Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pa Nkhani ya Kulambira Koona

Pa Nkhani ya Kulambira Koona

 Zimene Tikuphunzira kwa Yesu

Pa Nkhani ya Kulambira Koona

Kodi Mulungu amavomereza kulambira konse?

▪ Yesu ankamva chisoni kwambiri ndi anthu amene ananamizidwa ndi chipembedzo chonyenga. Iye anachenjeza kuti pali “aneneri onyenga amene amabwera . . . atavala ngati nkhosa, koma mkati mwawo ali mimbulu yolusa.” (Mateyo 7:15) Kodi mukudziwa kuti anthu ena amachita zoipa m’dzina la chipembedzo?

Yesu anapemphera kwa Mulungu kuti: “Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yohane 17:17) Choncho, Mulungu samavomereza kulambira kumene kumatsutsana ndi choonadi cha m’Baibulo. Motero, ponena za atsogoleri onyenga a chipembedzo, Yesu anagwiritsa ntchito mawu a Mulungu akuti: “Amandilambira ine pachabe, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu monga ziphunzitso za Mulungu.”​—Mateyo 15:9.

Kodi pali chipembedzo choona?

▪ Yesu atakumana ndi mkazi wina wachisamariya amene anaphunzitsidwa zabodza ndi chipembedzo chonyenga, anamuuza kuti: “Inu mumalambira chimene simuchidziwa; . . . Olambira oona adzalambira Atate ndi mzimu ndi choonadi, pakuti Atate amafuna oterowo azimulambira.” (Yohane 4:22, 23) Zimenezi zikusonyeza kuti n’zotheka kupeza chipembedzo choona.

Yesu anati: “Sindichita kanthu mongoganiza ndekha; koma ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira.” Choncho Yesu ankadziwa kuti chipembedzo chimene iye ankaphunzitsa ndicho chokha chinali choona. (Yohane 8:28) N’chifukwa chake ananena kuti: “Ine ndine njira ndi choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Popeza kuti anthu amene amalambira Mulungu movomereka amafika kwa Atate kudzera  m’njira imodzi, iwo ayeneranso kukhala ogwirizana m’chipembedzo chimodzi choona.

Kodi mungawadziwe bwanji amene amalambira Mulungu movomerezeka?

▪ Mkhristu ndi munthu amene amatsatira Yesu Khristu. Tiyeni tione zinthu zinayi zimene zingatithandize kuzindikira otsatira a Yesu.

1. Yesu Khristu anapemphera kwa Yehova kuti: ‘Dzina lanu ndalidziwikitsa.’ (Yohane 17:26) Nawonso Akhristu oona amachitabe chimodzimodzi.

2. Yesu ankalalikira za Ufumu wa Yehova ndipo anatuma ophunzira ake kuti akalalikire za Ufumu umenewu kunyumba ndi nyumba. Iye anati: “Mukalowa mu mzinda kapena m’mudzi uliwonse, fufuzani mmenemo yemwe ali woyenerera.” Kenako anauza otsatira ake kuti: “Pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse.” (Mateyo 10:7, 11; 28:19) Masiku ano, n’zosavuta kudziwa Akhristu oona chifukwa akupitiriza kugwira ntchito imeneyi.

3. Yesu anakana kuchita nawo zandale. Choncho, ponena za otsatira ake, iye anati: “Sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” (Yohane 17:14) Anthu amene amalambira Mulungu movomerezeka sayenera kulowerera zandale.

4. Yesu anali wodzipereka kwambiri pofuna kusonyeza ena chikondi. Iye anati: “Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Akhristu oona amakondana kwambiri ndipo samenya nawo nkhondo.

Kodi ubwino wolambira Mulungu movomerezeka ndi wotani?

▪ Kuti muzilambira Yehova movomerezeka, choyamba muyenera kumudziwa bwino. Kudziwa Mulungu kudzakuthandizani kukhala munthu wabwino kwambiri ndiponso kukonda kwambiri Mulungu. Yehova analonjeza kuti adzapereka moyo wosatha kwa anthu amene amam’konda. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona.”​—Yohane 17:3.

Kuti mudziwe zambiri, onani mutu 15 wa buku ili Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 16]

“Chenjerani ndi aneneri onyenga amene amabwera kwa inu atavala ngati nkhosa, koma mkati mwawo ali mimbulu yolusa.”​—Mateyo 7:15