Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Anapitiriza Kukula, Akukondedwa ndi Yehova”

“Anapitiriza Kukula, Akukondedwa ndi Yehova”

 Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

“Anapitiriza Kukula, Akukondedwa ndi Yehova”

SAMUELI anayang’anitsitsa Aisiraeli anzake. Mtundu wa Isiraeli unali utasonkhana m’tawuni ya Giligala, ataitanidwa ndi mwamuna wokhulupirika ameneyu. Iye anali atatumikira monga mneneri komanso woweruza kwa zaka zambiri. Pa kalendala yathu ya masiku ano, umenewu unali mwezi wa May kapena June ndipo nyengo ya chilimwe n’kuti itayamba kale. Tirigu m’minda ya m’derali anali atakhwima, wongodikira kukololedwa. Pa nthawiyi anthu anangoti duu. Kodi pamenepa Samueli akanatani kuti zolankhula zake zikhale zogwira mtima kwa anthuwa?

Aisiraeli anaumirira kuti akufuna munthu wina woti akhale mfumu yawo. Koma iwo sankadziwa kuopsa kwa zimene ankafunazo. Sanadziwenso kuti akunyoza kwambiri Mulungu wawo Yehova komanso mneneri wake. Pamenepa tingati iwo anakana kuti Yehova akhale Mfumu yawo. Ndiyeno kodi Samueli akanatani kuti athandize anthuwo kulapa?

Kenako Samueli anauza khamu la anthulo kuti: “Ine, ndakalamba ndipo ndachita imvi.” Tsitsi lake, lomwe pa nthawiyi lonse linalidi laimvi, linathandiza anthu kuona kuti zimene Samueli akunenazo ndi zoona. Kenako iye anati: “Ine ndatumikira Mulungu ndi kukutsogolerani kuyambira pa ubwana wanga, mpaka lero.” (1 Samueli 11:14, 15; 12:2) Ngakhale kuti Samueli anali wokalamba, iye ankakumbukirabe zimene zinkachitika ali mwana. Zimene anasankha kuchita kalelo ali mnyamata zinachititsa kuti pa moyo wake wonse akhale munthu wachikhulupiriro ndiponso wodzipereka kwa Mulungu wake Yehova.

Ngakhale kuti ankakhala ndi anthu opanda chikhulupiriro komanso osakhulupirika, nthawi ndi nthawi Samueli ankafunika kulimbitsa chikhulupiriro chake. Masiku anonso, ndi zovuta kukhala ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa tikukhala m’dziko loipa ndiponso anthu ndi opanda chikhulupiriro. Tiyeni tione zimene tikuphunzira kwa Samueli kuyambira ali mwana.

“Kutumikira Pamaso pa Yehova, Ali Mwana”

Zimene zinachitika Samueli ali mwana zinali zapadera. Iye anasiya kuyamwa atatsala pang’ono kukwanitsa zaka zinayi kapena zitapitirira pang’ono. Atangosiya kuyamwa, anayamba kutumikira pa chihema chopatulika cha Yehova ku Silo, mtunda wa makilomita 30 kuchokera kwawo ku Rama. Bambo ake a Elikana ndi mayi ake a Hana anamupereka kuti akatumikire Yehova mwapadera ndipo zimenezi zinachititsa kuti Samueli akhale Mnaziri kwa moyo wake wonse. * Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti makolo a Samueli sankamukonda ndiponso anangomutaya?

Ayi ndithu. Iwo ankadziwa kuti mwana wawoyu azikasamalidwa bwinobwino ku Silo. Popeza kuti Samueli ankagwira ntchito ndi Mkulu wa Ansembe Eli, n’zosakayikitsa kuti Eli ankaonetsetsa kuti Samueli akusamalidwa bwino. Panalinso azimayi angapo amene ankathandiza nawo zinthu zina ndi zina pachihema chopatulika ndipo ankagwira ntchitoyo motsatira dongosolo linalake.​—Ekisodo 38:8.

