Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Sizichita Nawo Mapemphero Pamodzi ndi Zipembedzo Zina?

N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Sizichita Nawo Mapemphero Pamodzi ndi Zipembedzo Zina?

 Zimene Owerenga Amafunsa . . .

N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Sizichita Nawo Mapemphero Pamodzi ndi Zipembedzo Zina?

▪ Buku lina linanena kuti “padzikoli pali zipembedzo pafupifupi 10,000.” (World Christian Encyclopedia) Chifukwa choti anthu azipembedzo zosiyanasiyana sagwirizana, iwo amaona kuti kupempherera pamodzi kungathetse vutoli. Amakhulupirira kuti kuchita zimenezi kungathandize kuti azikhala mwamtendere ndiponso mogwirizana m’dzikoli limene anthu sagwirizana.

Baibulo limalimbikitsa anthu kuti azikhala mogwirizana. Ndipo mtumwi Paulo anayerekezera mpingo wachikhristu ndi thupi la munthu limene ziwalo zonse ‘n’zolumikizika bwino ndi zogwirizana.’ (Aefeso 4:16) Mofanana ndi zimenezi, mtumwi Petulo analimbikitsa okhulupirira anzake kuti: “Nonsenu mukhale a maganizo amodzi.”​—1 Petulo 3:8.

Akhristu oyambirira ankakhala limodzi ndi anthu azikhalidwe ndiponso zipembedzo zosiyanasiyana. Komabe, pa nkhani yakuti zipembedzo zosiyanasiyana zizichitira pamodzi mapemphero, Paulo anafunsa kuti: “Munthu wokhulupirira agawana chiyani ndi wosakhulupirira?” Ndiyeno anachenjeza Akhristu kuti ‘atuluke pakati pawo.’ (2 Akorinto 6:15, 17) Mawu amenewa akusonyeza kuti Paulo sankagwirizana nazo zoti zipembedzo zosiyanasiyana zizichitira pamodzi mapemphero. N’chifukwa chiyani sanagwirizane nazo?

Mtumwi Paulo anafotokoza kuti sizoyenera kuti Akhristu oona azichitira limodzi mapemphero ndi anthu amene si Akhristu oona, chifukwa zili ngati kumangidwa m’goli ndi osakhulupirira. (2 Akorinto 6:14) Zimenezi zingawononge chikhulupiriro cha Akhristu oona. Tingayerekezere zimene Paulo ankada nazo nkhawa ndi zimene bambo wachikondi angade nazo nkhawa atadziwa kuti ana ena a m’dera limene akukhala ndi akhalidwe loipa. Bamboyo angachite zinthu mwanzeru poletsa ana ake kuti asamacheze ndi ana akhalidwe loipawo. Koma anthu ena sangasangalale ndi zimene bamboyo wachita. Komabe, zimene bamboyu wachita zingateteze ana ake kuti asatengere makhalidwe oipa. N’chimodzimodzinso Paulo. Iye ankadziwa kuti kupewa kuchita mapemphero pamodzi ndi zipembedzo zina kungateteze Akhristu ku zinthu zoipa.

Paulo anachita zimenezi potengera chitsanzo cha Yesu. Ngakhale kuti Yesu ankalimbikitsa kuti anthu azikhala mwamtendere, iye sanachitire pamodzi mapemphero ndi anthu azipembedzo zina. M’nthawi yake, panali magulu ambiri achipembedzo monga Afarisi ndi Asaduki. Ndipotu magulu achipembedzo amenewa anagwirizana kuti azitsutsana ndi Yesu mpaka anamukonzera chiwembu kuti amuphe. Koma Yesu analangiza otsatira ake kuti “asamale ndi zimene Afarisi ndi Asaduki amaphunzitsa.”​—Mateyo 16:12.

Nanga bwanji masiku ano? Kodi zimene Baibulo limachenjeza pa nkhani yochitira pamodzi mapemphero ndi anthu azipembedzo zina n’zothandiza? Inde n’zothandiza. Chifukwa zikhulupiriro zosiyana sizingagwirizane chifukwa choti anthu ake akuchitira pamodzi mapemphero monga mmene mafuta ndi madzi sizingasakanikirane ngakhale mutaziphatikiza. Mwachitsanzo, anthu azipembedzo zosiyanasiyana akachitira pamodzi mapemphero opempherera mtendere, kodi amakhala akupemphera kwa mulungu wake uti? Kodi amapemphera kwa Mulungu amene matchalitchi achikhristu amati alipo Atatu mwa mmodzi? Kapena amapemphera kwa Brahma, yemwe ndi mulungu wa Ahindu? Kapenanso mwina amapemphera kwa Buda? Kapena amapemphera kwa mulungu winawake?

Mneneri Mika analosera kuti, “masiku otsiriza” anthu ochokera m’mitundu yonse adzati: “Tiyeni, tikwere kuphiri la Yehova, ndi kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m’mabande ake.” (Mika 4:1-4) Kukhulupirira zinthu zofanana n’kumene kukuthandiza kuti anthu padziko lonse akhale mwamtendere ndiponso mogwirizana, osati kuchitira pamodzi mapemphero.

[Chithunzi patsamba 27]

Anthu a m’zipembedzo zikuluzikulu kwambiri padziko lonse anachitira mapemphero pamodzi mu 2008

[Mawu a Chithunzi]

REUTERS/​Andreas Manolis