Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Iye Amadziwa Bwino “Mtima wa Ana a Anthu”

Iye Amadziwa Bwino “Mtima wa Ana a Anthu”

 Yandikirani Mulungu

Iye Amadziwa Bwino “Mtima wa Ana a Anthu”

2 MBIRI 6:29, 30

KODI ndani amene sanadepo nkhawa ndi zinazake kapena kukumana ndi mavuto pa moyo wake? Nthawi zina tingaone ngati palibe amene akumvetsa mavuto amene tikukumana nawo komanso mmene tikumvera. Komabe pali winawake amene amamvetsa bwino mmene tikumvera ndipo ameneyu ndi Yehova Mulungu. Mawu a Solomo opezeka palemba la 2 Mbiri 6:29, 30 angatilimbikitse kwambiri.

Lembali likunena za pemphero la Solomo potsegulira kachisi ku Yerusalemu mu chaka cha 1026 B.C.E. Pemphero lakeli linatenga mwina mphindi 10 ndipo iye anatamanda Yehova kuti ndi Mulungu wokhulupirika, Wokwaniritsa malonjezo ndiponso Wakumva pemphero.​—1 Mafumu 8:23-53; 2 Mbiri 6:14-42.

Mwachitsanzo, Solomo anachonderera Mulungu kuti aziyankha mapembedzero a olambira Ake. (Vesi 29) Choncho ngakhale kuti Solomo anatchula mavuto ambiri (Vesi 28), iye anadziwanso kuti wolambira Yehova aliyense amadziwa “mliri wake” ndipo amamva “ululu wake.” Zimenezi zikutanthauza kuti munthu wina angakhale ndi vuto losiyana ndi limene wina ali nalo.

Kaya akukumana ndi mavuto atani, anthu oopa Mulungu sayenera kuthana nawo okha mavutowo. M’pemphero lake Solomo ankaganiza za wolambira Yehova amene ‘akutambasula manja ake’ chifukwa cha zimene zamuchitikira ndipo akupemphera kwa Yehova ndi mtima wonse. * Mwina apa Solomo anakumbukira atate wake Davide, amene pa nthawi ina atasautsika kwambiri ananena kuti: “Umutulire Yehova nkhawa zako.”​—Salimo 55:4, 22.

Kodi Yehova akanayankha bwanji mapemphero a anthu amene amupempha mochokera pansi pa mtima? Solomo anapempha Yehova kuti: “Inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika, ndipo mukhululuke ndi kuchitapo kanthu. Mupatse aliyense malinga ndi njira zake zonse.” (Vesi 30) Solomo ankadziwa kuti “Wakumva pemphero” amasamalira olambira ake osati ngati gulu basi, komanso aliyense payekha. (Salimo 65:2) Yehova amathandiza anthu m’njira zosiyanasiyana kuphatikizapo kukhululukira munthu amene walapa ndi mtima wonse ndipo akufuna kubwerera kwa iye.​—2 Mbiri 6:36-39.

Kodi n’chifukwa chiyani Solomo sanakayike kuti Yehova adzayankha mapemphero a anthu ochimwa amene alapa? Popitiriza pemphero lake Solomo anati: “Popeza [inu Yehova] mukudziwa mtima wake (popeza inu nokha ndiye mumadziwa bwino mtima wa ana a anthu).” Yehova amadziwa mliri kapena ululu umene wolambira wake aliyense wokhulupirika akumva mumtima mwake ndipo sasangalala wolambira wake akamakumana ndi mavuto.​—Salimo 37:4.

Pemphero la Solomo limeneli ndi lolimbikitsa kwambiri. Nthawi zina anthu anzathu sangamvetse ‘mliri ndi ululu wathu’ kapena kuti mmene tikumvera mumtima mwathu. (Miyambo 14:10) Koma Yehova amadziwa mitima yathu ndipo amatidera nkhawa kwambiri. Kupemphera kwa iye mochokera pansi pa mtima kungatithandize kupirira mavuto amene tikukumana nawo. Baibulo limati: ‘Mum’tulire nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’​—1 Petulo 5:7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Kale munthu ‘akatambasula manja’ atawakweza m’mwamba chinali chizindikiro chosonyeza kuti akupemphera.​—2 Mbiri 6:13.