Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Otchulidwa M’Baibulo Anakhaladi Ndi Moyo Nthawi Yaitali Choncho?

Kodi Anthu Otchulidwa M’Baibulo Anakhaladi Ndi Moyo Nthawi Yaitali Choncho?

 Kodi Anthu Otchulidwa M’Baibulo Anakhaladi Ndi Moyo Nthawi Yaitali Choncho?

MAYI JEANNE LOUISE CALMENT anamwalira pa August 4, 1997 m’tauni ya kwawo imene ili kum’mwera cha kum’mawa kwa dziko la France. Iwo anamwalira ali ndi zaka 122.

Masiku ano, kupita patsogolo kwa sayansi, zachipatala ndiponso zinthu zina, zikuthandiza anthu ambiri kuti azikhala ndi moyo wautali. Koma ngakhale zili choncho, si anthu ambiri amene amafika kapena kupitirira zaka 100. Mwina ndi chifukwa chake munthu amati akafika zaka 100 kapena kupitirira amatchuka kwambiri ngati mmene zinachitikira ndi mayi Calment.

Baibulo limanena kuti kale anthu ankakhala ndi moyo nthawi yaitali ndipo ena anafika zaka pafupifupi 1,000. Koma kodi zimenezi ndi zoona? Kodi anthu otchulidwa m’Baibulo anakhaladi ndi moyo nthawi yaitali choncho? Nanga zimenezi zikutikhudza bwanji masiku ano?

Anthu Amene Anakhala Ndi Moyo Nthawi Yaitali Kwambiri

Buku la m’Baibulo la Genesis limatchula anthu 7 amene anakhala ndi moyo zaka zoposa 900 ndipo onsewa anabadwa Chigumula cha Nowa chisanachitike. Anthu amenewa ndi Adamu, Seti, Inoshi, Kenani, Yaredi, Metusela ndi Nowa. (Genesis 5:5-27; 9:29) Ambiri mwa anthu amenewa si odziwika kwa anthu ambiri, koma onsewa analipo ndipo anali m’mibadwo 10 yoyambirira ya anthu. Metusela ndi amene anakhala ndi moyo wautali kuposa onsewo. Iye anakhala ndi moyo zaka 969.

Baibulo limatchula anthu enanso okwana 25 amene anakhala ndi moyo zaka zoposa zimene anthu amakhala ndi moyo masiku ano. Ena mwa anthu amenewa anakhala ndi moyo zaka 300, 400, 700 mwinanso kuposerapo. (Genesis 5:28-31; 11:10-25) Komabe anthu ambiri amaganiza kuti nkhani za m’Baibulo zonena za anthu amene anakhalako ndi moyo nthawi yaitali chonchi ndi nthano chabe. Koma kodi tiyenera kuonadi kuti nkhani zimenezi ndi nthano chabe?

 Nthano Kapena Zochitika Zenizeni?

Malinga ndi zimene chikalata chimene linatulutsa bungwe lina la zofufuzafufuza la ku Germany (Max Planck Institute for Demographic Research), akatswiri amakhulupirira kuti zaka za mayi Calment amene tawatchula poyamba aja ndi zolondola. Iwo amanena choncho chifukwa cha zinthu zimene mayiwo ananena zomwe ofufuzawo anapeza umboni wake mosavuta. Zinthuzo zinali zokhudza iwowo kapena achibale awo zimene zinachitika pa nthawi inayake. Kenako zimene mayiwo ananena anazitenga ndi kuziyerekezera ndi zinthu zopezeka mu mafaelo a boma, m’zikalata za kukhoti, ku tchalitchi, nkhani za mu nyuzipepala komanso mukaundula wa ziwerengero za anthu. Komano ngakhale kuti sanathe kupeza umboni wa mfundo zonse zimene mayiwo ananena, umboni umene iwo anapeza ndiponso mfundo zina zinawatsimikizira kuti mayiyu anakhaladi ndi moyo zaka zimenezi.

