Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tiyenera Kupemphera kwa Ndani?

Kodi Tiyenera Kupemphera kwa Ndani?

 Kodi Tiyenera Kupemphera kwa Ndani?

MULUNGU WAMPHAMVUYONSE wapatsa Yesu komanso angelo ena maudindo osiyanasiyana. Mwachitsanzo, Mulungu anapatsa Yesu Khristu udindo wolamulira dziko lapansi ndiponso anasankha angelo okhulupirika kuti azithandiza pa ntchito yolengeza uthenga wabwino. (Chivumbulutso 14:6) Koma pa nkhani ya pemphero sanachite zimenezi. Iye sanapatse aliyense udindo woyankha mapemphero. Mapemphero athu ayenera kupita kwa Mulungu yekha basi.

Yehova ndi “Wakumva pemphero.” (Salimo 65:2) Iye amamva ndiponso kuyankha mapemphero athu. Pa nkhani imeneyi, mtumwi Yohane analembera Akhristu anzake kuti: “Chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, [Mulungu] amatimvera. Komanso, popeza timadziwa kuti amatimvera tikapempha chilichonse, timakhala ndi chikhulupiriro kuti tilandira zinthu zimene tamupemphazo.”​—1 Yohane 5:14, 15.

Angelo okhulupirika safuna kuti tizipemphera kwa iwo. Iwo amamvetsa ndiponso kugwirizana ndi zimene Mulungu anakonza pa nkhani ya pemphero, ngakhale kuti nthawi zina Mulungu amagwiritsa ntchito iwowo kuyankha mapemphero a anthu. Mwachitsanzo, mneneri Danieli atapemphera kwa Yehova za mavuto a ku Yerusalemu, Mulungu anayankha pemphero la Danieli potumiza mngelo Gabirieli kuti akamulimbikitse.​—Danieli 9:3, 20-22.

 Kodi Amakhaladi Mauthenga Ochokera Kwa Anthu Amene Anamwalira?

Kodi ndi bwino kufuna kulankhula ndi anthu amene anamwalira? Timamva nkhani zambiri zokhudza anthu amene analankhulana ndi imene iwo amati ndi mizimu ya anthu akufa. Mwachitsanzo, sing’anga wina wamizimu anafika pakhomo pa mayi wina ku Ireland kudzamuuza kuti usiku analankhula ndi mwamuna wa mayiyu, dzina lake Fred. Koma Fred amene ankanenayo, anali atamwalira milungu ingapo izi zisanachitike. Sing’anga wamizimuyo anafotokozera mayiyu zimene “Fred” ananena. Mayiyu anadabwa chifukwa nkhani zimene sing’angayu anamuuza panalibenso munthu wina amene ankazidziwa koma iyeyo ndi mwamuna wake basi. Zinali zosavuta kuti mayiyu akhulupirire kuti mwamuna wake Fred anali moyo kudziko lamizimu ndipo akufuna kuti azilankhula naye kudzera mwa sing’anga wamizimuyo. Koma kukhulupirira zimenezi kumatsutsana ndi zimene Baibulo limanena momveka bwino zokhudza akufa.​—Onani bokosi lili m’munsili.

Ndiye kodi nkhani ngati zimenezi tingazifotokoze bwanji? Kodi chimachitika ndi chiyani kwenikweni? Njira ina imene ziwanda zimasocheretsera anthu, ndi kudziyerekeza kukhala ngati munthu amene anamwalira ndipo pa nkhani ya mayiyu, zinayerekeza kukhala Fred. Cholinga chake ndi kuchititsa anthu kuti asiye kukhulupirira zimene Baibulo limaphunzitsa komanso kuti asiye kukhulupirira Yehova. Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti Satana ndi ziwanda zake amasocheretsa anthu ndi ‘ntchito iliyonse yamphamvu ndi zizindikiro zabodza ndi zodabwitsa, ndi kusalungama ndi chinyengo chilichonse. Zonsezi amazichita kwa amene akupita kukawonongedwa.’​—2 Atesalonika 2:9,10.

 Ndi zachidziwikire kuti pali asing’anga komanso anthu ena amene amakhulupirira mizimu ndipo amakhulupirira kuti amalankhulana ndi akufa. Ngatidi amalankhulana ndi winawake, kwenikweni amakhala akulankhulana ndi ziwanda zomwe ndi adani a Yehova. Mofanana ndi zimenezi, pali anthu ena amene amanyengeka poganiza kuti akulambira Mulungu woona. Mtumwi Paulo anauziridwa kulemba chenjezo lamphamvu ili: “Zinthu zimene mitundu ina imapereka nsembe imazipereka kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.”​—1 Akorinto 10:20,21.

Popeza tadziwa kuti tingathe kupemphera kwa Mulungu, yemwe ndi Wamkulukulu, amene amatikonda ndiponso kutiganizira, tingafunirenjinso kupemphera kwa munthu wina? Ndipotu Baibulo limatitsimikizira kuti: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.”​—2 Mbiri 16:9.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Popeza tadziwa kuti tingathe kupemphera kwa Mulungu, yemwe ndi Wamkulukulu, amene amatikonda ndiponso kutiganizira, tingafunirenjinso kupemphera kwa munthu wina?

[Bokosi/​Chithunzi pamasamba 8, 9]

Mfundo Zoona Komanso Mfundo Zabodza

MFUNDO YOONA: SATANA ALIPODI

“Ngakhale Satana amadzisandutsa mngelo wa kuwala.”​—2 Akorinto 11:14.

“Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.”​—1 Petulo 5:8.

“Amene amachitabe tchimo anachokera kwa Mdyerekezi, chifukwa Mdyerekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi.”​—1 Yohane 3:8.

“Gonjerani Mulungu, koma tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.”​—Yakobo 4:7.

“Mdyerekezi . . . ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake, ndipo sanakhazikike m’choonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi. Pamene akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.”​—Yohane 8:44.

MFUNDO YABODZA: MUNTHU AKAFA MZIMU WAKE UMAPITA KWINAKWAKE

“Udzadya chakudya kuchokera m’thukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa. Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”​—Genesis 3:19.

“Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.”​—Mlaliki 9:5.

“Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse, pakuti kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda kumene ukupitako.”​—Mlaliki 9:10.

“Mzimu wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka. Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.”​—Salimo 146:4.

MFUNDO YOONA: ANGELO OKHULUPIRIKA AMATISAMALIRA

“Mngelo wa Yehova amamanga msasa mozungulira onse oopa Mulungu, ndipo amawapulumutsa.”​—Salimo 34:7; 91:11.

“Kodi angelo onse si mizimu yotumikira ena, yotumidwa kukatumikira amene adzalandire chipulumutso monga cholowa chawo?”​—Aheberi 1:14.

“Ndinaona mngelo winanso akuuluka chapafupi m’mlengalenga. Iye anali ndi uthenga wabwino wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa anthu okhala padziko lapansi, ndi kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse. Iye anali kunena mofuula kuti: ‘Opani Mulungu ndi kumupatsa ulemerero.’”​—Chivumbulutso 14:6, 7.

MFUNDO YABODZA: YESU NDI WOFANANA MPHAMVU NDI MULUNGU

“Koma ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu. Mutu wa mkazi ndi mwamuna, ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.”​—1 Akorinto 11:3.

“Koma zinthu zonse zikadzakhala pansi pake, Mwanayonso adzadziika pansi pa amene anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.”​—1 Akorinto 15:28.

“Ndithudi ndikukuuzani, Mwanayo sangachite chilichonse chongoganiza payekha, koma chokhacho chimene waona Atate wake akuchita.”​—Yohane 5:19.