Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Unali Mwayi Waukulu”

“Unali Mwayi Waukulu”

 Kalata Yochokera ku Haiti

“Unali Mwayi Waukulu”

CHIVOMEZI chitachitika ku Haiti pa January 12, 2010, zinandikhudza kwambiri moti sindinafunenso ngakhale kuonera nkhani zonena za chivomezicho pa TV. Ndiyeno pa 20 mwezi womwewo, mnzanga wina dzina lake Carmen anandiimbira foni n’kundiuza kuti zingakhale bwino titapita kukathandiza ku Haiti. Ndinadziwana ndi Carmen zaka zingapo zapitazo pamene tinkagwira ntchito ya unamwino mongothandiza pamalo ena amene ankamangapo Nyumba ya Ufumu. Kuyambira nthawi imeneyo tagwira limodzi ntchito zosiyanasiyana mongothandiza ndipo iye ndi ine timakondana kwambiri.

Koma Carmen atandiuza za ku Haiti, ndinamuuza kuti mwina zingandivute kukagwira nawo ntchito kumeneko chifukwa ndilibe mphamvu zokwanira komanso ndikumva chisoni kwambiri. Koma iye anandilimbikitsa pondikumbutsa kuti takhala tikugwira limodzi ntchito ngati zimenezi ndipo tikhoza kumakalimbikitsana. Mawu akewa anandilimbikitsadi moti ndinaimba foni kulikulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York ndipo ndinalankhula ndi munthu amene ankayang’anira ntchito yotumiza thandizo lochokera ku United States. Ndinamupempha kuti andilembe pa mndandanda wa anthu odzipereka kukagwira ntchito yothandiza anthu ku Haiti. Ndinamuuzanso za Carmen ndipo ndinanena kuti tingakonde kukagwira ntchito limodzi. Anandiuza kuti sanganditsimikizire ngati Carmen kapena ineyo tingaitanidwedi kukagwira ntchitoyi kapenanso ngati tingakagwiriredi ntchitoyi limodzi.

Zitatero ndinapitiriza kuchita zinthu monga mwa nthawi zonse ndipo ndinkakayikira kuti mwina satilola kupita ku Haiti. Patatha masiku anayi, Lolemba pa January 25, ndinalandira foni yochokera ku Brooklyn yondiuza kuti ndipite ku Haiti. Anandiuza kuti ngati ndikwanitse ndipite mawa lake. Sindinakhulupirire kuti andiloladi. Ndinavomera n’kulonjeza kuti ndikayesetsa kugwira ntchito mwakhama. Choyamba ndinapempha kuntchito kwathu kuti andipatse holide ya masiku angapo. Kenako ndinaimbira foni Carmen koma anandiuza kuti sanamuitane chifukwa sadziwa Chifalansa. Ngakhale kuti ndinachita mantha, ndinasangalala kwambiri chifukwa choitanidwa. Nditadula tikiti ya ndege, ndinanyamuka pa January 28 kuchokera ku New York kupita mumzinda wa Santo Domingo ku Dominican Republic, dziko limene linachita malire ndi dziko la Haiti.

Mtsikana wina wa Mboni za Yehova anandichingamira kubwalo la ndege ndipo anapita nane ku ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova ku Dominican Republic. Tsiku lomwelo kunafikanso anamwino awiri ochokera ku United States ndipo tinagona m’chipinda chimodzi. Tsiku lotsatira tinapita pa galimoto kunthambi ya ku Haiti yomwe ili ku Port-au-Prince ndipo tinayenda maola oposa 7.

Titawoloka malire n’kulowa m’dziko la Haiti, tinaona mmene chivomezi chinawonongera zinthu. Zinali zovuta kukhulupirira titaona mmene chivomezicho chinasakazira dziko lokongola limeneli pa masekondi 35 okha. Kungoona pa TV zimene zinachitikazo, unkazindikira kuti kunachitika zoopsa kwambiri. Ndiyeno taganizani mmene ndinamvera kuona malo amenewa ndi maso anga. Nyumba zambiri kuphatikizapo ya pulezidenti wa dzikolo zinawonongedwa ndipo zina zinagumukiratu osatsala kalikonse. Zambiri mwa nyumba zimenezi zinali zoti eni ake anagwira ntchito mwakhama moyo wawo wonse kuti apeze ndalama zomangira nyumbazi. Koma zonse zinawonongeka m’masekondi ochepa chabe. Zimenezi zinandikumbutsa mfundo yakuti  zinthu zakuthupi sizofunika kwambiri pa moyo wa munthu.

