Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Chinsinsi cha Banja Losangalala

Kuphunzitsa Ana Kuti Adzathe Kudziimira Paokha

Kuphunzitsa Ana Kuti Adzathe Kudziimira Paokha

George: * “Pamene mwana wanga Michael anali ndi zaka zinayi, madzulo aliwonse ankakonda kusiya zidole zake zili mbwee m’nyumba monse. Ndikangoyesa kumuuza kuti achotse zidolezo asanakagone, iye ankalusa kwambiri n’kuyamba kukuwa komanso kuchita zinthu zina zovutitsa. Nthawi zina zimenezi zinkandipweteketsa mtima kwambiri moti ndinkamulankhula mokalipa kwambiri, koma mapeto ake zinkangochititsa kuti tonse tikhale okhumudwa. Pofuna kuti tonse tizikagona tili osangalala, ndinasiya kulimbana naye ndipo ndinkangochotsa ndekha zidolezo.”

Emily: “Tsiku lina mwana wanga wazaka 13, dzina lake Jenny, sanamvetse malangizo amene aphunzitsi ake anamuuza kuti atsatire polemba ntchito ina imene anam’patsa. Iye atafika kunyumba analira kwa ola lathunthu. Ndinamuuza kuti akawapemphe aphunzitsi akewo kuti amuthandize koma iye ananena kuti amawaopa chifukwa ndi ovuta. Nditamva zimenezi ndinaganiza kuti ndingonyamuka nthawi yomweyo n’kukawalalatira aphunzitsiwo. Sindinkafuna kuti mwana wa ine azikhala wosasangalala chifukwa cha munthu winawake.”

KODI munayamba mwakumanapo ndi mavuto ngati amene George ndi Emily anakumana nawowa? Palinso makolo ambiri amene amakhumudwa kwambiri akaona mwana wawo akuvutika ndi chinachake kapena ali wokhumudwa. Mwachibadwa, makolo amafuna kuteteza ana awo. Komabe, mavuto amene makolo omwe tawatchula pamwambawa anakumana nawo, kwenikweni anawapatsa mwayi wophunzitsa ana awo kuti azidziwa udindo wawo. N’zoona kuti zimene mwana wazaka zinayi angaphunzire sizingafanane ndi zimene mwana wa zaka 13 angaphunzire.

Komabe, muyenera kudziwa kuti n’zosatheka kuti muzimuteteza mwana wanu nthawi zonse ku mavuto amene angamakumane nawo pamoyo wake wonse. Mwana akakula, amasiya atate wake ndi amake ndipo amayenera “kunyamula katundu wakewake,” kutanthauza kuti amayenera kudziimira payekha. (Agalatiya 6:5; Genesis 2:24) Kuti ana azitha kukwaniritsa udindo wawo, makolo ayenera kukhala ndi cholinga chowaphunzitsa  kuti akadzakula adzakhale oganizira ena, achikondi komanso odalirika. Kuchita zimenezi sikophweka ayi.

Koma chosangalatsa n’chakuti Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa makolo pa nkhani ya mmene iye ankachitira zinthu ndi ophunzira ake. Yesu analibe ana akeake. Koma cholinga chake posankha ndi kuphunzitsa ophunzira ake, chinali chakuti iwowo akatsala adzathe kupitiriza ntchitoyo. (Mateyo 28:19, 20) Cholinga cha Yesu chinakwaniritsidwa chifukwa patsogolo pake ophunzira akewo anatha kuchita bwinobwino ntchitoyo paokha. Nawonso makolo amafuna kuti ana awo akadzakula adzathe kudziimira paokha. Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zokha zimene makolo angaphunzire kwa Yesu.

Muzipereka Chitsanzo Chabwino kwa Mwana Wanu

Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, anauza ophunzira ake kuti: “Ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.” (Yohane 13:15) Potengera zimenezi, makolo ayenera kuwafotokozera ana awo zimene angachite kuti adzathe kukwaniritsa udindo wawo komanso ayenera kuwasonyeza chitsanzo pa nkhani imeneyi.

Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimakonda kulankhula zinthu zosonyeza kuti ndimasangalala kukwaniritsa udindo wanga? Kodi ndimalankhula zosonyeza kuti ndimasangalala ndikamathandiza anthu ena? Kapena kodi ndimakonda kudandaula n’kumadziyerekezera ndi anthu amene amaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino?’

N’zoona kuti palibe munthu wangwiro. Tonsefe nthawi zina timaona kuti zochita zatichulukira. Komabe, chitsanzo chanu ndi chomwe chingathandize kwambiri ana anu kudziwa kuti kukwaniritsa udindo wawo n’kofunika kwambiri.

TAYESANI IZI: Ngati zingatheke, nthawi zina muzim’tenga mwana wanuyo kuntchito kwanu n’kukamusonyeza zimene mumachita kuti muzipeza ndalama zothandizira banja lanu. Ngati pali munthu wina amene akufunikira kumuthandiza kugwira ntchito inayake, pitani limodzi ndi mwana wanuyo. Kenako, kambiranani zimene nonse mwasangalala nazo pogwira ntchitoyo.​—Machitidwe 20:35.

Muzidziwa Zimene Sangakwanitse

Yesu ankadziwa kuti zidzawatengera nthawi ophunzira ake kuti adzafike potha kuchita bwinobwino zinthu zimene iye ankafuna kuti adzachite. Panthawi ina iye anawauza kuti: “Ndili ndi zambiri zakuti ndikuuzeni, koma simungathe kuzimvetsa zonsezo pakali pano.” (Yohane 16:12) Yesu sanangofikira kuwasiya ophunzira ake kuti azichita zinthu zonse paokha. Koma anakhala nawo kwa nthawi yaitali n’kuwaphunzitsa zinthu zambiri. Ndiyeno atakhutitsidwa kuti angathe kuchita zinthu paokha, anawatumiza kuti akagwire ntchito imene anawapatsa.

Mofanana ndi zimenezi, makolo sayenera kusiyira ana udindo kapena ntchito zoyenera munthu wamkulu. Komabe, anawo akamakula, makolo ayenera kuona zinthu zoyenerana ndi msinkhu wawo. Mwachitsanzo, makolo ayenera kuphunzitsa ana awo kuti azitha kusamalira thupi lawo, kusamalira chipinda chawo, kuchita zinthu pa nthawi yake ndiponso kugwiritsa ntchito bwino ndalama. Mwana akayamba sukulu, makolo ayenera kumuthandiza kudziwa kuti ntchito imene amapatsidwa kusukulu ndi yofunika ndipo ndi udindo wake kuigwira.

Udindo wa makolo siwongopereka ntchito kwa ana awo. Iwo ayeneranso kuwathandiza kuti athe kuchita bwino ntchitozo. Mwachitsanzo, George, bambo amene tamutchula poyamba uja, anazindikira kuti china chimene chinkachititsa kuti mwana wake Michael azivuta kwambiri akamuuza kuti achotse zidole zake chinali chakuti ntchitoyo inkamukulira. George anati: “M’malo mongomukalipira kuti achotse zidole zakezo, ndinamusonyeza njira yabwino yogwirira ntchitoyo.”

Kodi iye anachita chiyani? George anati: “Choyamba, ndinakhazikitsa nthawi yoti iye azichotsa zidole zake madzulo aliwonse. Kenako, ndinkamuthandiza kuchotsa zidolezo m’chipindamo ndipo tinkayamba ndi mbali imodzi ya chipindacho. Tinkagwira ntchitoyo mokhala ngati tikusewera n’kumapikisana kuti tione amene angachotse zambiri. Pasanapite nthawi, tinazolowera kuchita zimenezi madzulo aliwonse tisanakagone. Ndinamulonjeza kuti akamaliza ntchitoyo mwamsanga, ndiziwonjezera nthawi yomuwerengera buku la nthano asanakagone. Koma akalephera kumaliza  ntchitoyo mwamsanga, ndizimuchepetsera nthawiyo.”

