Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

3 Kodi Tiyenera Kupemphera Bwanji?

3 Kodi Tiyenera Kupemphera Bwanji?

M’ZIPEMBEDZO zambiri amakonda kuphunzitsa anthu mmene ayenera kukhalira popemphera, mawu amene ayenera kutchula komanso mwambo umene ayenera kutsatira. Koma Baibulo limatithandiza kuona kuti zimenezi sizofunika kwenikweni. M’malomwake, limatilimbikitsa kuganizira chinthu chofunika kwambiri pa funso lakuti, “Kodi tiyenera kupemphera bwanji?”

Baibulo limanena za atumiki a Mulungu amene ankapemphera pamalo osiyanasiyana komanso atakhala mwa njira zosiyanasiyana. Anapemphera chamumtima ndipo ena anapemphera mokweza malinga ndi mmene zinthu zinalili pa nthawi yopempherayo. Ankapemphera akuyang’ana kumwamba kapena atagwada. Iwo sankagwiritsa ntchito mafano, mikanda kapena mabuku popemphera, koma angangopemphera mochokera pansi pamtima ndipo ankalankhula mawu awoawo. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti mapemphero awo amvedwe?

Monga tatchulira kale m’nkhani imene yangotha kumene ija, iwo ankapemphera kwa Mulungu mmodzi, Yehova. Palinso chinthu china chofunika kwambiri chimene anachita. Pa lemba la 1 Yohane 5:14 timawerenga kuti: “Ifetu timamudalira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” Choncho mapemphero athu ayenera kukhala ogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

Kuti tizipemphera mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, choyamba tiyenera kudziwa kuti chifuniro chakecho n’chiyani. Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kuphunzira Baibulo kuti mapemphero athu akhale ogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu azimvetsera mapemphero athu pokhapokha ngati ndife akatswiri pa nkhani ya Baibulo? Ayi, koma Mulungu amafuna kuti tiziphunzira chifuniro chake, kuchimvetsa komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chakecho. (Mateyu 7:21-23) Choncho, tifunika kupemphera mogwirizana ndi zimene timaphunzira m’Baibulo.

Mulungu amayankha mapemphero amene timapemphera m’dzina la Yesu, mwachikhulupiriro komanso mogwirizana ndi chifuniro chake

Tikapitiriza kuphunzira za Yehova ndi chifuniro chake, chikhulupiriro chathu chidzakula. Zimenezi n’zofunika ngati tikufuna kuti Mulungu azimvetsera mapemphero athu. Yesu ananena kuti: “Chinthu chilichonse chimene mudzapempha m’mapemphero anu, mudzalandira ngati muli ndi chikhulupiriro.” (Mateyu 21:22) Kukhala ndi chikhulupiriro sikutanthauza kungokhulupirira chilichonse popanda kuchiganizira bwinobwino. Koma kumatanthauza kukhulupirira chinachake choti ngakhale kuti n’chosaoneka ndi maso, pali umboni wamphamvu wakuti chinthucho chilipodi. (Aheberi 11:1) M’Baibulo muli umboni wambirimbiri wosonyeza kuti Yehova, ngakhale kuti sitingamuone, alipo ndithu, ndi wodalirika ndipo amayankhadi mapemphero a anthu amene amamukhulupirira. Komanso, tingamupemphe kuti atithandize kuti tizimukhulupirira kwambiri ndipo iye amasangalala kutipatsa zimene tikufunikira.​—Luka 17:5; Yakobo 1:17.

Yesu anatchula chinthu chinanso chofunika kwambiri popemphera. Iye anati: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Zimenezi zikutanthauza kuti Yesu ndi njira yotithandiza kuti mapemphero athu  afike kwa Atate, Yehova. N’chifukwa chake Yesu anauza otsatira ake kuti azipemphera m’dzina lake. (Yohane 14:13; 15:16) Koma zimenezi sizikutanthauza kuti tizipemphera kwa Yesu. M’malo mwake, tiyenera kupemphera m’dzina la Yesu podziwa kuti iye ndi amene amachititsa kuti mapemphero athu afike kwa Atate wathu wangwiro ndi woyera.

Nthawi ina otsatira a Yesu anamupempha kuti: “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera.” (Luka 11:1) Zikuoneka kuti popereka pempho limeneli, iwo sanali kumupempha kuti awafotokozere mfundo zimene tangokambirana kumenezi, koma ankamupempha kuti awauze zinthu zimene ayenera kutchula popemphera. M’mawu ena, funso lawo kwenikweni linali lakuti, ‘Kodi tizipempha chiyani?’