Komanso Hana ndi Elikana sanamuiwale mwana wawo woyambayu, yemwe kubadwa kwake kunasonyeza kuti Mulungu wayankha pemphero lawo. Hana anali atapempha Mulungu kuti amuthandize kuti akhale ndi mwana wamwamuna ndipo analonjeza kuti adzapereka mwanayo kwa Mulungu kuti azikamutumikira. Chaka chilichonse Hana ankapita kukamuona Samueli ndipo ankamupititsira malaya atsopano amene wamusokera kuti azikavala potumikira pachihema chopatulika. N’zosachita kufunsa kuti  mwanayu ankasangalala kwambiri mayi ake akadzamuona. Makolo ake ankamulimbikitsa, kumuphunzitsa ndiponso kumulangiza kuti aziona kuti ndi mwayi waukulu kutumikira Yehova pamalo amenewo. N’zosakayikitsa kuti zimenezi zinamuthandiza kwambiri kuti azichita bwino pa utumiki wake.

Masiku ano makolo angaphunzire zambiri kwa Hana ndi mwamuna wake Elikana. Makolo ambiri amalera ana n’cholinga chakuti mwana wawoyo akadzakula azidzawapezera zinthu zofunika pamoyo ndipo saganizira za zinthu zauzimu. Koma mosiyana ndi zimenezi, makolo a Samueli anaika zinthu zauzimu patsogolo ndipo zimenezi zinathandiza kwambiri kuti mwana wawoyo atakula akhalenso wokonda kwambiri zinthu zauzimu.​—Miyambo 22:6.

Tingathe kuona m’maganizo mwathu mwana ameneyu akukula ndiponso akuyendayenda m’dera lamapiri ku Silo n’cholinga choti adziwe bwinobwino malowo. Mwina Samueli akayang’anitsitsa tawuni ya Silo imene inali m’chigwa, n’kuonanso chihema cha Yehova chimene chinali pafupi ndi tawuniyi, ankasangalala ndiponso kunyadira kwambiri. Chihema chimenechi chinalidi malo opatulika. * Chinali chitamangidwa zaka pafupifupi 400 m’mbuyomo ndipo amene anatsogolera ntchito yomanga chihemachi anali Mose. Chihema chopatulikachi chinali malo okhawo padziko lonse kumene anthu ankapita kukalambira Mulungu woona, Yehova.

Kuyambira ali mwana, Samueli ankakonda kwambiri chihema chopatulikachi. Mu nkhani ina imene iye analemba timawerenga kuti: “Samueli anali kutumikira pamaso pa Yehova, ali mwana ndipo anali kuvala efodi wansalu.” (1 Samueli 2:18) Efodi ameneyu chinali chovala chopanda manja ndipo zikuoneka kuti n’chimene chinkadziwikitsa Samueli kuti amagwira ntchito yothandiza ansembe kuchihema. Ngakhale kuti Samueli sanali wansembe, iye ankagwira ntchito imene inaphatikizapo kutsegula zitseko zolowera m’bwalo la chihema chopatulika m’mawa uliwonse ndiponso kutumikira Eli amene anali wokalamba. Komabe ngakhale kuti iye ankasangalala kugwira ntchito imeneyi, patapita nthawi anayamba kuvutika mumtima mwake chifukwa zinthu zina sizinkayenda bwino panyumba ya Yehova.

Anakhalabe Woyera Ngakhale Kuti Ankakhala ndi Anthu Oipa

Samueli ali mwana, anaona anthu akuchita zinthu zoipa komanso zachinyengo kwambiri. Eli anali ndi ana aamuna awiri, Hofeni ndi Pinihasi. Samueli analemba kuti: “Ana aamuna a Eli anali anthu opanda pake. Iwo anali kunyalanyaza Yehova.” (1 Samueli 2:12) Mfundo ziwiri zimene zatchulidwa m’vesi limeneli n’zogwirizana kwambiri. Hofeni ndi Pinihasi anali “anthu opanda pake,” kapena kuti “ana achabechabe” chifukwa ankanyalanyaza Yehova. Iwo sankaganizirako n’komwe mfundo zolungama za Yehova ndiponso zimene iye amafuna. Zimenezi n’zimene zinachititsa kuti azichitanso machimo ena ambirimbiri.