Titafika ku ofesi yanthambi, munthu wolandira alendo anationa tikulowa ndipo anatithamangira n’kutikumbatira kwinaku akumwetulira mwansangala kwambiri. Iye anatithokoza chifukwa chosiya kaye ntchito zathu ndi cholinga chodzathandiza anthu ku Haiti. Titamaliza kudya chakudya chamasana, tinapita ku Nyumba ya Msonkhano yapafupi yomwe pa nthawiyi inkagwiritsidwa ntchito ngati chipatala. Kumeneko ndinakumananso ndi a Mboni ena amene anabwera kudzathandiza monga mzamba wina wochokera ku Switzerland. Ndinakumananso ndi mwamuna wina ndi mkazi wake ochokera ku Germany, ndipo onse anali madokotala. Iwo analinso ndi wowathandiza wawo.

Ndinayamba ntchito usiku womwewo. M’nyumba ya Msonkhanoyo munali odwala 18 ndipo ena anali Mboni za Yehova pomwe ena anali a zipembedzo zina. Onsewa anagona pamatiresi omwe anawayala pansi. Wodwala aliyense anathandizidwa mofanana ndiponso kwaulere ndi madokotala a Mboni za Yehova.

Usiku umenewo wodwala wina amene anali wachikulire, wa zaka 80 anamwalira. Pa nthawi imene anamwalirayo mkazi wawo, ineyo komanso mnzanga wina amene tinkagona chipinda chimodzi tinali pomwepo. Kenako, mtsikana wina dzina lake Ketly anayamba kulira kwambiri chifukwa cha ululu. Mkono wake wakumanja unali utadulidwa chifukwa chovulala ndi chivomezi. Pafupi ndi Ketly panali mayi ena a Mboni amene anali mphunzitsi wake wa Baibulo. Usiku uliwonse mayi wa Mboniyo ankagona pafupi ndi Ketly kumudikirira.

Choncho ndinapita pamene panali Ketly kuti ndione mmene ndingamuthandizire kuchepetsako ululu wake. Koma ululu umene ankaumva sunali wa kuvulala kokhako ayi. Iye anali kuvutika mumtima. Anandiuza kuti pamene chivomezi chinkachitika n’kuti ali kunyumba kwa mnzake. Poyamba iwo sanadziwe chimene chinkachitika. Choncho anagwirana manja n’kuyamba kuthawira panja, koma khoma la nyumba linawagwera n’kuwakwirira. Ketly anaitana mnzakeyo koma sanayankhe ndipo nthawi yomweyo anadziwa kuti mnzakeyo wamwalira. Mbali ina ya thupi la mnzakeyo inali itamutsamira mpaka pamene kunafika anthu odzamupulumutsa patatha maola anayi. Chifukwa cha ngoziyi, mkono wonse wakumanja wa Ketly unadulidwa.

Usiku umenewo Ketly ankalephera kugona chifukwa ankangokumbukira za ngoziyo. Ketly akulira, anandiuza kuti: “Ndikudziwa zimene Baibulo limanena za masiku otsiriza kuti kudzachitika zivomezi. Ndikudziwanso kuti tikuyembekezera zinthu zabwino kwambiri m’tsogolo. Ndikudziwa kuti ndifunika kuthokoza chifukwa choti ndili moyo. Koma kwa nthawi yochepa muyerekezere kuti zimene zandichitikirazi zakuchitikirani inuyo. Moyo umakuyenderani bwinobwino koma mwadzidzidzi mwakumana ndi zimene zandichitikirazi.” Posowa chonena ndi mawu amenewa, ndinangomugwira nanenso n’kuyamba kulira. Tonse tinalira kwa nthawi yaitali mpaka pamene iyeyo anagona.

