Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

5 Kodi Tiyenera Kupemphera Pamalo Ati, Nanga Nthawi Yanji?

5 Kodi Tiyenera Kupemphera Pamalo Ati, Nanga Nthawi Yanji?

MWINA mwaonapo kuti anthu a m’zipembedzo zambiri amamanga nyumba zikuluzikulu zopemphereramo ndipo amaika nthawi imene anthu ayenera kukapemphera. Kodi Baibulo limanena kuti tiyenera kupemphera tili pamalo ena ake komanso pa nthawi inayake?

Baibulo limasonyeza kuti pali nthawi zina zimene tiyenera kupemphera. Mwachitsanzo, Yesu asanadye ndi otsatira ake anapemphera kwa Mulungu, kumuyamikira chifukwa cha chakudyacho. (Luka 22:17) Ndipo pamene ophunzira ake anasonkhana kuti alambire Mulungu, anapemphera limodzi. Pamenepa iwo anachita zimene zinkachitika kuyambira kale m’masunagoge a Ayuda ndiponso m’kachisi ku Yerusalemu. Mulungu anafuna kuti kachisi akhale “nyumba yopemphereramo mitundu yonse.”​—Maliko 11:17.

Atumiki a Mulungu akasonkhana pamodzi n’kupemphera, Mulungu angayankhe mapemphero amenewo. Ngati iwo ali ogwirizana mwauzimu ndiponso zimene akunena m’mapemphero awowo zikugwirizana ndi Malemba, Mulungu amakondwera. Ndipo pemphero lingachititse kuti Mulungu achite zinthu zimene mwina sakanachita. (Aheberi 13:18, 19) Nthawi zonse, Mboni za Yehova zimapemphera pamisonkhano yawo imene imachitikira pa Nyumba ya Ufumu. Tikukuitanirani kumisonkhano imeneyi kuti mudzamve mapemphero amenewa.

Komabe Baibulo silineneratu nthawi imene tiyenera kupemphera kapena malo opemphererapo. M’Baibulo muli nkhani za atumiki a Mulungu amene anapemphera nthawi zosiyanasiyana ndiponso pamalo osiyanasiyana. Yesu anati: “Popemphera, lowa m’chipinda chako pawekha ndi kutseka chitseko, ndipo pemphera kwa Atate wako amene ali kosaoneka. Ukatero Atate wako amene amaona kuchokera kosaonekako adzakubwezera.”​—Mateyu 6:6.

Tingapemphere nthawi iliyonse ndiponso kulikonse

Kodi mfundo imeneyi si yolimbikitsa? Mukhoza kupemphera kwa Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse pa nthawi iliyonse komanso muli nokhanokha, ndipo dziwani kuti Mulungu adzamva mapemphero anu. N’chifukwa chake Yesu nthawi zambiri ankapita kwayekha kukapemphera. Pa nthawi ina, iye anachezera usiku wonse kupemphera kwa Mulungu kuti amuthandize kusankha bwino chochita pa nkhani ina yofunika kwambiri.​—Luka 6:12, 13.

Baibulo limanenanso za amuna ndi akazi ena amene anapemphera kwa Mulungu pofuna kuti asankhe bwino zochita pa nkhani zofunika kwambiri kapena pofuna kuti awathandize pa mavuto awo. Nthawi zina anapemphera mokweza mawu koma nthawi zina anapemphera chamumtima. Anapemphera pagulu komanso anapemphera ali pa okha. Komabe chofunika kwambiri n’choti anapemphera. Ndipotu Mulungu amauza atumiki ake kuti: “Muzipemphera mosalekeza.” (1 Atesalonika 5:17) Iye ndi wofunitsitsa kumvetsera mapemphero a anthu amene amachita chifuniro chake ngakhale atapemphera kambiri bwanji. Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Mulungu amatikonda kwambiri?

Komabe, chifukwa cha mmene zinthu zilili m’dzikoli, anthu ena amafuna kudziwa ngati pemphero lili lothandizadi. Mwina inuyo mungafunse kuti, ‘Kodi kupemphera kungandithandizedi?’