Chilamulo cha Mulungu chinali ndi malangizo osapita m’mbali onena za ntchito ya ansembe ndiponso mmene angaperekere nsembe pachihema chopatulika. Yehova anapereka malangizowa pa zifukwa zabwino kwambiri. Zili choncho chifukwa nsembe zimenezi zinaimira dongosolo limene Mulungu anakonza loti akhululukire anthu machimo ndi kuyamba kuwaonanso kuti ndi oyera ndiponso oyenera kuwadalitsa ndi kuwatsogolera. Koma Hofeni ndi Pinihasi anatsogolera ansembe anzawo kuchita zinthu zosalemekeza nsembe zimene anthu ankapereka. *

Kodi mukuganiza kuti Samueli, yemwe pa nthawiyi anali wachinyamata, ankamva bwanji kuona zinthu zoipa choncho zikupitirira kuchitika? Samueli ayenera kuti ankaona anthu ambiri osauka, ankhawa komanso oponderezedwa akubwera kudzapereka nsembe zawo kuchihema chopatulika. Koma m’malo molimbikitsidwa mwauzimu, anthuwa ankachoka kuchihemako ali okhumudwa komanso atachititsidwa manyazi  kwambiri. Kodi Samueli anamva bwanji atamva kuti Hofeni ndi Pinihasi ankaswanso malamulo a Yehova pochita zachiwerewere ndi ena mwa azimayi amene ankatumikiranso kuchihema komweko? (1 Samueli 2:22) Mwina iye ankayembekezera kuti Eli achitapo kanthu kuti zimenezi zisapitirire.

Eli anali ndi mphamvu zoletsa makhalidwe oipa amenewa. Popeza anali mkulu wa ansembe, iye anali ndi udindo woyang’anira zochitika zonse pachihema chopatulikacho. Komanso monga bambo, iye anali ndi udindo wopereka chilango kwa ana akewo. Ndipotu zimene anawa ankachita kunali kungodzipweteka okha komanso kuvulaza anthu ena ambirimbiri m’dzikolo. Koma Eli analephera kukwaniritsa udindo wake monga mkulu wa ansembe komanso bambo. Iye anangodzudzula ana ake mowanyengerera. (1 Samueli 2:23-25) Koma anawo ankafunika kuwapatsa chilango chokhwima kwambiri chifukwa zimene ankachitazo chilango chake chinali kuphedwa.

Zinthu zinafika poipa kwambiri moti Yehova anatumiza mneneri wina kwa Eli kuti akamuuze uthenga wamphamvu kwambiri wonena za chiweruzo cha Yehova. Mneneriyu sanatchulidwe dzina lake, koma Baibulo limangomutchula kuti “munthu wa Mulungu.” Yehova anauza Eli kuti: ‘Ukulemekezabe ana ako kuposa ine.’ Chifukwa cha zimenezi, Mulungu anauza Eli kuti ana ake oipawo adzafa onse tsiku limodzi ndiponso kuti banja la Eli lidzakumana ndi mavuto akulu mpaka anthu a m’banjalo sadzakhalanso ndi mwayi wotumikira ngati ansembe. Kodi uthenga wa mphamvu umenewu anathandiza kuti zinthu zisinthe m’banja limeneli? Baibulo limasonyeza kuti zinthu sizinasinthe.​—1 Samueli 2:27–3:1.

