Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

Anthu Amene Analemba za Yesu

Anthu Amene Analemba za Yesu

KODI umasangalala kukuwerengera za Yesu?​— * Anthu ena amadabwa kumva kuti m’Baibulo mulibe nkhani iliyonse imene Yesu analemba. Komabe, pali anthu 8 amene analemba nawo Baibulo amene amatiuza za iye. Anthu amenewa analipo m’nthawi ya Yesu, ndipo amatiuza zimene iye anaphunzitsa. Kodi ungatchule mayina a anthu 8 amenewa?​— Anthuwa ndi Mateyo, Maliko, Luka, ndi Yohane. Anthu anayi enawo ndi Petulo, Yakobe, Yuda, ndi Paulo. Kodi umadziwa chiyani za anthu amenewa?​—

Tiye tikambirane kaye za anthu atatu amene analemba nawo za Yesu amene analinso m’gulu la atumwi ake 12. Kodi umawadziwa mayina awo?​— Petulo, Yohane ndi Mateyo. Petulo analemba makalata awiri opita kwa Akhristu anzake. Iye analemba zinthu zimene ankadziwa kuti Yesu anachita ndiponso ananena. Tsegula Baibulo lako pa 2 Petulo 1:16-18, ndipo werenga pamenepo kuti umve zimene Petulo anafotokoza zokhudza zimene zinachitika atamva Yehova Mulungu akulankhula ndi Yesu.​—Mateyo 17:5.

Mtumwi Yohane analemba mabuku asanu a m’Baibulo. Iye anakhala pafupi ndi Yesu pachakudya chomaliza chimene Yesuyo anadya ndi ophunzira ake. Panthawi imene Yesu anamwalira, Yohane anali pomwepo. (Yohane 13:23-26; 19:26) Yohane analemba limodzi la mabuku a m’Baibulo anayi onena za moyo wa Yesu. Ndipo mabukuwo amatchedwa Uthenga Wabwino. Iye analembanso buku la Chivumbulutso limene limanena za masomphenya amene Yesu anamuonetsa. Yohane analembanso makalata atatu a m’Baibulo amene ali ndi dzina lake. (Chivumbulutso 1:1) Munthu wina wachitatu amene analemba nawo nkhani zokhudza Yesu m’Baibulo ndi Mateyo, yemwe anali mtumwi wa Yesu. Poyamba, iye anali wokhometsa msonkho.

Anthu ena awiri amene analemba nawo Baibulo ankamudziwa kwambiri Yesu. Iwo anali azing’ono ake, chifukwa amayi awo anali amodzi. Anthu amenewa anali ana a Yosefe ndi Mariya. (Mateyo 13:55) Poyamba, sanali ophunzira a Yesu. Iwo ankaganiza kuti Yesu anali wamisala chifukwa ankakonda kwambiri kulalikira. (Maliko 3:21) Kodi mayina awo ndani?​— Wina ndi Yakobe. Iye analemba buku la m’Baibulo lotchedwa Yakobe. Winayo ndi Yudasi, amene amadziwikanso ndi dzina lakuti Yuda. Iye analemba buku la m’Baibulo la Yuda.​—Yuda 1.

Anthu ena awiri amene analemba nkhani zokhudza moyo wa Yesu anali Maliko ndi Luka. Mariya, mayi ake a Maliko, anali ndi nyumba yaikulu ku Yerusalemu, kumene Akhristu oyambirira kuphatikizapo mtumwi Petulo, ankasonkhanako. (Machitidwe 12:11, 12) Zaka zingapo zimenezi zisanachitike, madzulo a tsiku limene Yesu anachita Pasika ndi atumwi ake, Maliko ayenera kuti anawatsatira atapita ku munda wa Getsemane. Yesu atamangidwa, asilikali anamugwira Maliko, koma anathawa n’kusiya chovala chake.​—Maliko 14:51, 52.

Luka anali dokotala wophunzira kwambiri amene anakhala wophunzira, Yesu atamwalira. Iye anaphunzira kwambiri nkhani yokhudza moyo wa Yesu ndipo anailemba momveka ndiponso molondola. Patapita nthawi, Luka anayamba kuyenda ndi mtumwi Paulo ndipo analembanso buku la m’Baibulo lotchedwa Machitidwe.​—Luka 1:1-3; Machitidwe 1:1.

Paulo ndi munthu wa 8 amene analemba nkhani ya m’Baibulo yokhudza Yesu. Iye anaphunzitsidwa ndi Gamaliyeli, mphunzitsi wotchuka wachilamulo. Paulo, amene panthawiyo ankatchedwa Saulo, anakula ndiponso kuphunzitsidwa ndi Afarisi. Iye ankadana ndi ophunzira a Yesu ndipo ankawapha. (Machitidwe 7:58–8:3; 22:1-5; 26:4, 5) Kodi ukudziwa zimene zinachitika kuti Paulo aphunzire zoona zake za Yesu?​—

Paulo anali paulendo wa ku Damasiko kukamanga ophunzira a Yesu pamene kuwala kochokera kumwamba kunam’pangitsa khungu. Iye anamva mawu akuti: “Saulo, Saulo n’chifukwa chiyani ukundizunza?” Amalankhulayo ndi Yesu ndipo anauza Paulo kuti apite ku Damasiko. Ndiyeno Yesu anauza wophunzira Ananiya kulankhula ndi Paulo, ndipo Paulo anakhala wophunzira wa Yesu. (Machitidwe 9:1-18) Paulo analemba mabuku a m’Baibulo 14, kuyambira buku la Aroma mpaka Aheberi.

Kodi unayamba kuwerenga mabuku a m’Baibulo onena za Yesu kapena kodi munthu wina akumakuwerengera?​— China cha zinthu zofunika kwambiri zimene ungachite pa moyo wako, n’kuyamba panopo ukadali wamng’ono kuphunzira zimene Baibulo limanena zokhudza Yesu.

^ ndime 3 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana wanu, pamene pali mzere pakusonyeza kuti muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.