Nanga bwanji nkhani za m’Baibulo? Kodi pali umboni wakuti zinachitikadi? Inde ulipo. Ngakhale kuti si mfundo zonse zimene anthu ofufuza apeza umboni wake, iwo apeza umboni wosiyanasiyana wotsimikizira kuti zinthu zakale zotchulidwa m’Baibulo zinachitikadi. Mbiri yakale, sayansi, ndiponso kuwerengera madeti a zochitika zakale zimasonyeza umboni umenewo. * Sitifunika kudabwa ndi zimenezi chifukwa Baibulo limanena kuti: “Mulungu akhale wonena zoona, ngakhale kuti munthu aliyense angapezeke kukhala wonama.” (Aroma 3:4) Inde, m’Baibulo mulibe nkhani yabodza chifukwa ndi buku ‘louziridwa ndi Mulungu.’​—2 Timoteyo 3:16.

Mose amene anatsogoleredwa ndi Yehova Mulungu kulemba Pentatuke kapena kuti mabuku asanu oyambirira a m’Baibulo, ndi mmodzi mwa anthu otchuka komanso olemekezedwa kwambiri m’mbiri yonse ya anthu. Ayuda amamuona kuti ndiye wamkulu kwambiri pa aphunzitsi awo onse. Komanso Asilamu amamuona kuti ndi mmodzi wa aneneri awo akuluakulu. Ndipo Akhristu amaona kuti Mose anali kalambulabwalo wa Yesu Khristu. Ndiyeno kodi ndi zomveka kuganiza kuti zimene munthu wotchuka ndiponso wolemekezedwa ameneyu analemba ndi zabodza?

Kodi Ankawerengera Zaka Mosiyana ndi Masiku Ano?

Anthu ena amanena kuti mmene ankawerengera zaka kalelo ndi zosiyana ndi mmene timawerengera masiku ano, moti chimene ankati ndi chaka nthawi imeneyo kwenikweni unali mwezi umodzi. Komabe tikafufuza bwino nkhani za m’buku la Genesis timapeza kuti anthu kalelo ankawerengera nthawi mofanana ndi mmene timawerengera masiku ano. Taganizirani zitsanzo ziwiri izi. Nkhani yonena za Chigumula imanena kuti Chigumulacho chinayamba Nowa ali ndi zaka 600, “m’mwezi wachiwiri, pa tsiku la 17 la mweziwo.” Ndiyeno nkhaniyi imapitiriza kunena kuti madzi anamiza dziko lapansi kwa masiku 150 ndipo “m’mwezi wa 7, pa tsiku la 17 la mweziwo, chingalawacho chinaima pamapiri a Ararati.” (Genesis 7:11, 24; 8:4) Choncho Baibulo limati nthawi yokwana miyezi isanu, kuchokera pa tsiku la 17 la mwezi wachiwiri kukafika pa tsiku la 17 la mwezi wa 7 chaka chomwecho, ndi masiku 150. Ndiyetu n’zooneratu kuti mfundo yoti chaka chinali mwezi umodzi ilibe umboni.

Ndiyenso taganizirani chitsanzo china ichi. Malinga ndi zimene lemba la Genesis 5:15-18 limanena, Mahalalele anabereka mwana wamwamuna ali ndi zaka 65 ndipo anapitiriza kukhala ndi moyo zaka zina 830 kenako anamwalira ali ndi zaka 895. Mdzukulu wake Inoki nayenso anabereka mwana wamwamuna ali ndi zaka 65. (Genesis 5:21) Zikanakhala kuti kale chaka chinali ngati mwezi umodzi, ndiye kuti anthu amenewa anabereka anawo ali ndi zaka 5 zokha. Kodi zimenezi zingatheke?

Kuwonjezera pa umboni umenewu, nawonso akatswiri ofukula zinthu zakale apeza zinthu zomwe zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena zoti kale anthu ankakhaladi ndi moyo nthawi yaitali. Baibulo limanena kuti Abulahamu anali wochokera mumzinda wa Uri ndiponso kuti anasamukira mumzinda wa Harana. Kenako anasamukira m’dera lina la ku Kanani ndipo anagonjetsa Kedorelaomere, mfumu ya Elamu. (Genesis 11:31; 12:5; 14:13-17) Zimene akatswiri ofukula zinthu zakale apeza zimatsimikizira kuti kunalidi malo komanso anthu otchulidwa m’nkhani ya Abulahamuyi. Komanso zofukulidwa ndi akatswirizi zimatithandiza kumvetsa bwino madera ndi zikhalidwe za anthu otchulidwa mu nkhani imeneyi. Popeza kuti zimene Baibulo limanena zokhudza Abulahamu ndi zoona, palibenso chifukwa chokayikira kuti iye anamwalira ali ndi zaka 175.​—Genesis 25:7.