Kodi makhalidwe oipa amenewa anamukhudza bwanji Samueli? Baibulo limasonyeza kuti pa nthawi yonse imene zinthu zomvetsa chisonizi zimachitika, Samueli ankachita zinthu zabwino ndipo anakula akukonda kwambiri zinthu zauzimu. Kumbukirani kuti pa 1 Samueli 2:18 timawerenga kuti Samueli ‘anali kutumikira mokhulupirika pamaso pa Yehova, ali mwana.’ Choncho, ngakhale pamene anali mwana, Samueli ankakonda kwambiri kutumikira Mulungu. Vesi 21 limanena mfundo ina yolimbikitsa kwambiri. Limati: “Mwanayo Samueli anapitiriza kukula, akukondedwa ndi Yehova.” Pamene ankakula, chikondi chake pa Atate wake wakumwamba chinali kukulanso kwambiri. Ubwenzi wolimba kwambiri umenewu ndi Yehova, ndi umene umatiteteza kwambiri kuti tisatengere zoipa zilizonse zimene zimachitika.

Samueli akanatha kuganiza kuti ngati mkulu wa ansembe ndiponso ana ake akuchita machimo, ndiye kuti palibe vuto ngati nayenso atamachita zilizonse zimene akufuna. Koma anthu ena, kuphatikizapo amene ali ndi udindo, akamachita zinthu zoipa, si chifukwa choti nafenso tizichita zoipa. Masiku ano Akhristu achinyamata ambiri amatsatira chitsanzo cha Samueli ndipo ‘akupitirizabe kukula ndi Yehova,’ ngakhale akukhala ndi anthu ena amene akuchita zoipa.

Kodi khalidwe labwino la Samueli linamuthandiza bwanji? Timawerenga kuti: “Izi zili choncho, mwanayo Samueli anali kukula ndi kukondedwa kwambiri ndi Yehova komanso anthu.” (1 Samueli 2:26) Choncho Samueli ankakondedwa ndi anthu amene analinso ndi makhalidwe abwino. Komanso Yehova anasangalala kwambiri ndi kukhulupirika kwa mnyamata ameneyu. Mosakayikira, Samueli ankadziwa kuti Mulungu adzachitapo kanthu pa zoipa zimene zinkachitika ku Silo. Koma mwina ankadabwa kuti Mulungu adzachitapo kanthu liti.

“Lankhulani, Ine Mtumiki Wanu Ndikumvetsera”

Tsiku lina usiku, mafunso a Samueli anayankhidwa. Unali m’mawa kwambiri, kudakali mdima. Pa nthawiyi n’kuti nyali yaikulu ya m’chihemamo ikuwalabe. Kenako Samueli anamva wina akumuitana. Iye anaganiza kuti ndi Eli yemwe pa nthawiyi anali wokalamba ndiponso ankaona movutikira zedi. Samueli anaimirira ndipo “anathamangira kwa Eli.” Mwina mnyamatayu anadzuka mwamsangamsanga, osavala ndi nsapato zomwe, kuthamangira kwa Eli kuti akamve chimene akumuitanira. N’zochititsa chidwi kuona kuti Samueli ankalemekezabe kwambiri Eli ndiponso ankamuchitira zinthu zosonyeza kukoma mtima. Samueli ankadziwa kuti ngakhale kuti Eli ankachita zinthu zoipa zonsezi, iye anali adakali mkulu wa ansembe wa Yehova.​—1 Samueli 3:2-5.

