Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Masomphenya a Zinthu Zakumwamba

Masomphenya a Zinthu Zakumwamba

 Masomphenya a Zinthu Zakumwamba

NGAKHALE mutayang’ana kumwamba nthawi yaitali bwanji, simungaone angelo. Ngakhale mutatchera khutu bwanji kuti mumve angelo akulankhula, simungamve chilichonse. Koma ngakhale ndi choncho, n’zosakayikitsa kuti angelo alipo. Angelo ndi amphamvu komanso anzeru kwambiri ndipo ali ndi mayina komanso makhalidwe osiyanasiyana. Ena amatichitira zabwino, koma ena amatifunira zoipa. Choncho tingati onse amafuna kutichitira zinazake anthufe.

Nayenso Mulungu woona ndi Mzimu. (Yohane 4:24) Dzina lake ndi Yehova ndipo dzina limeneli ndi lapadera komanso limamusiyanitsa ndi milungu yonse yonama. (Salimo 83:18) Wamasalimo analemba kuti: “Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri. Iye ndi wochititsa mantha kuposa milungu ina yonse. Chifukwa milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake, koma Yehova ndiye anapanga kumwamba. Ulemu ndi ulemerero zili pamaso pake. Mphamvu ndi kukongola zili m’nyumba yake yopatulika.”​—Salimo 96:4-6.

Masomphenya Onena za Mulungu Woona

Baibulo limatiuza kuti: “Palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse.” (Yohane 1:18) Munthu amene anabadwa osaona sangathe kudziwa mitundu yosiyanasiyana ya zinthu. N’chimodzimodzi anthufe. Sitingathe kudziwa maonekedwe ndiponso kukongola kwa Mulungu. Koma mofanana ndi mmene mphunzitsi amafotokozera ana zinthu zovuta kuzimvetsa m’njira yoti anawo amvetse, Mulungunso kudzera m’Mawu ake Baibulo amatifotokozera zinthu zimene sitingathe kuziona pogwiritsa ntchito zinthu zimene tingathe kuziona. Kudzera m’masomphenya amene anthu akale okhulupirika anaona, Yehova amatithandiza kukhala ndi chithunzi cha mmene kumwamba kulili. Amatithandizanso kuti tidziwe kugwirizana kumene kulipo pakati pa zolengedwa zakumwambako ndi ifeyo.

Mwachitsanzo, m’masomphenya amene mneneri Ezekieli anaona, moto, kuwala, mwala wamtengo wapatali wa safiro, ndi utawaleza zinaimira ulemerero wa Yehova. M’masomphenya ena, mtumwi Yohane anaona Yehova atakhala pampando wake wachifumu, ndipo ananena kuti Mulungu “anali wooneka ngati mwala wa yasipi, ndi mwala wofiira wamtengo wapatali.” Iye ananenanso kuti “utawaleza wooneka ngati mwala wa emarodi unazungulira mpando wachifumuwo.” Zimenezi zikusonyeza kuti pamene Yehova wakhala, pamakhala pokongola, posangalatsa ndiponso pamakhala mtendere wokhawokha.​—Chivumbulutso 4:2, 3; Ezekieli 1:26-28.

Nayenso mneneri Danieli anaona masomphenya okhudza Yehova. Iye anaona angelo “mamiliyoni 100 amene anali kuimirira pamaso [pa Yehova] nthawi zonse.” (Danieli 7:10) Ziyeneratu kuti zinali zochititsa mantha kwambiri. Munthu ataona mngelo mmodzi, ngakhale m’masomphenya chabe,  zingakhale zochititsa mantha. Ndiyeno taganizirani mmene zingakhalire mutaona mamiliyoni ambirimbiri a angelo.

M’Baibulo angelo amatchulidwa maulendo pafupifupi 400 ndipo ena mwa iwo ndi aserafi ndi akerubi. Mawu achigiriki ndiponso achiheberi amene m’Baibulo anawamasulira kuti “mngelo,” amatanthauza “mthenga.” Choncho, angelo amalankhulana ndipo kale ankalankhulanso ndi anthu. Dziwani kuti angelo si anthu amene poyamba ankakhala padziko lapansi kenako n’kupita kukhala kumwamba. Yehova analenga angelo amenewa kale kwambiri asanalenge anthu.​—Yobu 38:4-7.

M’masomphenya amene Danieli anaona, angelo ambirimbiri anasonkhana pa zochitika zina zapadera. Kenako Danieli anaona “wina wooneka ngati mwana wa munthu” akufika kumpando wachifumu wa Yehova kuti apatsidwe “ulamuliro, ulemerero, ndi ufumu kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira.” (Danieli 7:13, 14) “Mwana wa munthu” amene anapatsidwa ufumu kuti alamulire dziko lonse lapansi ndi Yesu Khristu woukitsidwa ndipo ali ndi udindo waukulu kuposa angelo onse. Posachedwapa ulamuliro wake udzalowa m’malo mwa maboma a anthu ndipo udzathetsa matenda, chisoni, kuponderezana, umphawi ndiponso imfa.​—Danieli 2:44.

Mosakayikira, angelo ambirimbiri okhulupirika anasangalala kwambiri Yesu ataikidwa kukhala mfumu chifukwa iwo amafunira anthu zabwino. Komabe n’zomvetsa chisoni kuti si angelo onse amene amafunira anthu zabwino.

