Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufufuza Zoona Zenizeni za Kumwamba

Kufufuza Zoona Zenizeni za Kumwamba

 Kufufuza Zoona Zenizeni za Kumwamba

MFUNDO yakuti anthu adzapita kumwamba ingamveke yosangalatsa kwambiri. Asilamu, Ahindu, Abuda, anthu ambiri a m’matchalitchi achikhristu, ndiponso amene sali m’chipembedzo chilichonse amakhulupirira zosiyanasiyana pa nkhani yakuti pali moyo wina umene munthu angakhale nawo akafa. Anthu ambiri amaganiza kuti kumwamba ndi malo okongola ndiponso osangalatsa kumene anthu samavutika ndipo amakakumananso ndi “okondedwa awo amene anamwalira.” Koma zimene anthu ambiri amachita zimasonyeza kuti mawu akale awa ndi oona, akuti: Aliyense amafuna kupita kumwamba, koma palibe amene amafuna kufa kuti apite kumwambako. N’chifukwa chiyani zili choncho?

Ngati tinalengedwa kuti tizifa ndi kupita kumwamba, kodi si bwenzi anthu ambiri akulakalaka kufa ngati mmene ana amafunira kukula ndiponso mmene achinyamata amakhumbira kulowa m’banja? Komatu anthu ambiri samafuna kufa.

Ngakhale zili choncho, alaliki ambiri amanena kuti tinalengedwa kuti tidzapite kumwamba moyo wathu wakanthawi padziko pano ukatha. Mwachitsanzo, Theodore Edgar Cardinal McCarrick, yemwe anali bishopu wamkulu wa ku Washington, D.C., ananena kuti: “Kwathu si padziko pano ayi. Kwathu ndi kumwamba, n’kumene tinalengedwa kuti tikakhale.” Nayenso mtsogoleri wakale wa bungwe la matchalitchi la U.S. National Association of Evangelicals, ananena kuti: “Cholinga cha moyo ndicho kupereka ulemelero kwa Mulungu kenako n’kupita kumwamba . . . chifukwa kwathu ndi kumwamba.”

Nthawi zambiri anthu amene amakhulupirira kuti munthu akafa amakakhala ndi moyo kumwamba, amangokhulupirira zimenezi popanda zifukwa zokwanira. George Barna ndi mtsogoleri wa kampani imene imachita kafukufuku wa zikhulupiriro za zipembedzo zosiyanasiyana. Iye anapeza kuti anthu ambiri amayamba kukhala ndi “maganizo okhudza moyo uno ndiponso moyo umene munthu angakhale pambuyo pa imfa potengera maganizo amene amapezeka mu zinthu monga mafilimu, nyimbo ndiponso mabuku a nthano.” M’busa wina wa ku Florida, ku America, wa tchalitchi cha Episikopo, ananena kuti: “Sitikudziwa chilichonse chokhudza kumwamba. Chomwe tikungodziwa n’chakuti kumwamba n’kumene kuli Mulungu.”

Komabe nkhani yonena za kumwamba ndi nkhani yofunika kwambiri m’Baibulo. Kodi Mawu a Mulungu amati kumwamba n’kotani? Kodi anthu analengedwa kuti azikakhala kumwamba? Ngati anthu amapita kumwamba, kodi amakachitako chiyani?

[Mawu Otsindika patsamba 3]

N’chifukwa chiyani anthu ambiri amafuna kupita kumwamba, koma palibe amene amafuna kufa kuti apite kumwambako?