Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ogwira Ntchito Zapakhomo”

“Ogwira Ntchito Zapakhomo”

 Moyo wa Akhristu a M’nthawi ya Atumwi

“Ogwira Ntchito Zapakhomo”

“Tsopano pamene anali kuyenda, analowa m’mudzi wina. Kumeneko mayi wina dzina lake Marita anam’landira m’nyumba mwake monga mlendo. Mayi ameneyu anali ndi m’bale wake dzina lake Mariya. Iyeyu anakhala pansi kumapazi kwa Ambuye n’kumamvetsera mawu awo. Koma Marita anatanganidwa ndi ntchito zochuluka. Choncho anafika pafupi ndi kunena kuti: ‘Ambuye, kodi simukusamala kuti m’bale wangayu wandirekera ndekha ntchito? Tamuuzani tsopano kuti andithandize.’ Poyankha Ambuye anati kwa iye: ‘Marita, Marita, ukuda nkhawa ndiponso kutanganidwa ndi zinthu zambiri. Komatu zinthu zofunika kwenikweni n’zochepa chabe, mwinanso n’chimodzi chokha basi. Kumbali yake, Mariya wasankha chinthu chabwino kwambiri, ndipo sadzalandidwa chimenecho.’”​—LUKA 10:38-42.

N’ZOONEKERATU kuti Marita anali mkazi wolimbikira ntchito. Ndipo, n’zosakayikitsa kuti anthu ambiri ankamulemekeza. Pa chikhalidwe cha Ayuda a m’nthawi ya atumwi, mkazi ankalemekezedwa malinga ndi kudzipereka kwake pogwira ntchito zapakhomo ndiponso chifukwa cha luso lake posamalira banja lake.

Nawonso akazi achikhristu a m’nthawi ya atumwi analimbikitsidwa kuti akhale “ogwira ntchito zapakhomo.” (Tito 2:5) Koma analinso ndi mwayi ndiponso udindo wophunzitsa ena za chikhulupiriro chawo chachikhristu. (Mateyo 28:19, 20; Machitidwe  2:18) Kodi zina mwa “ntchito zochuluka” zimene akazi achiyuda a m’nthawi ya atumwi ankagwira zinali zotani? Ndipo kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimene Yesu ananena zokhudza Mariya?

‘Kutanganidwa ndi Ntchito Zochuluka’ Mkazi wachiyuda wokwatiwa ankadzuka m’mamawa kwambiri, mwina dzuwa lisanatuluke. (Miyambo 31:15) Akatha kuphikira banja lake phala, ankaperekeza ana ake aamuna kusukulu ya kusunagoge. Ana aakazi ankatsala pakhomo kuti aphunzire ntchito zowathandiza kuti adzakhale akazi abwino akadzakwatiwa.

Mayi ndi ana ake aakazi ankayamba kugwira ntchito zapakhomo zofunika monga: kuthira mafuta mu nyale (1), kusesa (2) ndiponso kukama mkaka wa mbuzi zapabanjalo (3). Kenako, ankaphika mikate yoti adye patsikulo. Choyamba, atsikana ankapeta tirigu kuti achotse zitsotso (4) ndipo ankapera tiriguyo pogwiritsa ntchito mphero (5). Mayi ankasakaniza ufawo ndi madzi komanso zofufumitsira. Ankasakaniza bwinobwino zinthuzo (6) ndipo kenako ankazisiya kuti zifufume uku akugwira ntchito zina. Panthawi imeneyi, atsikana ankasefa mkaka wa mbuzi uja kuti utsale mkaka woundana wokha basi (7).

Dzuwa litakwera pang’ono, mayi ndi ana ake aakaziwo ankapita kumsika wa m’deralo. Kumeneko, iwo ankasangalala ndi fungo labwino la zokometsera zakudya, kulira kwa nyama zosiyanasiyana ndiponso phokoso la anthu akunenerera katundu amene akufuna kugula. Kumsikaku amayiwo ankagula chakudya cha tsikulo (8). Ankatha kugula ndiwo zamasamba ndiponso nsomba zouma. Akakhala mkazi wachikhristu, ankatha kugwiritsanso ntchito mpata umenewu kuuza ena za chikhulupiriro chake.​—Machitidwe 17:17.

Mayi wanzeru ankagwiritsa ntchito nthawi imene anali kuyenda popita kumsikaku kuthandiza ana ake kuti adziwe ndi kukonda mfundo za m’Malemba. (Deuteronomo 6:6, 7) Mwina ankakambirananso mfundo zimene zingathandize ana akewo kuti azidzasamala ndalama pogula zinthu.​—Miyambo 31:14, 18.

