Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kucheza ndi Mnzathu Kodi Mzimu Woyera N’chiyani?

Kucheza ndi Mnzathu Kodi Mzimu Woyera N’chiyani?

 Kucheza ndi Mnzathu Kodi Mzimu Woyera N’chiyani?

A MBONI ZA YEHOVA amakonda kukambirana ndi anzawo nkhani za m’Baibulo. Kodi muli ndi funso lililonse pa nkhani ya m’Baibulo limene mumafuna kudziwa yankho lake? Kodi mumafuna kudziwa zikhulupiriro ndiponso zinthu zina zimene Mboni za Yehova zimachita? Ngati ndi choncho, musachedwe kufunsa a Mboni za Yehova mukakumana nawo. Adzasangalala kukambirana nanu nkhani zimenezi.

Tiyeni tione mmene wa Mboni za Yehova angachezere ndi munthu wina. Tiyerekeze kuti bambo ena a Mboni za Yehova dzina lawo a Phiri afika pakhomo pa a Banda.

Kodi Mukuganiza Kuti “Mzimu Woyera” N’chiyani?

A Banda: Ndinamvapo anthu ena akunena kuti Mboni za Yehova si Akhristu ndipo simukhulupirira kuti kuli mzimu woyera.

A Phiri: Choyamba ndikufuna kukutsimikizirani kuti ndife Akhristu ndithu. Ndabwera pakhomo panu pano lero, chifukwa chakuti ndimakhulupirira Yesu Khristu. Ndipotu Yesu ndi amene analamula otsatira ake kuti azilalikira. Koma ndikufunseni kaye. Mukanena kuti “mzimu woyera” kodi mukutanthauza chiyani?

A Banda: Ndikunena za Mulungu mzimu kapena kuti mthandizi amene Yesu analonjeza kuti adzatitumizira. Chikhulupiriro chakuti kuli mzimu woyera n’chofunika kwambiri kwa ine. Ndimafuna kuti mzimu woyera uzinditsogolera pa moyo wanga.

A Phiri: Anthu ambiri amaganiza choncho. M’mbuyomu ndinafufuzapo zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya mzimu woyera. Ngati muli ndi nthawi yochepa, bwanji ndikufotokozereni zimene ndinapeza?

A Banda: Chabwino fotokozani.

A Phiri: Koma tidziwane kaye. Ine dzina langa ndine Phiri. Nanga inu dzina lanu ndani?

A Banda: Ndine Banda.

A Phiri: Zikomo kwambiri. Kuti ndisakuwonongereni nthawi yambiri tiyeni tikambirane mfundo imodzi yokha. Ndikugwirizana ndi zimene mwanena poyamba paja kuti mzimu woyera ndi mthandizi amene Yesu anatilonjeza. Koma kodi mukutanthauza kuti mzimu woyera nawonso ndi Mulungu?

A Banda: Inde. N’zimene ndinaphunzira.

Kodi Mzimu Woyera Ndi Munthu?

A Phiri: Tiyeni tione nkhani ina ya m’Baibulo imene ingatithandize kudziwa ngati mzimu woyera ndi munthu kapena ayi. Mwina inunso mukuidziwa bwino nkhani ya m’mavesi amenewa. Pa Machitidwe 2:1-4 pali mawu akuti: “Tsopano pa tsiku la chikondwerero cha Pentekosite, onse anali atasonkhana pamalo amodzi. Mwadzidzidzi kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo unadzaza m’nyumba yonse imene iwo anakhalamo. Pamenepo anaona malawi amoto ooneka ngati malilime,  ndipo anagawanika ndi kukhala pa aliyense wa iwo limodzilimodzi. Ndiyeno onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo anayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana, monga mmene mzimuwo unawachititsira kulankhula.”

A Banda: Nkhani imeneyi ndikuidziwa bwino kwambiri.

A Phiri: Ndiyeno ndikufunseni, kodi munthu angadzazidwe ndi munthu wina?

A Banda: Ayi. Zimenezo sizingachitike.

