Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limatiuza Wolamulira wa Dzikoli

Baibulo Limatiuza Wolamulira wa Dzikoli

 Baibulo Limatiuza Wolamulira wa Dzikoli

PA NTHAWI ina Yesu anauza anthu kuti: “Wolamulira wa dzikoli aponyedwa kunja.” Nthawi ina ananenanso kuti, ‘wolamulira wa dziko alibe mphamvu pa iye’ komanso kuti “wolamulira wa dziko lino waweruzidwa.” (Yohane 12:31; 14:30; 16:11) Kodi pamenepa Yesu ankanena za ndani?

Tikaona zimene Yesu ananena zokhudza “wolamulira wa dzikoli,” n’zodziwikiratu kuti ankanena za munthu wina, osati Atate ake, Yehova Mulungu. Ndiyeno kodi “wolamulira wa dzikoli” ndi ndani? Kodi iye “aponyedwa kunja” motani? Nanga “waweruzidwa” motani?

“Wolamulira wa Dzikoli” Anadziulula Yekha

Pamene Mdyerekezi ankayesa Yesu, anadzitamandira chifukwa cha ulamuliro umene ali nawo, mofanana ndi mmene mtsogoleri wa zigawenga amachitira akafuna kusonyeza mphamvu zake. Satana anaonetsa Yesu “maufumu onse a padziko lapansi,” ndipo kenako anauza Yesu kuti: “Ndikupatsani ulamuliro pa maufumu onsewa ndi ulemerero wawo wonse, chifukwa unaperekedwa kwa ine. Ndikhoza kuupereka kwa aliyense amene ndakonda kum’patsa. Chotero ngati inuyo mungandiweramireko kamodzi kokha, ulamuliro wonsewu udzakhala wanu.”​—Luka 4:5-7.

Zikanakhala kuti Mdyerekezi ndi dzina chabe lotanthauza zoipa zonse, ngati mmene anthu ena amaganizira, kodi pamene Yesu ankayesedwapa tingati iye anangokhala ndi maganizo oipa mumtima mwake? Kapena kodi inangokhala nkhawa chabe chifukwa cha mavuto amene amakonzera kukumana nawo pambuyo pobatizidwa? Ayi, Yesu sanakhalepo ndi maganizo oipa chifukwa Baibulo limanena kuti ‘mwa iye munalibe tchimo.’ (1 Yohane 3:5) N’chifukwa chake Yesu ananena kuti Mdyerekezi ndi “wolamulira wa dziko,” komanso kuti iye ndi “wopha anthu” ndiponso “wabodza.”​—Yohane 14:30; 8:44.

Patapita zaka pafupifupi 60 kuchokera pamene Khristu anayesedwa ndi Mdyerekezi, mtumwi Yohane anakumbutsa Akhristu anzake za mphamvu zimene Mdyerekezi ali nazo. Iye ananena kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” Yohane ananenanso kuti Mdyerekezi “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 12:9) Apa n’zoonekeratu kuti Baibulo likamati “wolamulira wa dzikoli” limanena Mdyerekezi. Koma kodi iye ali ndi mphamvu zochuluka bwanji zolamulira anthu?

Wolamulira wa Dzikoyu Ali Ndi Anzake Omuthandiza

Pamene mtumwi Paulo ankalemba za nkhondo ya chikhulupiriro imene Akhristu amamenya, anatchula za adani oipa kwambiri amene Akhristuwo akulimbana nawo. Iye ananena momveka bwino kuti: “Sitikulimbana ndi anthu athupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi maboma, maulamuliro, olamulira dziko a mdimawu, ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.” (Aefeso 6:12) Choncho pa nkhondo imeneyi tikulimbana ndi “makamu a mizimu yoipa,” osati “anthu athupi la magazi ndi nyama ayi.”

Mabaibulo ambiri amene amasuliridwa posachedwapa amasonyeza kuti mawu akuti “makamu a mizimu yoipa” amene ali pavesili, amatanthauza anthu auzimu oipa komanso amphamvu kwambiri ndipo mawuwa si dzina chabe lotanthauza zoipa zonse. Mabaibulo ena amamasulira mawuwa kuti “mizimu yotsogolera zoipa zonse imene imakhala kumwamba” (Revised Standard Version), “gulu la mizimu yoipa imene imakhala kumwamba” (The Jerusalem Bible), ndiponso “gulu la anthu oipa amphamvu kwambiri amene amakhala kumwamba” (The New English Bible). Choncho, Mdyerekezi wakhala akulamulira anthu pogwiritsa ntchito angelo opanduka amene anasiya “malo awo okhala” kumwamba.​—Yuda 6.