Ntchito ina imene akazi ankachita tsiku lililonse inali kupita kuchitsime (9). Kumeneko ankatunga madzi ogwiritsa ntchito pabanja pawo, ndipo mwina kuchitsimeko ankachezanso ndi azimayi ena. Akabwerera kunyumba, mayi ndi ana akewo ankayamba kuphika mikate. Choyamba, ankaumba timbamu ta ufa anakanda uja kuti tikhale ngati zitumbuwa, ndipo kenako ankaziika mu uvuni yomwe imakhala yotentha kale (10). Nthawi zambiri uvuniyi inkamangidwa panja pa nyumba. Iwo ankasangalala ndi fungo labwino la mikateyo ikamapsa ndiponso ndi nkhani zosiyanasiyana zimene ankakambirana.

Akatha zimenezi, ankapita kukachapa zovala (11) kumtsinje wapafupi. Choyamba, azimayiwo ankachapa zovalazi ndi sopo wopangidwa ndi chidulo cha zomera. Akatsukuluza ndi kufinya zovalazo, ankaziyanika pazomera ndiponso pamiyala.

 Akabweretsa zovalazo kunyumba, mayi ndi ana akewo ankatha kupita pamwamba pa nyumba yawo kuti akasoke (12) zovala zomwe zang’ambika. Kenako ankazisunga m’malo mwake. Akatha zimenezi, atsikanawo ankaphunzitsidwanso kupeta nsalu ndi kuluka zinthu (13). Akamaliza zimenezi, inkakhala nthawi yoti ayambe kuphika chakudya chamadzulo (14). Ayuda anali odziwa kuchereza alendo moti banja lililonse linkakhala lokonzeka kudya ndi alendo chakudya chawo. Nthawi zambiri chakudya chake chinkakhala mikate, ndiwo zamasamba, chambiko, nsomba zouma ndipo ankamwera madzi ozizira.

Madzulo a tsiku lililonse, ana akamafuna kukagona ankawapaka mafuta ngati anavulala posewera. Kenako, makolowo ankayatsa nyale n’kuyamba kufotokozera anawo nkhani ya m’Malemba. Pomaliza ankapemphera limodzi ndi anawo. Ana akapita kukagona, m’nyumbamo munkakhala zii ndipo mwamuna ankakhala ndi chifukwa chomveka chouzira mkazi wake mawu otchuka akuti: “Mkazi wangwiro ndani angam’peze? Pakuti mtengo wake uposa ngale.”​—Miyambo 31:10.

Kusankha “Chinthu Chabwino Kwambiri” N’zoonekeratu kuti akazi anzeru a m’nthawi ya atumwi ankakhala otanganidwa ndi “ntchito zochuluka.” (Luka 10:40-42) N’chimodzimodzinso akazi a masiku ano, makamaka amene ali ndi ana. Ndi zoona kuti zipangizo zamakono zafewetsako ntchito zina zapakhomo. Komabe, chifukwa cha mavuto osiyanasiyana, amayi ambiri amakakamizikanso kukhala pa ntchito n’cholinga choti azipeza ndalama.

Ngakhale kuti amakumana ndi mavuto ambiri, akazi achikhristu ochuluka masiku ano, amatsanzira chitsanzo cha Mariya amene watchulidwa kumayambiriro uja. Akazi amenewa amaona kuti zinthu zauzimu ndi zofunika kwambiri. (Mateyo 5:3) Iwo amasamalira kwambiri mabanja awo chifukwa Malemba amawalimbikitsa kutero. (Miyambo 31:11-31) Komabe, amatsatira mfundo imene Yesu anamuuza Marita. Poti Marita ankaona kuti ubwenzi wake ndi Mulungu ndi wofunika kwambiri, iye ayenera kuti anatsatira malangizo amenewa. Akazi achikhristu samalola kuti ntchito zawo zapakhomo ziwalepheretse kuphunzira za Mulungu (15) kapena kuuza ena zimene amakhulupirira. (Mateyo 24:14; Aheberi 10:24, 25) Pochita zimenezi, iwo amakhala akusankha “chinthu chabwino kwambiri.” (Luka 10:42) Chifukwa cha zimenezi, iwo amakondedwa kwambiri ndi Mulungu, Khristu, ndiponso ndi anthu a m’banja mwawo.​—Miyambo 18:22.