“Kodi zinatheka bwanji kuti Mulungu yemwe ndi wachikondi alenge Mdyerekezi?” Popeza Baibulo limanena kuti Mulungu ndi wabwino komanso wangwiro, zingaoneke zosatheka kuti alenge munthu wankhanza, wopanda chifundo komanso woipa. Koma zoona n’zakuti, Baibulo silinena kuti Mulungu analenga munthu wotereyu. Ponena za Mulungu, ilo limati: “Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro, njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika, amene sachita chosalungama. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.”​—Deuteronomo 32:4; Salimo 5:4.

Mfundo yofunika kuiganizira ndi yakuti, kodi munthu wangwiro wolengedwa ndi Mulungu angachite zinthu zoipa? Mulungu sanalenge anthu ndiponso angelo ngati makina amene amangogwira ntchito imene anapangidwira. Koma iye anawapatsa ufulu wosankha zimene akufuna kuchita. Choncho munthu komanso mngelo aliyense angathe kusankha kuchita zabwino kapena zoipa. Ndipotu anthu ndiponso angelo amene Mulungu analenga akanati asamathe kusankha okha zochita n’kumangochita zabwino chifukwa chakuti ndi mmene analengedwera, zochita zawozo sizikanakhala ndi tanthauzo lililonse.

Choncho, n’zomveka kunena kuti Mulungu sangapereke ufulu wosankha zochita kwa zolengedwa zake kenako n’kumazikanizanso zolengedwazo kuchita zoipa ngati zitasankha kutero. Yesu ananena mawu osonyeza kuti Mdyerekezi sanagwiritse ntchito bwino ufulu wake wosankha zochita. Iye anati: “[Mdyerekezi] sanakhazikike m’choonadi.” (Yohane 8:44) Mawu amenewa akusonyeza kuti amene anadzakhala Mdyerekezi, poyamba anali munthu wauzimu wangwiro ndipo pa nthawiyo anali ‘wokhazikika m’choonadi.’ * Yehova Mulungu anapatsa zolengedwa zake ufulu wosankha chifukwa chakuti amazikonda komanso amazikhulupirira.​—Onani bokosi lakuti,  “Kodi Mngelo Kapena Munthu Wangwiro Angataye Ungwiro Wake?” patsamba 6.

“Mdyerekezi amatumidwa ndi Mulungu” Anthu ena amaona kuti Baibulo limasonyeza mfundo imeneyi m’buku la Yobu. Buku lina lothirira ndemanga  pa nkhani za m’Baibulo limanena kuti, mawu akuti Mdyerekezi anali “kuzungulirazungulira m’dziko lapansi” akusonyeza ntchito imene akazitape akale a ku Perisiya ankagwira. Iwo ankatumidwa ndi mfumu yawo kuti apite m’dziko lonselo kukafufuza nkhani n’kukapereka lipoti kwa mfumuyo. (Yobu 1:7) Komano, ngati Mdyerekezi anatumidwadi ndi Mulungu kuti akafufuze nkhani inayake, n’chifukwa chiyani ankafunika kufotokozera Mulungu kumene ankachokera, kuti anali “kuzungulirazungulira m’dziko lapansi”? Nkhani ya m’buku la Yobu siisonyeza kuti Mdyerekezi amathandiza Mulungu ntchito zina. M’malomwake imatchula Mdyerekezi kuti ndi Satana, kutanthauza “Wotsutsa.” Zimenezitu zikusonyezeratu kuti Mdyerekezi ndi Mdani wamkulu wa Mulungu. (Yobu 1:6) Ndiyeno kodi maganizo akuti Mdyerekezi amatumidwa ndi Mulungu amachokera kuti?

Chaka cha 100 C.E. chisanafike, mabuku amene anthu ena anawawonjezera m’Baibulo (monga la “Book of Jubilees” ndiponso la “Common Rule”) a kagulu kachipembedzo ka ku Qumran, anafotokoza nkhani yosonyeza kuti Mdyerekezi amakambirana zochita ndi Mulungu moti amachita zinthu motsatira chifuniro cha Mulunguyo. Katswiri wina wa mbiri yakale, dzina lake J. B. Russell, analemba m’buku lake kuti Martin Luther, yemwe anali mtsogoleri wa zipembedzo zomwe zinachoka m’tchalitchi cha Katolika, ankaona kuti Mdyerekezi ndi chipangizo chimene Mulungu amagwiritsira ntchito. Iye ankanena kuti Mdyerekezi “ali ngati chipangizo cha Mulungu chodulirira mbewu kapena khasu limene amagwiritsa ntchito m’munda wake.” (Mephistopheles) Russel anawonjezeranso kuti malinga ndi zimenezi, “khasu limeneli limasangalala likamadula udzu m’munda” komabe limagwira ntchito imeneyi potsatira zimene Mulungu akufuna, choncho tingati limachita zofuna za Mulungu. Patapita nthawi, katswiri wina wamaphunziro  apamwamba a zaumulungu, dzina lake John Calvin, anayamba kugwirizana ndi zimene Luther ankaphunzitsazi. Koma mfundo zimenezi zinakhumudwitsa anthu ambiri okhulupirira Mulungu amene amakonda chilungamo chifukwa ankaona kuti kugwiritsa ntchito Mdyerekezi mwa njira imeneyi sikungakhale chilungamo. Iwo ankaona kuti sizingatheke kuti Mulungu wachikondi akonze zoti padzikoli pazichitika zoipa. (Yakobo 1:13) Chiphunzitso chimenechi, komanso zinthu zina zoopsa kwambiri zimene zakhala zikuchitika m’zaka za m’ma 1900, zachititsa kuti anthu ambiri asamakhulupirire kuti kuli Mulungu ndiponso Mdyerekezi.

