Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“N’chifukwa Chiyani Akuima Malo Ngati Amenewa?”

“N’chifukwa Chiyani Akuima Malo Ngati Amenewa?”

 KALATA YOCHOKERA KU SOUTH AFRICA

“N’chifukwa Chiyani Akuima Malo Ngati Amenewa?”

“DERA LINO NDI LOOPSA KWAMBIRI, KUMAKHALA MBAVA NDI MAHULE.” Mawu amenewa ali pachikwangwani china chimene chili m’mbali mwa msewu wina wafumbi. Tinapatuka mumsewu umenewu, n’kuima pafupi ndi chikwangwani chinanso chachikulu m’dera limeneli, cholozera kumalo ena achisangalalo apamwamba kwambiri. Pomwe tinaimapo panalinso magalimoto angapo. Anthu ena omwe ankadutsa m’magalimoto awo okongola ankatiyang’ana modabwa kwambiri ndipo mwina mumtima ankangoti: ‘N’chifukwa chiyani akuima malo ngati amenewa?’

Titaimika galimoto yathu, tinatsika n’kupita pagulu la anzathu omwe anali atavala bwino kwambiri ndipo anali ataima pamthunzi wachikwangwanicho. Pagulu lathulo panali anthu azikhalidwe ndiponso mitundu yosiyanasiyana. Zimenezi sizichitika kawirikawiri ku South Africa. Tinali titayenda ulendo wa makilomita 100 kudzafika kumalo amenewa omwe ali kumpoto, chakumadzulo kwa mzinda wa Johannesburg. Cholinga chathu chinali kukalalikira choonadi cha m’Baibulo kwa anthu a m’dera lakumidzili.

Tinachita msonkhano wachidule m’mphepete mwa msewuwo pokonzekera utumiki wolalikira nyumba ndi nyumba. Pamsonkhanowo tinakambirana vesi la m’Baibulo ndipo titapemphera tinakakweranso magalimoto athu, n’kunyamuka. Kumene timapita kunali nyumba ndiponso zisakasa zomangidwa mopanda dongosolo. Nyumbazo zinkaoneka zing’onozing’ono poyerekezera ndi milu ikuluikulu ya zinyalala za m’migodi zomwe zili m’derali. Anthu a m’dera limeneli ndi osauka kwambiri ngakhale kuti kuli migodi ya miyala yamtengo wapatali.

Ine ndi mkazi wanga ndiponso banja lina lochokera ku Germany tinayamba kulalikira nyumba ndi nyumba. M’derali anthu ambiri sali pa ntchito ndipo n’chifukwa chake nyumba zake n’zosaoneka bwino. Zambiri mwa nyumbazi ndi zisakasa zomangidwa ndi malata komanso matabwa osalimba. Pokhoma nyumbazi amatenga zitsekerero za mabotolo amowa, n’kuziphwanya ndipo kenako amaziboola ndi misomali n’kuzikhomerera kunyumbazi kuti zilimbe.

Tikafika panyumba iliyonse tinkachita odi ndipo kawirikawiri timapeza mayi wapanyumbapo. Munthu aliyense yemwe tinalankhula naye anali wofunitsitsa kumva uthenga umene tinabweretsa ndipo anatilandira bwino kwambiri ngati ndife anthu apadera. Chifukwa choti dzuwa linkatentha kwambiri, m’nyumba munkatentha ngati muuvuni ndipo tikafika pakhomo, makolo ankangouza ana kutulutsa mipando kuti tikhale panja, pansi pa mtengo.

Kenako, banja lonse linkabwera pamodzi n’kukhalira masitulu ndi makeleti. Ngakhale ana omwe nthawi zambiri ankakhala akusewera ndi zidole zawo ankawaitana kuti adzamvetsere uthengawo. Tikawerenga mavesi angapo tinkauza ana omwe amatha kuwerenga kuti awerenge ndime  zina m’mabuku athu. Pafupifupi munthu aliyense amene tinakumana naye analandira mabuku anthu mosangalala kwambiri ndipo anatipempha kuti tidzamuchezerenso ulendo wina.