Tsiku lililonse ankatumiza dokotala mmodzi ndi anamwino awiri kumalo osiyanasiyana kuti akathandize odwala. Ineyo ananditumiza ku Petit Goave, ulendo wa maola awiri kuchokera ku Port-au-Prince. Ndinapita ndi namwino wina wochokera ku Florida ndi dokotala wochokera ku France. Tinafika kumeneko 9:30 m’mawa. Tinatsitsa katundu wathu n’kupita naye mu Nyumba ya Ufumu ya kuderalo. Anthu a kumeneko anali atauzidwa kuti tikubwera, choncho tinawapeza atangokhalakhala n’kumatidikirira.

Posakhalitsa tinayamba ntchito yathu. Kunja kunkatentha kwambiri ndipo anthu ofuna kuthandizidwa ankangochulukirachulukira. Tinagwira ntchito osapuma mpaka cha m’ma 3 koloko madzulo. Tsiku limenelo, tinabaya katemera anthu okwana 114 ndipo tinathandiza anthu enanso okwana 105. Ndinatopa kwambiri komabe ndinali wosangalala kuti ndinathandiza nawo anthu ovutika.

Ndinatha milungu iwiri ndi masiku angapo ndikuthandiza anthu ku Haiti. Pafupifupi usiku ulionse ndinkagwira ntchito kwa maola 12 ku Nyumba ya Msonkhano. Imeneyi inali ntchito yaikulu ndipo ndinali ndisanagwirepo ntchito chonchi pa moyo wanga wonse. Komabe ndinaona kuti kupita ku Haiti unali mwayi waukulu ndiponso dalitso.  Panopa ndikusangalala chifukwa ndinathandizako anthu a ku Haiti omwe anakumana ndi mavuto aakulu.

Komanso tingaphunzire zambiri kwa anthu a ku Haiti. Mwachitsanzo, mmodzi wa odwala amene ndinawasamalira anali mnyamata wazaka 15, dzina lake Eliser, yemwe anadulidwa mwendo chifukwa chovulala kwambiri. Ndinaona kuti mnyamatayu ankasungako chakudya chake kuti agawire Jimmy amene ankamuyang’anira usiku. Eliser anandifotokozera kuti Jimmy akamabwera madzulo kudzamudikirira nthawi zina ankakhala asanadye. Khalidwe la Eliser limeneli linandithandiza kuona kuti si kuti timachita kufunikira kukhala ndi zambiri pamoyo kapena kukhala wosadwala kuti tigawane ndi ena zimene tili nazo.

Anthu amene ndinkagwira nawo ntchito mongodzipereka nawonso ankasonyeza mzimu womwewu. Panali wina amene sankapeza bwino, komanso wina amene ankamva kupweteka msana. Koma onsewa anafuna kuthandiza kaye odwala ena ngakhale kuti nawonso anali ndi mavuto amenewa. Zimenezi zinandilimbikitsa kwambiri. Tonsefe nthawi zina tinkavutika maganizo ndiponso kutopa komabe tinkathandizana ndipo tinapitirizabe kugwira ntchito yathuyi. Sindidzaiwala ulendo wanga wa ku Haiti. Ndikuyamikira kwambiri kuti ndili m’gulu la Akhristu okoma mtima, okondana ndiponso amene amalolera kudzimana ndi cholinga chakuti athandize ena.

Ndisanachoke ku Haiti, awiri mwa odwala amene ndinawathandiza, amene anadulidwa mkono anandilembera makalata ondithokoza. Koma iwo ananenetsa kuti ndikawerenge makalatawo ndikakakwera ndege. Ndinachitadi zimene ananenazo. Nditawerenga makalata awowo, anandikhudza mtima kwambiri moti ndinkangolira.

Mpaka pano ndimaimbirana foni ndiponso kulemberana makalata ndi anthu amene ndinadziwana nawo ku Haiti. Ndi zoona kuti pa nthawi ya mavuto umadziwana ndi anthu ena ndipo mumakhala mabwenzi, koma pa nthawi imeneyi ndi pamenenso mabwenzi enieni amadziwika. Sindikukayika kuti ubwenzi wathu ndi anthu amenewa upitirirabe zivute zitani. Ndikuona kuti kukagwira nawo ntchito imeneyi unali mwayi waukulu.