“Mdyerekezi si munthu weniweni koma ndi dzina chabe loimira zinthu zonse zoipa” Kunena kuti kunja kuno kulibe Mdyerekezi ndipo dzinali langokhala loimira zoipa zonse, kungapangitse kuti nkhani zina za m’Baibulo zikhale zovuta kuzimvetsa. Mwachitsanzo, malinga ndi nkhani imene ili pa Yobu 2:3-6, kodi Mulungu ankalankhula ndi ndani? Kodi tingati ankalankhula ndi maganizo oipa amene anali mumtima mwa Yobu, kapena tingati ankangolankhula yekha? Komanso kodi zikanatheka bwanji kuti Mulungu ayamikire Yobu chifukwa cha makhalidwe ake abwino kenako n’kulola kuti Yobuyo ayesedwe ndi maganizo oipa? Kunena kuti Mulungu anachita zimenezi n’chimodzimodzi ndi kunena kuti Mulungu ndi woipa. Zimenezi ndi zosiyana ndi zimene Baibulo limanena, zakuti iye “sachita zosalungama.” (Salimo 92:15) Mosiyana ndi zimenezi, Mulungu anakana ‘kutambasula dzanja lake’ kuti apweteke Yobu. Choncho, n’zoonekeratu kuti Mdyerekezi si maganizo chabe oipa kapena mbali yoipa ya makhalidwe a Mulungu. Iye ndi munthu wauzimu amene anadzipanga yekha kukhala Mdani wa Mulungu.

Kodi Amene Akulamulira Dzikoli Ndani Kwenikweni?

Masiku ano anthu ambiri amaganiza kuti ndi zachikale kumaganiza kuti kunja kuno kuli Mdyerekezi. Komabe anthu ambiri amamvetsa akauzidwa mfundo yakuti Mdyerekezi, osati wina aliyense, ndi amene amachititsa zoipa zonse. Ndipotu, pofuna kuti asiye kukhulupirira zoti kunja kuno kuli Mdyerekezi, anthu ambiri afika posiya kukhulupirira ngakhale Mulungu komanso mfundo zonse zokhudza makhalidwe abwino.

Wolemba ndakatulo wina wa zaka za m’ma 1800, dzina lake Charles-Pierre Baudelaire, analemba kuti: “Njira yaikulu kwambiri imene Mdyerekezi amanamizira nayo anthu, ndi kuyesetsa kuchititsa anthufe kukhulupirira zoti iye kulibe.” Pogwiritsa ntchito njira yodzibisa imeneyi, Mdyerekezi wachititsa anthu kuti azikayikira zoti kuli Mulungu. Zikanakhala kuti Mdyerekezi kulibe, ndiye kuti Mulungu ndi amene akanakhala ndi mlandu wa mavuto amene ali padzikoli ndipo zimenezi ndi zimene Mdyerekezi amafuna kuti anthu azikhulupirira.

Mofanana ndi mmene mtsogoleri wa zigawenga amachitira, Mdyerekezi amadzibisa n’cholinga chakuti akwaniritse zofuna zake. Kodi iye amafuna chiyani kwenikweni? Baibulo limayankha kuti: “Mulungu wa nthawi ino wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira, kuti asaone kuwala kwa uthenga wabwino waulemerero wonena za Khristu, yemwe ali chifaniziro cha Mulungu.”​—2 Akorinto 4:4.

Komabe pali funso limene tikufunika kudziwa yankho lake. Kodi Mulungu adzachita naye chiyani Mdyerekezi amene mwakabisira amachititsa mavuto komanso zinthu zonse zoipa? Nkhani yotsatira ili ndi yankho la funso limeneli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu sanawononge Mdyerekezi nthawi yomweyo chifukwa cha kupanduka kwake, werengani mutu 11 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Kodi Mdyerekezi ndi mtumiki wa Mulungu kapena ndi wotsutsa?

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 6]

 Kodi Mngelo Kapena Munthu Wangwiro Angataye Ungwiro Wake?

Ungwiro umene Mulungu anapatsa anthu oyambirira komanso angelo uli ndi malire. Ngakhale kuti Adamu analengedwa wangwiro, iye anafunika kuchita zinthu zogwirizana ndi malamulo a m’chilengedwe amene Mlengi wake anakhazikitsa. Mwachitsanzo, sizikanatheka kuti azidya dothi, miyala ndiponso matabwa koma n’kukhala bwinobwino osadwala. Komanso iye akananyalanyaza lamulo lachilengedwe la mphamvu yokoka, n’kukwera paphiri lalitali kenako n’kudumpha, akanavulala kwambiri ngakhalenso kufa kumene.

N’chimodzimodzinso ndi malamulo a Mulungu okhudza makhalidwe abwino. Palibe mngelo kapena munthu aliyense wangwiro amene angaswe malamulo a Mulungu amenewa koma osakumana ndi mavuto. Choncho, munthu kapena mngelo akagwiritsa ntchito molakwa ufulu wake wosankha zochita, zinthu sizimuyendera bwino ndipo amachita tchimo.​—Genesis 1:29; Mateyu 4:4.