Adani a Mulungu Ndiponso Anthu

Anthu atangolengedwa kumene, mmodzi mwa angelo, anapandukira Yehova ndipo anadzichititsa kukhala Satana, kutanthauza “Wotsutsa.” Iye anachita zimenezi pofuna kuti anthu azimulambira.  Satana ndi woipa kuposa wina aliyense, ndipo amatsutsa kwambiri Yehova, amene ndi wachikondi kwambiri kuposa wina aliyense. Angelo enanso anagwirizana ndi Satana n’kukhala opanduka ndipo Baibulo limati angelo amenewa ndi ziwanda. Ziwanda zimenezi ndi zoipa kwambiri ndipo zimachitira anthu nkhanza ngati mmene Satana amachitira. Ziwanda ndi zimene zimachititsa kwambiri kuti padzikoli pakhale mavuto monga kupanda chilungamo, matenda, umphawi ndiponso nkhondo.

Masiku ano anthu ambiri m’Matchalitchi Achikhristu sakondanso kulankhula za Satana. Koma ngakhale zili choncho, buku la m’Baibulo la Yobu limatithandiza kudziwa mngelo wopanduka ameneyu ndiponso zolinga zake. Baibulo limati: “Tsopano linafika tsiku limene ana a Mulungu woona ankapita kukaonekera pamaso pa Yehova, ndipo ngakhalenso Satana anapita nawo limodzi.” Polankhula ndi Mulungu, Satana ananena mwamwano kuti Yobu ankatumikira Mulungu chifukwa cha zabwino zimene Mulungu ankamuchitira. Poyesa kusonyeza umboni wa zimene ankanenazo, Satana anabweretsera Yobu mavuto aakulu. Ziweto zonse za Yobu zinafa ndipo ana ake onse 10 anafanso. Kenako anachititsa kuti Yobu adwale zilonda zopweteka kwambiri thupi lake lonse. Koma zonsezi sizinaphule kanthu.​—Yobu 1:6-19; 2:7.

Pali zifukwa zabwino zimene Yehova walolera Satana kuchita zoipa zakezo. Koma si kuti amulekerera mpaka kalekale. Posachedwapa Mdyerekezi awonongedwa. Yehova anayamba kale kuchita zinthu zina zosonyeza kuti Satana adzawonongedwa. Zinthu zimenezi zinachitika kumwamba ndipo zafotokozedwa m’buku la Chivumbulutso ndi cholinga chakuti tizidziwe. Baibulo limati: “Kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli [amene ndi Yesu Khristu ataukitsidwa] ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka [Satana]. Chinjokacho ndi angelo ake chinamenya nkhondo, koma sichinapambane, ndipo malo awo sanapezekenso kumwamba. Choncho chinjokacho chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.”​—Chivumbulutso 12:7-9.

Onani kuti lembali likunena kuti Satana “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” Iye akuchita zimenezi polimbikitsa zipembedzo kuti ziziphunzitsa zabodza ndi cholinga choti anthu asamamvere Yehova komanso Mawu ake. Bodza lina limene zipembedzo zimaphunzitsa ndi lakuti munthu akamwalira, mzimu wake umapita kwinakwake. Pali zinthu zosiyanasiyana zimene anthu amakhulupirira pa mfundo imeneyi. Mwachitsanzo ku Africa kuno komanso ku Asia, anthu ambiri amakhulupirira kuti munthu akamwalira amapita kudziko lamizimu kukakhala ndi makolo akale. Ziphunzitso zonena za purigatoliyo ndiponso zonena kuti anthu oipa amakapsa kumwamba, zinayamba chifukwa chokhulupirira kuti munthu akamwalira amapitirizabe kukhala ndi moyo kwinakwake.

Kodi Munthu Akamwalira Amapitadi Kumwamba?

Nanga bwanji zimene anthu ambiri padziko lonse amakhulupirira zakuti anthu onse abwino amapita kumwamba? Ndi zoona kuti anthu ena abwino amapita kumwamba. Komatu anthu amene amapita kumwambawo ndi ochepa kwambiri tikayerekezera ndi anthu ambirimbiri amene anamwalira chilengedwere dzikoli. Baibulo limanena kuti anthu okwana 144,000 “anagulidwa padziko lapansi” ndipo adzakhala “ansembe” ndi “mafumu olamulira dziko lapansi.” (Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 3) Anthu amenewa limodzi ndi Mwana wa munthu, Yesu Khristu, ndi amene adzalamulira mu boma la kumwamba mu Ufumu wa Mulungu. Boma limenelo lidzawonongeratu Satana ndi ziwanda zake ndipo lidzabweretsa paradaiso padziko lapansi. Kenako, anthu ambiri amene anamwalira adzaukitsidwa ndipo adzakhala ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi.​—Luka 23:43.

Choncho, pomalizira tinganene kuti ndi zoona kuti kumwamba kuli mizimu yambirimbiri. Wamkulu pa onsewa ndi Yehova Mulungu yemwe ndi Mlengi wa za moyo zonse. Pali angelo okhulupirika mabiliyoni ambiri amene amamutumikira. Motsogoleredwa ndi Satana, angelo ena anapandukira Yehova ndipo akuyesetsa kuti asocheretse anthu. Komanso anthu ena ochepa kwambiri “anagulidwa” kapena kuti kusankhidwa kuchokera padziko lapansi kuti akagwire ntchito yapadera kumwamba. Malinga ndi mfundo imeneyi, tsopano tiyeni tikambirane za amene tifunika kulankhula naye ndiponso mmene tingalankhulire naye.