Masana tinapuma pang’ono kuti tidye chakudya tisanapite kukacheza ndi anthu ena omwe tinawayendera pa ulendo wina. Khomo loyamba linali la bambo wina dzina lake Jimmy, yemwe anali wochokera ku Malawi ndipo ankagwira ntchito mumgodi. Tinaphunzira Baibulo ndi Jimmy kwa miyezi ingapo ndipo iye ankasangalala kwambiri tikafika kudzaphunzira naye. Iye anakwatira mkazi wachitswana ndipo anali ndi ana awiri okongola kwabasi. Popeza kuti pa ulendo womaliza umene tinabwera kuno sitinamupeze, pa ulendowu tinkafunitsitsa kumuona.

Pomwe tinayandikira nyumba ya Jimmy tinazindikira kuti chinachake sichili bwino pakhomopo. Chimanga chake cha m’dimba chomwe nthawi zambiri tinkachipeza chili chobiliwira, chinali chitafota. Nazonso nkhuku zomwe nthawi zambiri tinkazipeza zikuyendayenda ndi kupalasapalasa panja pa nyumbayo panalibe. Chitseko cha nyumbayo chinali chokhomedwa ndi tcheni chachikulu kwambiri. Kenako panafika mayi wina amene ankakhala moyandikana ndi Jimmy kudzatilonjera. Titamufunsa ngati akudziwa komwe Jimmy anapita, iye anatiuza nkhani yomvetsa chisoni kwambiri. Iye anatiuza kuti Jimmy anamwalira ndipo ana ndi mkazi wake anabwerera kwawo.

Ngakhale kuti m’derali anthu amaona kuti ndi mwano kufunsa mafunso ambirimbiri okhudza anthu ena, ife tinafunsabe kuti tidziwe chomwe chinachitika. Mayiyo anatiyankha kuti: “Jimmy ankadwala. Pajatu masiku ano anthu akumwalira ndi matenda osiyanasiyana.” Mayiyu sanatchule matenda omwe Jimmy anamwalira nawo, popeza anthu sakonda kukambirana zimenezi. Koma chifukwa chakuti kumanda kukudzadza, ndi umboni wa zimene mayiyo ananena. Tinakambirana naye mwachidule za chiyembekezo chakuti akufa adzauka. Kenako tinachoka n’kupita kunyumba ina tili ndi chisoni kwambiri.

Tinalowa m’mudzi wina ndipo tinayendetsa galimoto yathu mpaka kunyumba zakumapeto zoyandikana ndi mulu waukulu kwambiri wa dothi la m’migodi. Kenako tinalowa mukamsewu kena komwe kali chakumapeto kwa msewu waukuluwo. Tinafika pamalo ena pomwe tinaona mwala wina wake m’munda ndipo unalembedwa ndi penti mawu ooneka bwino akuti: “Zengerezu analinda kwawukwawu.” David * ndi amene analemba mawu amenewa ndipo atationa anatulutsa mutu wake pawindo la kagalimoto kake kakale kamtundu wa m’benene. Atatizindikira, anamwetulira ndipo mano ake omwe anawamata tizitsulo tonyezimira tagolide anaonekera. Ndiyeno anapukuta m’manja mwake n’kubwera kudzatipatsa moni.

Iye anati: “Muli bwanji? Takulandirani, koma ndiye munasowatu, munali kuti?” Tinasangalala kuonananso ndi David. Iye anatipepesa n’kutiuza kuti sititha kuphunzira naye chifukwa anali atapeza ntchito kumgodi ndipo anafunika kupita kuntchitoko. Nthawi yonse yomwe tinakambirana naye ankangomwetulira. Iye anatiuza mosangalala kuti: “Zimene tinakambirana pa nthawi yoyamba ija zasintha kwambiri moyo wanga. Ndikunena zoona, sindikudziwa kuti bwenzi pano ndili kuti ndikanakhala kuti sindinakumane nanu.”

Tinasangalala kwambiri kukumana ndi David. Kenako tinauyamba ulendo wobwerera kwathu dzuwa litayamba kulowa. Tinayang’ana dera limene tinkachokeralo komaliza ndipo panthawiyi silinkaoneka bwino chifukwa cha fumbi. Tinadzifunsa mumtima kuti, ‘Kodi anthu onsewa adzafikiridwa bwanji ndi uthenga wabwino?’ Tinamvetsa bwino kwambiri tanthauzo la mawu a Yesu akuti: “Zokolola n’zochulukadi, koma antchito ndi ochepa.”​—Luka 10:2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Dzinali talisintha.

[Mawu a Chithunzi Patsamba 17]

Kind permission given by the South African Post Office