Samueli anamudzutsa Eli n’kumuuza kuti: “Ndabwera mbuyanga, ndamva kuitana.” Koma Eli ananena kuti sanamuitane ndipo anamuuza kuti akagone. Samueli anamvanso kuitana ndipo anapitanso kwa Eli. Ndipo zinachitikanso kachitatu. Pa mapeto pake Eli anazindikira chimene chinkachitika. Chifukwa cha zimene zinkachitika pachihema chopatulika, Yehova sankalankhulanso pafupipafupi ndi anthu m’masomphenya kapena kuwatumizira uthenga waulosi. Koma Eli anadziwa kuti tsopano Yehova wayambanso kulankhula ndi anthu kudzera mwa mwanayu. Eli anauza Samueli kuti apite kukagona ndipo anamulangiza mmene angayankhire akamvanso kuitana. Samueli anamvera. Pasanapite nthawi anamvanso kuitana kuti: “Samueli, Samueli!” Mwanayo anayankha  kuti: “Lankhulani, ine mtumiki wanu ndikumvetsera.”​—1 Samueli 3:1, 5-10.

Tsopano Yehova anapeza mtumiki wake ku Silo amene anali kumumvetsera. Samueli anapitirizabe kumvera Yehova kwa moyo wake wonse. Kodi nanunso mumamvera Yehova? Sitichita kufunikira kumva Mulungu akutiitana usiku chifukwa masiku ano tikhoza kumva mawu a Mulungu nthawi ina iliyonse. Tili ndi Baibulo lonse lomwe ndi Mawu a Mulungu. Tikamamvetsera Mulungu n’kumachita zimene akutiuza, tidzakhala ndi chikhulupiriro cholimba. Zimenezi ndi zimene zinachitika kwa Samueli.

Zimene zinachitika usiku umenewo zinasintha kwambiri moyo wa Samueli. Tikutero chifukwa kuyambira nthawi imeneyo iye anayamba kudziwa Yehova mwapadera kwambiri ndipo anakhala mneneri wake komanso womulankhulira. Poyamba mnyamatayu anachita mantha kuuza Eli uthenga wa Yehova, popeza unali wonena kuti ulosi wa chiweruzo cha Yehova ku banjali watsala pang’ono kukwaniritsidwa. Koma Samueli analimba mtima n’kuuza Eli uthengawo ndipo Eli modzichepetsa anavomereza chiweruzo cha Mulungu. Pasanapite nthawi, zonse zimene Yehova ananena zinachitikadi. Aisiraeli anamenyana ndi Afilisiti ndipo Hofeni ndi Pinihasi anaphedwa pa tsiku limodzi. Nayenso Eli anafa atamva kuti adani alanda Likasa lopatulika la Yehova.​—1 Samueli 3:10-18; 4:1-18.

Koma Samueli anapitirizabe kudziwika kuti anali mneneri wokhulupirika. Nkhaniyo imati: “Yehova anali naye.” Imanenanso kuti Yehova anakwaniritsa ulosi wina uliwonse wa Samueli.​—1 Samueli 3:19.

“Samueli Anafuulira Yehova”

Komabe, kodi zimenezi zikutanthauza kuti Aisiraeli anamvera malangizo a Samueli n’kukhala anthu okonda zinthu zauzimu ndiponso okhulupirika? Ayi. Patapita nthawi ananena kuti sakufuna kuti azitsogoleredwa ndi mneneri basi. Iwo anati akufuna munthu woti akhale mfumu yawo ngati mmene zinaliri ndi anthu a mitundu ina. Yehova anauza Samueli kuti awapatse mfumu imene anapemphayo. Koma anayeneranso kuwauza Aisiraeli kuopsa kwa tchimo lawo pa zimene anasankhazo. Aisiraeli sanakane Samueli koma anakana Yehova. Choncho, Samueli anaitanira Aisiraeli onse ku Giligala kuti akambirane nawo nkhani yofunika kwambiriyi.

 Ndiye tiyeni tione zimene zinachitika kumeneko. Tsiku limeneli Samueli, amene pa nthawiyi anali wokalamba, anakumbutsa Aisiraeli kuti watumikira Mulungu mokhulupirika pa moyo wake wonse. Kenako timawerenga kuti: “Samueli anafuulira Yehova,” kumupempha kuti abweretse mvula yamabingu.​—1 Samueli 12:17, 18.