Buku la m’Baibulo la Danieli, lomwe lili ndi maulosi ambiri, limafotokoza bwino kuti “olamulira dziko” amenewa akhala akusonyeza mphamvu zawo padzikoli kuyambira kalekale. Mwachitsanzo, pa nthawi ina mneneri Danieli anapemphera kwa masabata atatu chifukwa chodera nkhawa kwambiri Ayuda anzake, omwe mu 537 B.C.E. anachoka ku ukapolo ku Babulo n’kubwerera ku  Yerusalemu. Mngelo amene anatumizidwa ndi Mulungu kuti akalimbikitse mneneriyu, anauza Danieli chifukwa chake anafika mochedwa. Iye anati: “Kalonga wa ufumu wa Perisiya ananditsekereza kwa masiku 21.”​—Danieli 10:2, 13.

“Kalonga wa ufumu wa Perisiya” ameneyu sanali munthu chifukwa munthu sangatsekereze mngelo wa Mulungu kwa milungu itatu. Mwachitsanzo, pa nthawi ina mngelo mmodzi yekha anapha asilikali amphamvu okwana 185,000 usiku umodzi wokha. (Yesaya 37:36) Choncho n’zoonekeratu kuti mngeloyu sanatsekerezedwe ndi mfumu ya Perisiya yotchedwa Koresi. Komanso mfumuyi sikanachita zimenezi chifukwa inkachitira zabwino Danieli ndi Ayuda anzake. Zimenezi zikusonyeza kuti ‘kalonga wa Perisiya’ ameneyu anali chiwanda chimene Mdyerekezi ankachigwiritsa ntchito ndipo chiwanda chimenechi chinapatsidwa ulamuliro pa Ufumu wa Perisiya. Ndipotu kumapeto kwa nkhaniyi, mngelo wa Mulungu ananena kuti anafunika kukamenyananso ndi “kalonga wa Perisiya” komanso chiwanda china chotchedwa “kalonga wa Girisi.”​—Danieli 10:20.

Kodi zimenezi zikutiuza chiyani? Zikutiuza kuti palidi “olamulira dziko” osaoneka, kapena kuti ziwanda zomwe ndi akalonga ndipo zinagawana dziko lapansili n’kumalilamulira motsogoleredwa ndi Satana Mdyerekezi. Koma kodi cholinga cha Satana ndi ziwanda zake ndi chiyani?

Wolamulira wa Dzikoli Anadziwika Kuti Ndi Woipa

M’buku lomalizira la m’Baibulo la Chivumbulutso, mtumwi Yohane anafotokoza mmene Yesu, kapena kuti Mikayeli mkulu wa angelo, anagonjetsera Mdyerekezi ndi ziwanda zake n’kuwathamangitsa kumwamba. Iye ananenanso zotsatira zoipa za kuthamangitsidwa kumeneku. Iye anati: “Tsoka dziko lapansi . . . chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”​—Chivumbulutso 12:9, 12.

Kodi Mdyerekezi wasonyeza bwanji mkwiyo wake waukulu? Zigawenga zambiri zikathedwa nzeru zimayendera mfundo yakuti ‘ngati sinditha kulamulira anthu kuli bwino ndingowawononga.’ Mfundo imeneyi ndi imenenso Mdyerekezi ndi ziwanda zake akuyendera. Iwo atsimikiza mtima kuti akamawonongedwa, awonongedwe limodzi ndi anthu apadzikoli. Podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa, Mdyerekezi akugwiritsa ntchito kwambiri imodzi mwa njira zake zikuluzikulu, yomwe ndi amalonda. Iye akugwiritsa ntchito njira imeneyi kulimbikitsa anthu kukhala ndi mtima wokonda kugula zinthu ndipo zimenezi zimachititsa kuti zinthu zachilengedwe zapadziko lonse ziziwonongedwa. Kuwonongedwa kwa zachilengedwe kumeneku, kukubweretsa mantha akuti mwina anthu padzikoli alibe tsogolo.​—Chivumbulutso 11:18; 18:11-17.