A Phiri: Tiyeni tionenso bwinobwino vesi 17 la chaputala chomwechi. Mbali yoyamba ya vesili imati: “‘M’masiku otsiriza,’ akutero Mulungu, ‘ndidzatsanulira mbali ya mzimu wanga pa anthu osiyanasiyana.’” Ndiye ndikufunseninso. Kodi ndiye kuti Mulungu anatsanula mbali ina ya Mulungu wina wofanana naye?

A Banda: Ayi.

A Phiri: Yohane M’batizi anagwiritsa ntchito mawu ena pofotokoza za kudzazidwa ndi mzimu woyera. Mawu amenewa ali pa Mateyu 3:11. Kodi mungawerenge lemba limeneli?

A Banda: “Inetu ndikukubatizani m’madzi chifukwa cha kulapa kwanu, koma amene akubwera m’mbuyo mwanga ndi wamphamvu kuposa ine, ndipo sindili woyenera kumuvula nsapato zake. Ameneyo adzakubatizani ndi mzimu woyera komanso ndi moto.”

A Phiri: Zikomo kwambiri. Kodi mwaona zimene Yohane M’batizi ananena kuti zidzachitika ndi mzimu woyera?

A Banda: Ananena kuti anthu adzabatizidwa ndi mzimu woyera.

A Phiri: Zoona. Koma ananenanso kuti anthu adzabatizidwa ndi moto si choncho? Monga tonse tikudziwira, moto si munthu. Kodi vesi limeneli likusonyeza kuti mzimu woyera ndi munthu?

A Banda: Ayi.

A Phiri: Choncho malinga ndi malemba amene takambiranawa, mzimu woyera si munthu eti?

A Banda: Komadi ee.

Kodi Mzimu Woyera Ungakhale Bwanji “Mthandizi”?

A Phiri: Poyamba paja munanena mawu akuti “mthandizi”. Pa Yohane 14:26, Yesu ananena kuti mzimu woyera ndi “mthandizi.” Tiyeni tiwerenge lembali. “Koma mthandizi, amene ndi mzimu woyera, amene Atate wanga adzatumiza m’dzina langa, adzakuphunzitsani zinthu zonse ndi kukukumbutsani zonse zimene ndinakuuzani.” Anthu ena amaganiza kuti lemba limeneli limatsimikizira zoti mzimu woyera ndi munthu ndipo ungatithandize ndiponso kutiphunzitsa.

A Banda: Mwanena zoona. Inenso ndimakhulupirira zimenezo.

A Phiri: N’kutheka kuti pamenepa Yesu ankanena mawu ophiphiritsa. Taonani zimene Yesu ananena pa nkhani ya nzeru pa Luka 7:35. Iye anati: “Mulimonsemo, nzeru imatsimikizirika kukhala yolungama mwa ana ake onse.” (Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu) Kodi pamenepa tinganene kuti nzeru ndi munthu weniweni ndipo ingakhale ndi ana?

A Banda: Ayi. Pamenepadi mawu amenewa ndi ophiphiritsa.

A Phiri: Zoona. Yesu ankatanthauza kuti nzeru imadziwika ndi zotsatira zake. Baibulo lili ndi mawu ophiphiritsa ofotokoza zinthu zina ngati kuti n’zamoyo. Ifenso timatha kugwiritsa ntchito mawu oterewa pocheza ndi anzathu. Mwachitsanzo, m’mawa dzuwa likuwala, kodi mungadabwe munthu akunena kuti, “Tsegulani mawindo kuti dzuwa lizilowa”?

A Banda: Ayi. Inenso ndikhoza kunena zimenezo.

A Phiri: Kodi ponena zimenezi mungakhale mukutanthauza kuti dzuwalo ndi munthu amene angabwere m’nyumba mwanu ngati mlendo?

A Banda: Ayi. Kumeneku ndi kulankhula mophiphiritsa basi.

A Phiri: Ndiyeno kodi mwina Yesu ankalankhula mawu ophiphiritsa pamene ananena kuti mzimu woyera ndi mthandizi ndiponso mphunzitsi?

