Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Amamva Chisoni

Mulungu Amamva Chisoni

 Yandikirani Mulungu

Mulungu Amamva Chisoni

OWERUZA 2:11-18

IFE anthu opanda ungwiro, nthawi zina timadzimvera chisoni chifukwa cholakwitsa chinachake. Baibulo limanena kuti nayenso Yehova amamva chisoni. Koma mwina munganene kuti, “Mulungu ndi wangwiro ndipo samalakwitsa chilichonse, ndiyeno kodi amamva chisoni m’njira yotani?” Yankho la funso limeneli litithandiza kumvetsa mfundo ina yochititsa chidwi yakuti: Yehova amakhudzidwa ndi zochita zathu, moti amasangalala kapena kukhumudwa nazo. Tiyeni tikambirane mawu amene ali pa Oweruza 2:11-18.

Buku la Oweruza limafotokoza zochitika za m’nthawi imene mtundu wa Isiraeli unakumana ndi mavuto ambiri. Panthawiyi mtunduwu unkakhala ku Kanani, dziko limene Mulungu analonjeza Abulahamu. Zinthu zimene zinkachitika m’zaka zoposa 300 kuchokera pamene Aisiraeli anangofika m’dzikoli tingazifotokoze mwachidule kuti ankachita ndiponso kukumana ndi zinthu zinayi izi mobwerezabwereza: Kusiya Mulungu, kuponderezedwa, kuchonderera Mulungu, ndiponso kupulumutsidwa. *

Kusiya Mulungu. Potengera anthu a ku Kanani, Aisiraeli “anasiya Yehova” ndipo anayamba kutsatira milungu ina. Iwo ‘ankatumikira Baala ndi zifaniziro za Asitaroti.’ * Zimene anachitazi zinasonyeza kuti anapandukira Mulungu. Choncho n’zosadabwitsa kuti Aisiraeli ‘anautsa mkwiyo wa Yehova,’ Mulungu amene anawapulumutsa ku Iguputo.​—Vesi 11-13; Oweruza 2:1.

Kuponderezedwa. Aisiraeli akasiya Yehova, iye ankawakwiyira ndipo ankasiya kuwateteza. Choncho iye ankawapereka “m’dzanja la adani awo” omwe ankawalanda katundu.​—Vesi 14.

Kuchonderera Mulungu. Aisiraeli akakumana ndi mavuto adzaoneni, ankadzimvera chisoni chifukwa cha zochita zawo zoipa ndipo ankafuulira Mulungu kuti awathandize. Mawu akuti “kubuula kwawo chifukwa cha iwo akuwapsinja,” akusonyeza kuti iwo ankachonderera Mulungu. (Vesi 18) Mobwerezabwereza, Aisiraeli ankachonderera Mulungu akakumana ndi mavuto. (Oweruza 3:9, 15; 4:3; 6:6, 7; 10:10) Kodi Mulungu ankachita chiyani iwo akamuchonderera?

Kupulumutsidwa. Yehova ankamva kubuula kwa Aisiraeli ndipo ‘ankagwidwa chisoni.’ Mawu achiheberi amene amasuliridwa kuti ‘kugwidwa chisoni’ amatanthauzanso kuti “kusintha maganizo kapena cholinga.” Buku lina linanena kuti: “Yehova akakhudzidwa mtima chifukwa cha kubuula kwawo, ankasintha cholinga chake chowalanga ndipo ankawapulumutsa.” Chifukwa cha chifundo chake, Yehova ‘ankawaukitsira oweruza’ amene ankawapulumutsa kwa adani awo.​—Vesi 18.

Kodi mwaona chimene chinkachititsa Mulungu kumva chisoni, kapena kuti kusintha maganizo ake? Chinali chifukwa chakuti anthu ake ankakhala atasintha maganizo n’kusiya kuchita zoipa. Zimenezi tingaziyerekezere motere: Bambo wachikondi angathe kulanga mwana wake akalakwa, mwina pomuletsa kuchita zinthu zina. Koma akaona kuti mwanayo wapepesa mochokera pansi pa mtima, bamboyo sapitiriza kumulanga.

Kodi nkhani imeneyi ikutiphunzitsa kuti Yehova ndi wotani? Kuchimwa mwadala kumamukwiyitsa, koma kulapa mochokera pansi pa mtima kumamuchititsa kusonyeza chifundo. N’zochititsa chidwi kudziwa kuti zimene timachita zingathe kukhumudwitsa kapena kusangalatsa Mulungu. Motero yesetsani kuphunzira zimene mungachite kuti ‘muzikondweretsa mtima’ wa Yehova. (Miyambo 27:11) Mukamachita zimenezi simudzanong’oneza bondo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Zimene zili pa Oweruza 2:11-18 ndi mbali ya mawu oyamba achidule amene amafotokoza zimene Aisiraeli ankakonda kuchita. Zimenezi zafotokozedwa mwatsatanetsatane m’machaputala ena a bukuli.

^ ndime 3 Anthu a ku Kanani ankaona kuti Baala ndiye anali mulungu wamkulu kwambiri, ndipo Asitaroti anali mulungu wamkazi amene anthuwa ankakhulupirira kuti anali mkazi wa Baala.