Kuyambira pamene anthu analengedwa, Mdyerekezi wasonyeza kuti amafuna kuti anthu azimulambira. Njira zina zimene amagwiritsa ntchito kuti akwanitse cholinga chakechi ndi nkhani zandale ndiponso zachipembedzo. Buku la Chivumbulutso limafotokoza kuti atsogoleri andale ali ngati zilombo ndipo Mdyerekezi wawapatsa ‘ulamuliro waukulu.’ Limafotokozanso kuti mgwirizano wa andale ndi achipembedzo uli ngati dama lauzimu. (Chivumbulutso 13:2; 17:1, 2) Taganizirani zinthu zimene zakhala zikuchitika kwa zaka zambiri monga kuponderezana, ukapolo komanso nkhondo zoyamba chifukwa cha kusankhana mitundu, zimene zaphetsa anthu mamiliyoni ambirimbiri. Kodi pali amene anganene kuti anthu amachita zoipa ndiponso zinthu zochititsa mantha zimenezi chifukwa ndi mmene chibadwa chawo chilili? Kodi kapena zoipa zimene anthu amachitazi zimasonyeza kuti amatsogoleredwa ndi olamulira oipa auzimu?

Baibulo limatithandiza kudziwa amene amachititsa kuti atsogoleri komanso maulamuliro padzikoli azichita zinthu zoipa. Kaya anthu amachita modziwa kapena ayi, koma mfundo ndi yakuti iwo amasonyeza mzimu umene wolamulira wa dzikoli ali nawo komanso mfundo imene iye amayendera yakuti ‘ngati sinditha kulamulira anthu kuli bwino ndingowawononga.’ Komano kodi anthu adzavutika ndi ulamuliro wa Mdyerekezi mpaka liti?

Mdyerekezi Awonongedwa Posachedwapa

Khristu ali padziko lapansili, ananena ndiponso kuchita zinthu zosonyeza kuti Mdyerekezi ndi ziwanda zake awonongedwa posachedwapa. Ophunzira  a Yesu atamufotokozera mmene anachotsera ziwanda, iye anawauza kuti: “Ndinayamba kuona Satana atagwa kale ngati mphezi kuchokera kumwamba.” (Luka 10:18) Pamenepa Yesu ankasangalala chifukwa cha zomwe zinali kudzachitika m’tsogolo iye akadzabwerera kumwamba. Monga Mikayeli mkulu wa angelo, iye anali kudzagonjetsa wolamulira wa dziko ameneyu. (Chivumbulutso 12:7-9) Kuphunzira bwinobwino maulosi a m’Baibulo kumasonyeza kuti zimenezi zinachitika kumwamba m’chaka cha 1914, kapena chakachi chitangodutsa kumene. *

Kuchokera nthawi imeneyo, Mdyerekezi akudziwa kuti watsala pang’ono kuwonongedwa. Ngakhale kuti ‘dziko lonse lili m’manja mwake,’ pali anthu mamiliyoni ambiri masiku ano amene akukana ulamuliro wake. Izi zili choncho chifukwa Baibulo lawatsegula m’maso kuti am’dziwe bwinobwino Mdyerekezi komanso kuti adziwe ziwembu zake. (2 Akorinto 2:11) Iwo amakhala ndi chiyembekezo akakumbukira mawu amene Paulo analembera Akhristu anzake, akuti: “Mulungu amene amapatsa mtendere aphwanya Satana pansi pa mapazi anu posachedwapa.” *​—Aroma 16:20.

Posachedwapa Mdyerekezi awonongedwa. Mu ulamuliro wachikondi wa Khristu, anthu olungama adzasandutsa dzikoli kukhala paradaiso. Zinthu monga chiwawa, chidani komanso dyera zidzatheratu. Baibulo limati: “Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso.” (Yesaya 65:17) Umenewutu udzakhala mpumulo waukulu kwa anthu amene amakana kulamulidwa ndi wolamulira wa dzikoli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 20 Kuti mudziwe zambiri zokhudza chaka chimenechi, werengani zakumapeto m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? patsamba 215 mpaka 218. Buku limeneli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 21 Mawu a Paulo amenewa ndi ofanana ndi ulosi woyambirira wa m’Baibulo wolembedwa pa Genesis 3:15 umene umasonyeza kuti Mdyerekezi adzawonongedwa. Pofotokoza zimene zidzachitikezo, Paulo anagwiritsa ntchito mawu achigiriki amene amatanthauza “kuswa chinthu n’kukhala zidutswazidutswa.”​—Vine’s Complete Expository Dictionary of Old and New Testament Words.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Mu ulamuliro wachikondi wa Khristu, anthu olungama adzasandutsa dzikoli kukhala paradaiso