Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

4 Kodi Tiyenera Kupemphera za Chiyani?

4 Kodi Tiyenera Kupemphera za Chiyani?

ANTHU ena amanena kuti pa mapemphero onse a Akhristu, pemphero limene limanenedwa mobwerezabwereza ndi pemphero lachitsanzo la Yesu, lomwe ena amalitchula kuti Pemphero la Ambuye kapena la Atate Wathu Wakumwamba. Kaya zimenezi ndi zoona kapena ayi, koma mfundo ndi yakuti pemphero limeneli ndi limodzi mwa mapemphero amene anthu ambiri sawamvetsa. Anthu ambiri analiloweza pa mtima ndipo amalinena tsiku lililonse mwinanso kangapo patsiku. Koma cholinga cha Yesu pophunzitsa anthu pemphero limeneli si chinali chimenechi. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?

Asananene za pemphero limeneli, Yesu ananena kuti: “Popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza.” (Mateyu 6:7) Ndiyeno kodi Yesu akananena mawu amenewa zikanakhala kuti ankafuna kuti anthu azinena pemphero limeneli mobwerezabwereza? Ayi ndithu. Choncho, cholinga cha Yesu chinali kutiphunzitsa zinthu zimene tiyenera kutchula m’pemphero. Pemphero limeneli limatithandizanso kudziwa zinthu zofunika kuzitchula choyamba tikamapemphera. Tiyeni tionenso bwinobwino zimene ananena. Pemphero limeneli linalembedwa pa Mateyu 6:9-13.

“Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.”

Apatu Yesu anakumbutsa otsatira ake kuti mapemphero onse ayenera kupita kwa Atate, Yehova. Koma kodi mukudziwa kuti n’chifukwa chiyani dzina la Yehova lili lofunika ndiponso chifukwa chake liyenera kuyeretsedwa?

Kuyambira kale pamene anthu analengedwa, dzina loyera la Mulungu ladetsedwa ndi mabodza amene anthu amanena. Satana, yemwe ndi mdani wa Mulungu, amanena kuti Yehova ndi wabodza, ndi Wolamulira wodzikonda ndipo sayenera kumalamulira zolengedwa zake. (Genesis 3:1-6) Anthu ambiri agwirizana ndi Satana. Iwo amaphunzitsa kuti Mulungu ndi wopanda chifundo, ndi wouma mtima ndiponso amazunza anthu. Iwo amakananso mfundo yakuti Mulungu ndi Mlengi wa wazinthu zonse. Ena amalimbana ndi dzina la Mulungu lenilenilo lakuti Yehova polichotsa m’mabaibulo awo komanso poletsa anthu kuti asamaligwiritse ntchito.

Baibulo limasonyeza kuti Mulungu adzathetsa mabodza onsewa. (Ezekieli 39:7) Pochita zimenezo, iye adzathetsanso mavuto anu onse ndi kukupatsani zofunika zonse. Kodi adzachita bwanji zimenezo? Mawu otsatira amene Yesu ananena m’pempheroli, akupereka yankho la funso limeneli.

“Ufumu wanu ubwere.”

Masiku ano, atsogoleri a zipembedzo ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya Ufumu wa Mulungu. Koma anthu amene ankamvetsera zimene Yesu anaphunzitsa, ankadziwa kuti kale aneneri a Mulungu analosera kuti Mesiya, Mpulumutsi wosankhidwa ndi Mulungu, adzakhala mfumu ya Ufumu womwe udzasinthe zinthu padziko lapansi. (Yesaya 9:6, 7; Danieli 2:44) Ufumu umenewo udzayeretsa dzina la Mulungu mwa kuchititsa kuti mabodza onse a Satana aonekere. Kenako Ufumuwo udzachotsa Satana ndi ntchito zake zonse. Ufumu wa Mulungu udzathetsa nkhondo, matenda, njala ngakhalenso imfa. (Salimo 46:9; 72:12-16; Yesaya 25:8; 33:24) Choncho mukamapemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere, ndiye kuti mukupempha kuti malonjezo onsewa akwaniritsidwe.

“Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.”

