Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi a Mboni za Yehova Amachita Machiritso?

Kodi a Mboni za Yehova Amachita Machiritso?

 Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi a Mboni za Yehova Amachita Machiritso?

▪ A Mboni za Yehova sanachitepo machiritso kuyambira kale. Mofanana ndi Yesu, iwo amakhulupirira kuti ntchito yawo yaikulu ndi kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Amakhulupiriranso kuti pali chinthu china chofunika kwambiri chimene chimadziwikitsa Akhristu oona, osati machiritso.

Kunena zoona tonsefe timadziwa kuti zimene Yesu Khristu anachita pochiritsa anthu mwachifundo m’nthawi yake, zili ndi tanthauzo lofunika kwambiri. Zimene anachitazo zinatitsimikizira kuti akadzayamba kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”​—Yesaya 33:24.

Koma nanga bwanji masiku ano? Anthu ena m’Matchalitchi Achikhristu komanso m’zipembedzo zina amanena kuti amachiritsa anthu mozizwitsa. Koma Yesu anachenjezeratu mwamphamvu anthu onse amene azidzanena kuti amachita “zodabwitsa zambiri” m’dzina lake. Iye anati adzawauza kuti: “Sindinakudziweni inu. Chokani kwa ine, inu ochita zoipa.” (Mateyu 7:22, 23, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Ndiyeno kodi zimene anthu masiku ano amati ndi machiritso, ndi umboni wakuti Mulungu akuwavomereza kapena kuwadalitsa?

Taganizirani zimene Baibulo limanena zokhudza kuchiritsa kumene Yesu anachita. Tikayerekeza nkhani za m’Baibulo zimenezi, ndi zimene ochiritsa a masiku ano amachita, n’zosavuta kudziwa ngati machiritso a masiku ano amachokera kwa Mulungu kapena ayi.

Yesu sanagwiritse ntchito mphamvu yochiritsa pofuna kukopa anthu ambiri kuti akhale otsatira ake. M’malomwake, iye anachiritsa anthu ena pamalo posaonekera kwa anthu. Komanso nthawi zambiri iye ankauza anthu amene wawachiritsawo kuti asakauze aliyense.​—Luka 5:13, 14.

Yesu sankalipiritsa akachita chozizwitsa. (Mateyu 10:8) Ndiponso iye sanalepherepo kuchiritsa aliyense. Odwala onse amene anabwera kwa iye anawachiritsa matenda awo onse, ndipo sizinkadalira kuti munthuyo ali ndi chikhulupiriro kapena ayi. (Luka 6:19; Yohane 5:5-9, 13) Kuwonjezera pamenepo, Yesu anaukitsanso akufa.​—Luka 7:11-17; 8:40-56; Yohane 11:38-44.

Koma ngakhale kuti Yesu ankachita zozizwitsa, cholinga cha utumiki wake si chinali kukopa anthu ndi zozizwitsazo. M’malomwake, ntchito yake yaikulu inali kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Yesu anakonzanso zoti otsatira ake akaphunzitse ena za chiyembekezo cha moyo wathanzi mu Ufumu wa Mulungu.​—Mateyu 28:19, 20.

N’zoona kuti ena mwa otsatira a Yesu m’nthawi ya atumwi anali ndi mphatso zapadera zochiritsa, koma mphatso zimenezi zinali zoti zidzatha. (1 Akorinto 12:29, 30; 13:8, 13) Akhristu enieni masiku ano amadziwika chifukwa cha chikondi chopanda mpeni kumphasa, osati chifukwa chochiritsa anthu mozizwitsa. (Yohane 13:35) Kuchiritsa mozizwitsa kwa masiku ano sikunathandize kuti pakhale gulu la Akhristu enieni, ochokera m’mitundu ndi zikhalidwe zosiyanasiyana amene akukhala mogwirizana chifukwa cha chikondi chimenechi.

Komano pali gulu linalake la Akhristu ogwirizana chifukwa chokondana kwambiri moti amakaniratu kuchita chilichonse choipa kwa Akhristu anzawo ndiponso anthu ena, zivute zitani. Kodi Akhristu amenewa ndi ati? Ndi a Mboni za Yehova. Padziko lonse, a Mboni za Yehova amadziwika kuti ali ndi chikondi ngati cha Khristu. Kugwirizanitsa anthu amafuko, mitundu ndi zikhalidwe zosiyanasiyana ndi chozizwitsa. Mzimu woyera wa Mulungu ndi umene umachititsa kuti zimenezi zitheke. Tikukupemphani kuti mukakhale nawo pa umodzi mwa misonkhano yawo kuti mukaone nokha zimene tikunenazi.

[Chithunzi patsamba 13]

Kodi anthu ochita za machiritso masiku ano (ngati amene ali kudzanja lamanja) amathandizidwadi ndi Mulungu?