Koma kodi mvula yamabingu ikanagwadi m’nyengo yachirimwe imeneyi? Zoterezi zinali zisanachitikepo. Koma ngati panali ena mwa anthuwo amene ankakayikira kapena kumuseka Samueli, anadabwa. Mwadzidzidzi mitambo yamvula inasonkhana. Kunayamba kuwomba mphepo yamphamvu imene inaweramitsa tirigu yense m’minda. Ndiyeno kunagunda mabingu amphamvu, kenako kunagwa chimvula. Kodi anthuwo anachita chiyani? Baibulo limanena kuti: “Anthu onse anachita mantha kwambiri ndi Yehova ndiponso ndi Samueli.” Apa tsopano Aisiraeliwo anazindikira kuti achimwira Mulungu kwambiri.​—1 Samueli 12:18, 19.

Amene anachititsa kuti Aisiraeli azindikire kuti alakwa, sanali Samueli koma Mulungu wake, Yehova. Kungoyambira ali mwana mpaka kukalamba, Samueli anakhulupirira Yehova Mulungu ndipo anadalitsidwa. Mpaka pano Yehova sanasinthe. Iye akuthandizabe anthu amene amatsatira chikhulupiriro cha Samueli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Anaziri anali anthu amene ankalonjeza kuti pa moyo wawo sadzichita zinthu zina zake. Zimenezi zinkaphatikizapo kuti sadzamwa chakumwa chilichonse choledzeretsa ndiponso sadzameta tsitsi lawo. Anthu ambiri ankalonjeza kuti akhala Anaziri kwa kanthawi ndipo ndi anthu ochepa okha monga Samisoni, Samueli ndi Yohane M’batizi amene anakhala Anaziri kwa moyo wawo onse.

^ ndime 12 Chihema chopatulika chinali cha makona anayi, ndipo chinali chongopangidwa ndi matabwa amene anawaphimba ndi chinsalu chachikulu. Koma ngakhale zinali choncho, chihema chopatulikachi anachimanga pogwiritsa ntchito zipangizo zapamwamba kwambiri monga zikopa za akatumbu, nsalu zopetedwa mokongola kwambiri ndiponso matabwa amtengo wapatali okutidwa ndi siliva ndi golide. Kunja kwa chihemachi kunali bwalo limenenso linali la makona anayi. M’bwalomo munalinso guwa lansembe lokongola kwambiri. Zikuoneka kuti patapita nthawi anamanganso zipinda zina za ansembe m’bwalomo. Samueli ayenera kuti ankagona m’chimodzi cha zipinda zimenezi.

^ ndime 16 Nkhani imeneyi imanena zinthu ziwiri zopanda ulemu zimene ana a Eli ankachita. Chilamulo chinaneneratu zigawo za nyama yoperekedwa nsembe zimene ansembe anayenera kudya. (Deuteronomo 18:3) Koma kuchihemako, ansembe oipa amenewo anayamba kuchita zawozawo. Iwo ankauza anthu owathandizira kuti azipisa ndi chifoloko chachikulu m’miphika ya nyama imene inali pamoto ndipo ankatenga nyama iliyonse imene akufuna. Komanso anthu akabweretsa nsembe zawo kuchihema kuti azipereke paguwa la nsembe, ansembe oipawo ankachititsa owathandizira awo kuchitira chipongwe anthu odzapereka nsembewo. Ankachita zimenezi pokakamiza anthu kuti aziwapatsa nyama yosaphika ngakhale asanapereke mafuta a nyamayo ngati nsembe kwa Yehova.​—Levitiko 3:3-5; 1 Samueli 2:13-17.

[Chithunzi patsamba 17]

Ngakhale kuti anali ndi mantha, Samueli anauzabe Eli uthenga wa chiweruzo wochokera kwa Yehova

[Chithunzi patsamba 18]

Samueli anapemphera mwachikhulupiriro ndipo Yehova anayankha pemphero lake pobweretsa chimvula cha mabingu