Mawu a Yesu amenewa akusonyeza kuti ndi zosakayikitsa kuti chifuniro cha Mulungu chidzachitikadi padziko lapansi pano monga mmene chikuchitikira kumwamba, kumene Mulungu amakhala. Palibe chimene chinalepheretsa chifuniro cha Mulungu kuchitika kumwamba. Kumeneko Mwana wa Mulungu anamenyana ndi Satana ndi ziwanda zake ndipo anawaponya padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:9-12) Komanso, mofanana ndi mawu oyambirira m’pemphero lachitsanzo la Yesu, mawu onena za kuchitika kwa chifuniro cha Mulungu amenewa, akutithandiza kuti tiziganizira chinthu chofunika kwambiri, chimene ndi chifuniro cha Mulungu, osati chathu. Nthawi zonse chifuniro cha Mulungu n’chimene chimabweretsa zinthu zabwino kwambiri kwa zolengedwa zonse. Ndiye chifukwa chake Yesu, ngakhale kuti anali wangwiro, anauza Atate wake kuti: “Chifuniro chanu chichitike, osati changa.”​—Luka 22:42.

“Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.”

Kenako, Yesu anasonyeza kuti tikhozanso kupempherera zosowa zathu. Sikulakwa kupempha Mulungu kuti atipatse zimene tikusowa pa moyo wathu. Ndipo kuchita zimenezo kumatikumbutsa kuti Yehova ndi amene “amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:25) Baibulo limasonyeza kuti Yehova ndi kholo lachikondi ndipo amasangalala kupatsa ana ake zinthu zimene anawo akufuna. Komabe mofanana ndi kholo lililonse labwino, iye sapatsa anthu zinthu zimene akudziwa kuti sizingawathandize.

“Mutikhululukire zolakwa zathu.”

Kodi timafunikiradi kuti Mulungu atikhululukire? Anthu ambiri masiku ano asiya kukhulupirira kuti anthufe ndife ochimwa ndipo sakuonanso kuti uchimo ndi nkhani yaikulu. Koma Baibulo limasonyeza kuti uchimo ndi umene umayambitsa mavuto onse amene tikukumana nawo ndipo ndi umene umachititsa kuti anthufe tizifa. Popeza anthufe tinabadwa ochimwa, nthawi ndi nthawi timalakwa ndipo kuti tidzakhale ndi moyo wosatha, zikudalira kuti Mulungu azitikhululukira. (Aroma 3:23; 5:12; 6:23) Ndi zolimbikitsa kudziwa kuti Baibulo limanena kuti: “Inu Yehova ndinu Mulungu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.”​—Salimo 86:5.

“Mutilanditse kwa woipayo.”

Kodi mukudziwa kuti mukufunikira chitetezo cha Mulungu mwamsanga? Anthu ena amakana zoti “woipayo,” amene ndi Satana, alipodi. Koma Yesu anaphunzitsa kuti Satana alipo ndithu, moti anachita kunena kuti Satanayo ndiye “wolamulira wa dzikoli.” (Yohane 12:31; 16:11) Choncho Satana waipitsa maganizo a anthu ambiri m’dzikoli, ndipo akufunitsitsa kuipitsanso maganizo anu. Cholinga chake n’chakuti musakhale pa ubwenzi wabwino ndi Atate wanu wakumwamba, Yehova. (1 Petulo 5:8) Ngakhale zili choncho, Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa Satana ndipo amasangalala kuteteza anthu amene amamukonda.

Apa sitinatchule nkhani zonse zimene tingapempherere, koma tangofotokoza mwachidule chabe mfundo zikuluzikulu za m’pemphero lachitsanzo la Yesu. Kumbukirani kuti lemba la 1 Yohane 5:14 limati: “Chilichonse chimene tingamupemphe [Mulungu] mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” Choncho, musaganize kuti mavuto anu ndi aang’ono kwambiri oti simungamuuze Mulungu.​—1 Petulo 5:7.

Nanga bwanji za nthawi yoyenera kupemphera ndiponso malo amene tingapemphererepo? Kodi zimenezi n’zofunikanso?