Choncho palibe chifukwa chokayikira zimene Baibulo limanena kuti anthu akale amenewa anakhala ndi moyo nthawi yaitali kwambiri. Koma mwina munganene kuti, ‘Kaya anthu akale amenewo anakhala zaka zambiri kapena ayi, kodi zili ndi ntchito yanji kwa ine?’

 Mutha Kukhala ndi Moyo Wautali Kwambiri

Anthu amene anakhalako Chigumula chisanachitike anakhala ndi moyo nthawi yaitali. Umenewu ndi umboni wosonyeza kuti munthu anapangidwa mwapadera kwambiri kuti athe kukhala ndi moyo nthawi yaitali. Masiku ano sayansi yapita patsogolo kwambiri. Zimenezi zathandiza akatswiri kuphunzira zambiri zokhudza mmene thupi la munthu linapangidwira. Mwachitsanzo, aphunzira kuti thupi linapangidwa mochititsa chidwi moti limatha kudzichiritsa lokha. Zimenezi zachititsa asayansiwa kuvomereza kuti munthu angathe kukhala ndi moyo nthawi yaitali. Pulofesa wina wophunzitsa madokotala, dzina lake Tom Kirkwood, ananena kuti: “Madokotala sakumvetsabe zimene zimachititsa kuti anthu azikalamba.”

Komabe Yehova Mulungu amadziwa chimene chimachititsa kuti munthu akalambe komanso amadziwa mmene angathetsere vutoli. Iye ndi amene analenga munthu woyambirira Adamu ali wangwiro ndipo anafuna kuti anthu azikhala ndi moyo kwamuyaya. Koma ndi zomvetsa chisoni kuti Adamu anasankha kupandukira Mulungu. Zotsatira zake zinali zoti anachimwa ndipo sanakhalenso wangwiro. Baibulo limati: “Uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Zimenezi ndi zimene asayansi sakudziwa. Anthu amadwala, kukalamba ndiponso kufa chifukwa cha uchimo ndi kupanda ungwiro.

Komabe zimene Mlengi wathu wachikondi anafuna poyamba sizinasinthe. Pofuna kutsimikizira kuti zimenezi ndi zoona, iye anatipatsa nsembe ya dipo la Mwana wake Yesu Khristu. Dipo limeneli ndi limene lidzathandiza kuti tidzakhale angwiro komanso kuti tidzapeze moyo wosatha. Baibulo limati: “Monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.” (1 Akorinto 15:22) Anthu amene anakhalapo Chigumula chisanachitike anakhalako pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene anthu anali angwiro. Ndi chifukwa chake ankakhala ndi moyo nthawi yaitali kwambiri kuposa mmene timakhalira masiku ano. Koma masiku ano tili pafupi kwambiri ndi nthawi imene Mulungu akufuna kukwaniritsa zimene analonjeza. Posachedwapa, mavuto onse obwera chifukwa cha uchimo ndi kupanda ungwiro adzatha, ndipo anthu sazidzakalambanso ndiponso kufa.​—Yesaya 33:24; Tito 1:2.

Kodi mungatani kuti mudzapeze madalitso amenewa? Musaganize kuti zimene Mulungu analonjeza sizingachitike. Yesu anati: “Iye wakumva mawu anga ndi kukhulupirira amene anandituma ine ali nawo moyo wosatha.” (Yohane 5:24) Choncho phunzirani Baibulo ndipo muzizitsatira pa moyo wanu. Mukamachita zimenezo ndiye kuti mukutsatira chitsanzo cha anthu amene mtumwi Paulo anawafotokoza kuti ‘ankasunga maziko abwino a tsogolo lawo monga chuma, kuti agwire mwamphamvu moyo weniweniwo.’ (1 Timoteyo 6:19) Khulupirirani kuti Mulungu amene anachititsa kuti anthu omwe atchulidwa m’Baibulo akhale ndi moyo nthawi yaitali kwambiri, angachititsenso kuti inuyo mukhale ndi moyo wosatha.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Kuti mudziwe zambiri onani buku lakuti Baibulo​—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 12]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

1000*

969* METUSELA

950* NOWA

930* ADAMU

900*

800*

700*

600*

500*

400*

300*

200*

100* MUNTHU WA MASIKU ANO

*ZAKA