TAYESANI IZI: Ganizirani ntchito zimene mwana wanu aliyense angakwanitse kugwira zomwe zingathandize kuti zinthu pa banja panupo ziziyenda bwino. Dzifunseni kuti, ‘Kodi pali zinthu zina zimene ndimachitirabe ana anga ngakhale kuti iwo angathe kuzichita paokha?’ Ngati zili choncho, athandizeni kugwira ntchito zawozo mpaka mudzaone kuti angathe kugwira ntchitozo paokha. Auzeni momveka bwino zimene mungawachitire akagwira bwino ntchitoyo komanso akapanda kugwira. Kenako, chitani mogwirizana ndi zimene mwanenazo.

Muziwapatsa Malangizo Omveka Bwino

Yesu anali mphunzitsi wabwino motero ankadziwa kuti munthu angaphunzire zinthu mosavuta akamazichita. Mwachitsanzo, Yesu ataona kuti ophunzira ake adziwa zokwanira, anawatumiza “awiriawiri kuti atsogole kupita mu mzinda ndi malo aliwonse kumene iye adzafikako.” (Luka 10:1) Komabe sikuti anangowasiya kuti azikagwira ntchitoyo mmene akufunira. Asanawatumize, iye anawapatsa malangizo omveka bwino. (Luka 10:2-12) Ophunzirawo atabwerera n’kumuuza mmene ntchitoyo inayendera, Yesu anawayamikira ndiponso anawalimbikitsa. (Luka 10:17-24) Iye anasonyeza kuti ankawadalira kuti angathe kugwira ntchitoyo ndiponso anawayamikira.

Kodi mumatani ana anu akakhala kuti akufunikira kuchita zinazake zovuta? Kodi mumaonetsetsa kuti asachite zinthuzo poopa kuti akhumudwa ngati atalephera? Mwachibadwa, mungafune kuteteza mwana wanuyo kapena kungomuchitira zinthu zovutazo.

Koma ganizirani izi: Nthawi iliyonse imene mumateteza mwana wanuyo, kodi iyeyo amaphunzirapo chiyani? Kodi amaona kuti mumam’dalira ndipo mumaona kuti angathe kuchita zinthu payekha? Kapena amaona kuti mumam’tengabe ngati kamwana koti sikangathe kuchita chilichonse pakokha?

Mwachitsanzo, kodi Emily, mayi amene tamutchula uja, anathetsa bwanji vuto la mwana wake? M’malo molowerera, iye anaona kuti ndi bwino kumuuza Jenny kuti akakambirane ndi aphunzitsi akewo payekha. Motero iye anathandizana ndi Jenny kulemba mafunso oti akawafunse aphunzitsiwo. Kenako anakambirana nthawi yabwino yoti akalankhule ndi aphunzitsiwo. Ndipo anayeserera mmene zikakhalire pokambirana ndi aphunzitsi akewo. Emily anati: “Jenny analimba mtima kukalankhula ndi aphunzitsi ake ndipo iwo anamuyamikira chifukwa chochita zimenezi. Iye ananyadira kwambiri ndi zimene anachita ndipo nanenso ndinanyadira.”

TAYESANI IZI: Lembani vuto limene mwana wanu akukumana nalo panopa. Pambali pake, lembanipo zimene mungachite kuti mumuthandize kuthetsa yekha vutolo. Muuzeni kuti ayeserere zimene akuyenera kuchitazo. Musonyezeni kuti simukukayikira kuti akwanitsa kuthetsa vutolo payekha.

Mukamakonda kutchinjiriza ana anu kuti asamakumane ndi mavuto, ndiye kuti mukuwawononga chifukwa sadzatha kuthana ndi mavuto. M’malo mwake, alimbikitseni powalola kukwaniritsa udindo wawo paokha. Kuchita zimenezi ndi imodzi mwa mphatso zamtengo wapatali zimene mungawapatse.

^ ndime 3 Mayina asinthidwa.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Kodi zimene ndimafuna kuti ana anga azichita ndi zogwirizana ndi msinkhu wawo?

  • Kodi ndimawauza komanso kuwapatsa chitsanzo pa zimene ayenera kuchita kuti akwanitse zimene akufunikira kuchita?

  • Kodi mwana wanga ndinamulimbikitsapo liti kapena kumuyamikira pa zimene anachita?