A Banda: Ndikuganiza choncho. Mfundo imeneyi ikugwirizana ndi malemba amene  mwawerenga onena kuti mzimu unatsanulidwa ndiponso kuti anthu anabatizidwa ndi mzimu woyera. Tsopano popeza mzimu woyera si munthu, kodi tingati mzimuwo n’chiyani?

Kodi Mzimu Woyera N’chiyani?

A Phiri: Yesu anafotokoza tanthauzo la mzimu woyera pa Machitidwe 1:8. Tawerengani lemba limeneli.

A Banda: “Koma mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”

A Phiri: Pa lembali Yesu anagwirizanitsa mzimu woyera ndi mphamvu. Ndiyeno malinga ndi malemba amene tawerenga aja, kodi mphamvu imeneyi imachokera kuti?

A Banda: Kwa Mulungu Atate.

A Phiri: Mwanena zoona. Mzimu woyera ndi mphamvu imene Mulungu anagwiritsa ntchito polenga zinthu zonse. M’Baibulo pa Genesis 1:2 pali mawu akuti: “Mphamvu ya Mulungu inali kuyendayenda pamwamba pa madzi akuyawo.” Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “mphamvu” angatanthauzenso “mzimu.” Mzimu umenewu ndi mphamvu yosaoneka imene Mulungu amagwiritsa ntchito pokwaniritsa zimene akufuna. Mwina ndingokuonetsaninso lemba lina loti muliganizire. Tawerengani Luka 11:13.

A Banda: “Choncho ngati inu, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Ndithudi iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.”

A Phiri: Ngati Atate wathu wakumwamba amagwiritsa ntchito mzimu woyera ndiponso kuupereka kwa anthu amene amapempha, kodi pamenepa mzimuwo ungakhale wofanana ndi Atatewo?

A Banda: Oo, tsopano ndamvetsa.

A Phiri: Koma ndisakuchedwetseni poti munanena kuti muli ndi nthawi yochepa. Tsopano tisanamalize kuchezaku ndikufuna ndikufunseni. Malinga ndi malemba amene takambirana, kodi munganene kuti mzimu woyera ndi chiyani?

A Banda: Ndi mphamvu imene Mulungu amaigwiritsa ntchito.

A Phiri: Eyaa! Mfundo yake ndi imeneyo. Pa Yohane 14:26, pamene Yesu ananena kuti mzimu woyera ndi mthandizi kapena mphunzitsi, iye anagwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa ofotokoza mzimuwo ngati kuti ndi munthu.

A Banda: Ine sindimadziwa zimenezi.

A Phiri: Koma palinso mfundo ina yolimbikitsa imene tingaphunzire pa mawu a Yesu.

A Banda: Ndi mfundo iti imeneyo?

A Phiri: Tikhoza kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu woyera kuti utithandize ngati takumana ndi mavuto. Tikhozanso kumupempha kuti atipatse mzimuwo kuti utithandize kumvetsa choonadi chonena za Mulunguyo.

A Banda: Mfundo imeneyi ndi yochititsa chidwi kwambiri. Ndiiganizira mofatsa.

A Phiri: Koma ndisanapite, pali mfundo inanso yofunika kuiganizira mofatsa. Taona kuti mzimu woyera ndi mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito pofuna kukwaniritsa chilichonse chimene akufuna eti?

A Banda: Inde.

A Phiri: Nanga n’chifukwa chiyani sagwiritsa ntchito mphamvu yopanda malireyi kuthetsera mavuto ndi zinthu zoipa zonse zimene zafala m’dzikoli? Kodi munaganizirapo funso limeneli? *

A Banda: Ee, ndinaliganizirapo.

A Phiri: Bwanji ndidzabwere mlungu wamawa nthawi ngati yomwe ino kuti tidzakambirane?

A Banda: Mudzabwere, mudzandipeza.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 59 Kuti mumve zambiri, werengani mutu 11 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.